NYIMBO 48
Tiziyenda Ndi Yehova Tsiku Lililonse
Losindikizidwa
(Mika 6:8)
1. Timayenda ndi Yehova
Nthawi zonse modzichepetsa.
Amatikomera mtima
Tikamamusangalatsadi.
Mwa nsembe ya Yesu Khristu,
Tingayende ndi M’lungu.
Choncho timadzipereka
Potumikira Yehova.
2. Mapeto ali pafupi
Ndipo Satana ndi wokwiya.
Timatsutsidwa kwambiri
Choncho tingamachite mantha.
Yehova atiteteza
Ngati timamumvera.
Tizimutumikirabe
Ndi kum’konda nthawi zonse.
3. M’lungu amatithandiza
Ndi mzimu ndi mawu akenso.
Iye amatithandiza
Kudzeranso mu mpingo wake.
Tikayenda ndi Yehova
Tidzachita zabwino.
Choncho tikhulupirike
N’kukhala odzichepetsa.
(Onaninso Gen. 5:24; 6:9; 1 Maf. 2:3, 4.)