NYIMBO 106
Tikulitse Khalidwe la Chikondi
Losindikizidwa
1. Chonde Mulungu mutipatse
Makhalidwe anu onsewo.
Koma lofunika kwambiri
N’chikondi chomwe muli nacho.
Ngati tilibe chikondichi
Maluso athu ndi achabe.
Tizisonyezana chikondi
M’zochita ndi muzolankhula.
2. Chikondi ndi chokoma mtima
Sichimafuna zake zokha.
Sichimasunganso zifukwa,
Chimakhululukira ena.
Mavuto angakule bwanji
Chikondi chimapirirabe.
Chikondi sichimagonjanso.
Chidzakhalapo mpaka kale.
(Onaninso Yoh. 21:17; 1 Akor. 13:13; Agal. 6:2.)