Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yehova Waulula “Zimene Ziyenera Kuchitika Posachedwapa”
    Nsanja ya Olonda—2012 | June 15
    • Yehova Waulula “Zimene Ziyenera Kuchitika Posachedwapa”

      “Chivumbulutso choperekedwa ndi Yesu Khristu, chimene Mulungu anamupatsa, kuti aonetse akapolo ake zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwapa.”​—CHIV. 1:1.

      KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

      Kodi ndi mbali iti ya chifaniziro chachikulu imene ikuimira ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America?

      Kodi Yohane anafotokoza bwanji mgwirizano wa pakati pa ulamuliro wa Britain ndi America ndi bungwe la United Nations?

      Kodi Danieli ndi Yohane anafotokoza kuti ulamuliro wa anthu udzatha bwanji?

      1, 2. (a) Kodi maulosi a Danieli ndi Yohane amatithandiza bwanji? (b) Kodi mitu 6 yoyambirira ya chilombo imaimira chiyani?

      MAULOSI a Danieli ndiponso a Yohane amagwirizana ndipo amatithandiza kudziwa tanthauzo la zinthu zimene zikuchitika panopa ndiponso zimene zidzachitike m’tsogolo. Kodi tikuphunzira chiyani pa masomphenya a Yohane onena za chilombo, zimene Danieli anafotokoza zokhudza chilombo choopsa cha nyanga 10 komanso zimene Danieli ananena zokhudza chifaniziro chachikulu? Kodi kumvetsa bwino maulosi amenewa kuyenera kutilimbikitsa kuchita chiyani?

      2 Tiyeni tikambirane masomphenya a Yohane onena za chilombo. (Chiv. 13:1-18) Monga tinaonera m’nkhani yoyamba ija, mitu 6 yoyamba ikuimira ufumu wa Iguputo, Asuri, Babulo, Mediya ndi Perisiya, Girisi ndiponso Roma. Maufumu onsewa anadana ndi mbewu ya mkazi. (Gen. 3:15) Ufumu wa Roma, womwe ndi mutu wa 6, unakhalabe wamphamvu kwa zaka mahandiredi ambiri kuchokera pamene Yohane analemba masomphenya ake. Ndiyeno patapita nthawi, mutu wa 7 unayenera kulowa m’malo mwa Roma. Kodi ndi ulamuliro uti wamphamvu padziko lonse umene unalowa m’malo? Nanga unachitira zotani mbewu ya mkazi?

      MAYIKO A BRITAIN NDI UNITED STATES ANAKHALA AMPHAMVU

      3. Kodi chilombo choopsa cha nyanga 10 chikuimira chiyani ndipo nyanga 10 zikuimira chiyani?

      3 Kodi tingadziwe bwanji ufumu umene mutu wa 7 wa chilombo cha m’chaputala 13 cha buku la Chivumbulutso ukuimira? Tiyenera kuyerekezera masomphenya a Yohane ndi a Danieli okhudza chilombo choopsa cha nyanga 10.a (Werengani Danieli 7:7, 8, 23, 24.) Chilombo chimene Danieli anaona chinaimira ufumu wamphamvu padziko lonse wa Roma. (Onani tchati patsamba 12 ndi 13.) Ufumu wa Roma unayamba kugawikana m’zaka za m’ma 400 C.E. Nyanga 10 zimene zinamera pamutu wa chilombo choopsachi zikuimira maufumu amene anachokera mu ufumu wa Roma womwewu.

      4, 5. (a) Kodi nyanga yaing’ono inachita zotani? (b) Kodi mutu wa 7 wa chilombo ukuimira ufumu uti?

      4 Koma nyanga zinayi zokha za chilombo choopsachi ndi zimene zimatchulidwa mwapadera. Pa nyanga zinayizi, imodzi “yaing’ono” inazula zitatu zinazo. Zimenezi zinakwaniritsidwa pamene dziko la Britain, lomwe linali m’dera lolamulidwa ndi ufumu wa Roma, linakhala lamphamvu kwambiri. Koma pamene zinkafika zaka za m’ma 1600, zimenezi zinali zisanachitike. Mayiko ena atatu amene anachokera mu ufumu wa Roma, omwe anali Spain, Netherlands ndi France ndi amene anali amphamvu. Ndiyeno ufumu wa Britain unazula maufumu enawo m’njira yoti unayamba kukhala wamphamvu kwambiri kuposa maufumuwo. Pakati pa zaka za m’ma 1700, ufumu wa Britain unali utayamba kukula mphamvu. Koma pa nthawiyi, unali usanakhale mutu wa 7 wa chilombo.

      5 Ngakhale kuti ufumu wa Britain unali utayamba kukhala wamphamvu, madera a ku North America anachoka mu ulamuliro wake. Komabe, ufumu wa Britain unateteza maderawo ndi asilikali ake apanyanja. Maderawo ndi amene anapanga dziko la United States ndipo dzikolo linakhala lamphamvu kwambiri. Pamene tsiku la Ambuye linkayamba mu 1914, dziko la Britain linali kulamulira dera lalikulu kwambiri kuposa ufumu uliwonse m’mbuyomo. Ndipo dziko la United States linali lamphamvu padziko lonse pa nkhani zamalonda.b Ndiyeno pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse, dziko la United States linapanga mgwirizano wapadera ndi dziko la Britain. Izi zinachititsa kuti Britain ndi America apange ufumu wamphamvu padziko lonse womwe unaimiridwa ndi mutu wa 7 wa chilombo. Kodi ufumu umenewu unachita zotani ndi mbewu ya mkazi?

      6. Kodi mutu wa 7 wa chilombo wachitira zotani anthu a Mulungu?

      6 Tsiku la Ambuye litangoyamba, mutu wa 7 wa chilombo unaukira anthu a Mulungu kapena kuti otsalira a abale a Khristu padziko lapansi. (Mat. 25:40) Yesu anasonyeza kuti pa nthawi ya kukhalapo kwake, otsalira a mbewu adzakhala akugwira ntchito padziko lapansi. (Mat. 24:45-47; Agal. 3:26-29) Ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America unachita nkhondo ndi oyerawo. (Chiv. 13:3, 7) Pa nthawi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse, ulamulirowu unapondereza anthu a Mulungu, kuotcha mabuku awo ndiponso kuika m’ndende anthu oimira gulu la kapolo wokhulupirika. Zimene mutu wa 7 wa chilombochi unachita zinali ngati kupha ntchito yolalikira kwakanthawi. Yehova anali ataoneratu zochitikazi ndipo anaziulula kwa Yohane. Yehova anauzanso Yohane kuti mbali yachiwiri ya mbewu idzakhalanso ndi mphamvu n’kuyamba kutumikira Mulungu mwakhama. (Chiv. 11:3, 7-11) Mbiri ya atumiki a Yehova a masiku ano ikusonyeza kuti zimenezi zinachitikadi.

      ULAMULIRO WA BRITAIN NDI AMERICA KOMANSO MAPAZI ACHITSULO NDI DONGO

      7. Kodi mutu wa 7 wa chilombo ukugwirizana bwanji ndi chifaniziro chachikulu?

      7 Mapazi a chifaniziro chachikulu akuimira ufumu umene ukuimiridwanso ndi mutu wa 7 wa chilombo. Ufumu umenewu ndi ufumu wa Britain ndi America. Ufumu wa Britain unachokera mu ufumu wa Roma. Popeza dziko la United States linachokera mu ufumu wa Britain, tinganenenso kuti unachokera mu ufumu wa Roma. Choncho mapaziwo apangidwa ndi chitsulo koma chitsulocho n’chosakanizidwa ndi dongo. (Werengani Danieli 2:41-43.) Mmene mapaziwa alili zikugwirizana ndi nthawi imene mutu wa 7, womwe ndi ulamuliro wa Britain ndi America, unakhala wamphamvu padziko lonse. Chitsulo n’cholimba koma chikasakanizidwa ndi dongo, sichilimba. Mofanana ndi zimenezi, ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America ndi wofooka tikayerekezera ndi kumene unachokera, ku ulamuliro wa Roma. N’chifukwa chiyani tikutero?

      8, 9. (a) Kodi ulamuliro wa padziko lonse wa 7 unasonyeza bwanji kuti ndi wolimba ngati chitsulo? (b) Kodi dongo la kumapazi a chifaniziro likuimira chiyani?

      8 Nthawi zina, mutu wa 7 wa chilombo unkachita zinthu mwamphamvu ngati chitsulo. Mwachitsanzo, unapambana pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse. Pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, mutu wa 7 unasonyezanso kuti ndi wolimba ngati chitsulo.c Nkhondoyi itatha, nthawi zina mutu wa 7 unali kusonyezabe kuti ndi wolimba ngati chitsulo. Komabe, chitsulochi n’chosakanizidwa ndi dongo.

      9 Kwa nthawi yaitali, atumiki a Yehova akhala akuyesetsa kumvetsa tanthauzo la mapazi a chifaniziro chimenechi. Lemba la Danieli 2:41 limafotokoza msanganizo wa chitsulo ndi dongo monga “ufumu,” osati maufumu. Choncho dongolo likuimira zinthu zimene anthu ena amene ali pansi pa ulamuliro wa Britain ndi America akuchita. Zochita za anthuwa zimachititsa kuti ulamulirowu ukhale wosalimba poyerekezera ndi ulamuliro wa Roma, womwe unali ngati chitsulo. Dongolo likufotokozedwa ngati “ana a anthu,” kapena kuti anthu wamba. (Dan. 2:43) Anthu amene ali pansi pa ulamulirowu apanga magulu omenyera ufulu wosiyanasiyana. Anthu wamba amenewa achepetsa mphamvu za ulamuliro wa Britain ndi America kuti usakhale ngati chitsulo. Anthu ambiri amasiyana maganizo pa nkhani zokhudza boma ndipo olamulira ena amawina chisankho ndi mavoti ochepa. Zimenezi zimachititsa kuti olamulirawo asakhale ndi mphamvu zokwanira zochita zimene akufuna. Danieli anati: “Pa zinthu zina ufumuwo udzakhala wolimba koma pa zinthu zina udzakhala wosalimba.”​—Dan. 2:42; 2 Tim. 3:1-3.

      10, 11. (a) Kodi n’chiyani chidzachitikire “mapazi”? (b) Kodi tinganene chiyani pa nkhani ya chiwerengero cha zala za chifanizirochi?

      10 M’nthawi yathu ino, mayiko a Britain ndi United States akugwirizanabe kwambiri ndipo nthawi zambiri amachitira zinthu limodzi. Maulosi okhudza chifaniziro chachikulu ndiponso chilombo amatsimikizira kuti sipakhalanso ulamuliro wina wamphamvu padziko lonse umene udzalowa m’malo ulamuliro wa Britain ndi America. Ulamuliro wamphamvu padziko lonse womalizirawu ndi wosalimba tikauyerekezera ndi ufumu umene ukuimiridwa ndi miyendo yachitsulo. Koma sikuti udzangotha wokha.

      11 Kodi chiwerengero cha zala zakumiyendo za chifanizirochi chili ndi tanthauzo lapadera? Taganizirani izi. M’masomphenya ena, Danieli anatchula ziwerengero za zinthu. Mwachitsanzo, anatchula chiwerengero cha nyanga pamitu ya zilombo zosiyanasiyana. Ziwerengero zimenezi zinali ndi tanthauzo lapadera. Koma pofotokoza chifanizirochi, Danieli sanatchule chiwerengero cha zala zake. Choncho zikuoneka kuti chiwerengero chake chilibe tanthauzo lapadera ngati mmene zilili ndi chiwerengero cha manja, miyendo ndi mapazi ake. Koma zimene Danieli anatchula n’zoti zalazo zidzakhala zachitsulo ndi dongo. Zimene Danieli anafotokoza zikutithandiza kuzindikira kuti ulamuliro wa Britain ndi America ndi umene udzakhale wamphamvu padziko lonse pamene “mwala” woimira Ufumu wa Mulungu udzaphwanya mapazi a chifanizirochi.​—Dan. 2:45.

      ULAMULIRO WA BRITAIN NDI AMERICA UKUIMIRIDWANSO NDI CHILOMBO CHA NYANGA ZIWIRI

      12, 13. Kodi chilombo cha nyanga ziwiri chikuimira chiyani ndipo chinachita zotani?

      12 Ngakhale kuti ulamuliro wa Britain ndi America uli ngati chitsulo chosakanizidwa ndi dongo, masomphenya amene Yesu anaonetsa Yohane amasonyeza kuti ulamulirowu udzakhalabe wamphamvu m’masiku otsiriza. N’chifukwa chiyani tikutero? Yohane anaona masomphenya a chilombo cha nyanga ziwiri cholankhula ngati chinjoka. Kodi chilombo chodabwitsachi chikuimira chiyani? Popeza kuti chili ndi nyanga ziwiri, chikuimira ulamuliro wopangidwa ndi mayiko awiri. Apa Yohane anaona ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America koma ukuchita zinthu zina zapadera.​—Werengani Chivumbulutso 13:11-15.

      13 Chilombo chimenechi chinalimbikitsa anthu kupanga chifaniziro cha chilombo chotchulidwa pa Chivumbulutso 13:1. Yohane analemba kuti chifaniziro cha chilombochi chidzaonekera n’kuzimiririka ndipo kenako chidzaonekeranso. Zimenezi ndi zimene zinachitikadi ndi bungwe limene mayiko a Britain ndi United States analimbikitsa kuti likhazikitsidwe. Bungweli linapangidwa ndi cholinga choti ligwirizanitse ndiponso kuimira maufumu a padziko lapansi.d Bungweli linaonekera nkhondo yoyamba ya padziko lonse itatha ndipo linkatchedwa League of Nations. Koma linazimiririka pamene nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inkayamba. Pa nthawi ya nkhondo yachiwiri imeneyi, anthu a Mulungu analengeza kuti malinga ndi ulosi wa m’buku la Chivumbulutso, chifaniziro cha chilombochi chidzaonekeranso. Chifanizirochi chinaonekeradi monga bungwe la United Nations.​—Chiv. 17:8.

      14. N’chifukwa chiyani chifaniziro cha chilombo chikutchedwa “mfumu ya 8”?

      14 Yohane anafotokoza chifaniziro cha chilombo monga “mfumu ya 8.” Koma chifanizirochi sichisonyezedwa ngati mutu wa 8 pa chilombo choyamba chija chifukwa chakuti ndi chifaniziro chabe. Mphamvu zake zimachokera kwa mamembala ake, makamaka Britain ndi America, omwe ndi mamembala ake akuluakulu. (Chiv. 17:10, 11) Nanga n’chifukwa chiyani chikutchedwa “mfumu ya 8”? Chifukwa chakuti chifanizirochi chidzapatsidwa mphamvu zochita zinthu ngati mfumu. Zimene chidzachitezo zidzasinthiratu zinthu padzikoli.

      CHIFANIZIRO CHA CHILOMBO CHIDZAWONONGA HULE

      15, 16. Kodi hule likuimira chiyani ndipo chikuchitika n’chiyani ndi anthu ake?

      15 Yohane ananena kuti pamsana pa chilombo chofiira kwambiri, chomwe ndi chifaniziro cha chilombo, panali hule lophiphiritsa limene linkachilamulira. Dzina la hulelo ndi “Babulo Wamkulu.” (Chiv. 17:1-6) Hulelo likuimira zipembedzo zonse zonyenga ndipo mbali yaikulu ya zipembedzozi ndi matchalitchi amene amati ndi achikhristu. Zipembedzo zimagwirizana ndi chifaniziro cha chilombochi ndipo zimayesetsa kuchilamulira.

      16 Koma m’tsiku la Ambuye, Babulo Wamkulu waona kuti madzi ake auma kwambiri, kapena kuti anthu ake ambiri amusiya. (Chiv. 16:12; 17:15) Mwachitsanzo, pamene chifaniziro cha chilombo chinkayamba kuonekera, matchalitchi amene amati ndi achikhristu anali amphamvu kwambiri kumayiko akumadzulo ngati ku Ulaya ndi ku America. Matchalitchi amenewa ndi mbali yaikulu ya Babulo Wamkulu. Masiku ano, anthu asiya kulemekeza kapena kuikira kumbuyo matchalitchiwo komanso atsogoleri awo. Anthu ambiri akukhulupirira kuti zipembedzo zimalimbikitsa kapena kuyambitsa mikangano. Ndipo anthu ena ophunzira ayamba kunena kuti m’pofunika kuthetsa zipembedzo.

      17. Kodi n’chiyani chidzachitikire zipembedzo zonyenga posachedwapa, ndipo n’chifukwa chiyani?

      17 Koma zipembedzo zonyenga sizidzangotha pazokha. Hulelo lidzapitiriza kukhala lamphamvu ndiponso kuyesetsa kulamulira mafumu mpaka pamene Mulungu adzaika maganizo enaake m’mitima ya mafumuwo. (Werengani Chivumbulutso 17:16, 17.) Posachedwapa, Yehova adzachititsa magulu andale a dziko la Satanali, amene akuimiridwa ndi bungwe la United Nations, kuti aukire zipembedzo zonyenga. Iwo adzathetsa mphamvu zake ndiponso kusakaza chuma chake. Zaka zochepa zapitazo, anthu sakanakhulupirira kuti zimenezi zingachitike. Koma masiku ano, huleli lili pendapenda pamsana wa chilombo chofiira kwambiri. Ngakhale zili choncho, silidzagwa pang’onopang’ono koma lidzagwetsedwa mwadzidzidzi ndiponso mwamphamvu.​—Chiv. 18:7, 8, 15-19.

      MAPETO A ZILOMBO

      18. (a) Kodi chilombo chidzachita chiyani, ndipo zotsatira zake zidzakhala zotani? (b) Kodi lemba la Danieli 2:44 limasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu udzawononga mafumu ati? (Onani bokosi patsamba 17.)

      18 Zipembedzo zonyenga zitawonongedwa, chilombocho, chomwe ndi mabungwe andale m’dziko la Satanali, chidzalimbikitsidwa kuukira Ufumu wa Mulungu. Popeza sangathe kufika kumwamba, mafumu a dziko adzaukira anthu a padziko lapansi amene ali ku mbali ya Ufumu wa Mulungu. Koma zotsatira zake n’zodziwikiratu. (Chiv. 16:13-16; 17:12-14) Danieli anafotokoza chinthu china chimene chidzachitike pa nkhondo yomaliza. (Werengani Danieli 2:44.) Chilombo chotchulidwa pa Chivumbulutso 13:1, chifaniziro chake ndiponso chilombo cha nyanga ziwiri zidzawonongedwa.

      19. Kodi sitiyenera kukayikira za chiyani, ndipo ino ndi nthawi yochita chiyani?

      19 Panopo tikukhala m’masiku a mutu wa 7. Palibenso mutu wina umene udzaonekere chilombo chisanawonongedwe. Ulamuliro wa Britain ndi America ndi umene udzakhala wamphamvu padziko lonse pamene zipembedzo zonyenga zizidzawonongedwa. Maulosi a Danieli ndi Yohane akwaniritsidwa ndendende. Choncho sitikukayikira kuti posachedwapa zipembedzo zonyenga zidzawonongedwa ndipo nkhondo ya Aramagedo ifika. Mulungu waulula zinthu zimenezi pasadakhale. Kodi tidzatsatira machenjezo opezeka m’maulosi? (2 Pet. 1:19) Inoyi ndi nthawi yoti tikhale ku mbali ya Yehova ndi Ufumu wake.​—Chiv. 14:6, 7.

  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2012 | June 15
    • Mafunso Ochokera kwa Owerenga

      Kodi ndi liti pamene ulamuliro wa Britain ndi America unakhala ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa 7 wotchulidwa mu ulosi wa m’Baibulo?

      ▪ Chifaniziro chachikulu chimene Mfumu Nebukadinezara inalota sichiimira maulamuliro onse amphamvu apadzikoli. (Dan. 2:31-45) Chimangoimira maulamuliro asanu amene analamulira kuyambira nthawi ya Danieli, omwe analowerera kwambiri pa zochita za anthu a Mulungu.

      Zimene Danieli anafotokoza pomasulira chifanizirocho zinasonyeza kuti ulamuliro wa Britain ndi America udzachokera mu ulamuliro wa Roma osati kuugonjetsa. Danieli anaona kuti miyendo ya chifanizirochi inali yachitsulo ndipo chitsulocho chinafika mpaka kumapazi ndi kuzala zakumapazi. (Koma chitsulo cha kumapazi ndi zala chinasakanizidwa ndi dongo.)a Zimenezi zinasonyeza kuti ulamuliro wa Britain ndi America udzachokera m’miyendo yachitsulo. Mbiri yakale ikusonyeza kuti izi n’zimene zinachitikadi. Dziko la Britain linali mu ulamuliro wa Roma ndipo linayamba kukhala lamphamvu chakumapeto kwa zaka za m’ma 1700. Kenako dziko la United States nalonso linakhala lamphamvu. Koma pa nthawiyi, ulamuliro wamphamvu padziko wa 7 wotchulidwa mu ulosi wa m’Baibulo unali usanayambe. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa pa nthawiyi mayiko a Britain ndi United States anali asanachitire limodzi zinthu zikuluzikulu. Koma anachitira limodzi zinthu pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse.

      Pa nthawi imeneyo, “ana a ufumu” ankagwira ntchito yawo makamaka m’dziko la United States. Likulu lawo linali m’dzikoli, ku Brooklyn ku New York. (Mat. 13:36-43) Koma Akhristu odzozedwa ankalalikiranso m’mayiko amene ankalamulidwa ndi ufumu wa Britain. Pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse, dziko la Britain linachita mgwirizano wapadera ndi dziko la United States pomenyana ndi adani awo. Chifukwa cha nkhondoyo, kunali mzimu wokonda kwambiri dziko ku Britain ndi ku United States. Zimenezi zinachititsa kuti mayikowa ayambe kudana ndi anthu omwe anali mbali ya mbewu ya “mkazi” wa Mulungu. Analetsa mabuku awo ndipo anamanga anthu amene ankatsogolera pa ntchito yolalikira.​—Chiv. 12:17.

      Malinga ndi zimene ulosi wa m’Baibulo umanena, ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa 7 unali usanakhazikitsidwe pamene dziko la Britain linayamba kukhala lamphamvu chakumapeto kwa zaka za m’ma 1700. M’malomwake, unakhazikitsidwa chakumayambiriro kwa tsiku la Ambuye.b

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena