NYIMBO 84
Tizitumikira Modzipereka
Losindikizidwa
1. M’lungu wathu watipatsa
Zomwe timafunikira
Kuti tizisangalala
Pomwe tikulalikira.
(KOLASI)
Tigwire ntchitoyi
Modzipereka
Ndipo kulikonse tipita
Mofunitsitsa.
2. Padzikoli pali ntchito.
Kosowa tidzapitako
Tikatero tisonyeza
Kuti timakonda anthu.
(KOLASI)
Tigwire ntchitoyi
Modzipereka
Ndipo kulikonse tipita
Mofunitsitsa.
3. Kwathu kuno kuli ntchito.
Tikuphunzira maluso.
Taphunzira zinenero
Ndipo tikulalikira.
(KOLASI)
Tigwire ntchitoyi
Modzipereka
Ndipo kulikonse tipita
Mofunitsitsa.
(Onaninso Yoh. 4:35; Mac. 2:8; Aroma 10:14.)