NYIMBO 79
Athandizeni Kukhala Olimba
Losindikizidwa
1. Kuphunzitsa nkhosa za M’lungu
Ndi mwayi wapadera.
Yehova wawatsogolera
Kukonda choonadi.
(KOLASI)
Yehova tikupemphatu
Kuti muziwateteza.
Mwa Yesu tikupemphera, athandizenibe
Akhale olimba.
2. Mayesero akawagwera
Tinkawapempherera.
Tinkawaphunzitsa mwakhama,
Pano adalitsidwa.
(KOLASI)
Yehova tikupemphatu
Kuti muziwateteza.
Mwa Yesu tikupemphera, athandizenibe
Akhale olimba.
3. Akhale okudalirani
Inu M’lungu ndi Yesu.
Apirire pamayesero.
Akalandire moyo.
(KOLASI)
Yehova tikupemphatu
Kuti muziwateteza.
Mwa Yesu tikupemphera, athandizenibe
Akhale olimba.
(Onaninso Luka 6:48; Mac. 5:42; Afil. 4:1.)