NYIMBO 104
Mzimu Woyera Ndi Mphatso Yochokera Kwa Mulungu
Losindikizidwa
1. Yehova M’lungu ndinu wamkulu.
Mumaposa mitima yathu.
Muzitithandiza pamavuto.
Mutilimbitse ndi mzimu wanu.
2. Ndife ochimwa, operewera.
Nthawi zina timalakwitsa.
Tikupempha mutipatse mzimu
Utitsogolere nthawi zonse.
3. Tikafooka ndi kukhumudwa,
Mzimu uzitilimbikitsa.
Mutipatse mphamvu tisagonje.
Muzitipatsa mzimu woyera.
(Onaninso Sal. 51:11; Yoh. 14:26; Mac. 9:31.)