Mmene Anapezera Mphoto Yoyamba
Mnyamata wina analembera kalata nthambi ya ofesi ya Mboni za Yehova mumzinda wa Lusaka ku Zambia, posonyeza kukondwa kwake chifukwa cha Galamukani! Iye anafotokoza kuti analandira mphoto yoyamba chifukwa cha magazini imeneyi atalemba chimangirizo pampikisano wa ana akusekondale. Ana a sukuluŵa anauzidwa kuti alembe nkhani yamutu wakuti “Kupikisana kwa Mayiko a United States ndi Soviet Union Potumiza Anthu Ofufuza Mumlengalenga N’kumene Kwawononga Ndalama Zambiri Padziko Lonse” ndipo anawauza kuti afufuze nkhani imeneyi m’mabuku osiyanasiyana. Mnyamatayu anafotokoza motere:
“Mwamsanga ndinapeza magazini ya Galamukani! ya chingelezi ya September 8, 1992. Magaziniyi inali ndi nkhani imene ndinkafunayo. Ndinagwiritsanso ntchito mfundo zina za m’magazini ena a Galamukani!” Kuwonjezera pa mphoto yoyamba imene mnyamatayu analandira, analandiranso cheke cha ndalama zokwana madola 75. Ndi chimwemwe chodzala tsaya, mnyamatayu anati: “Anthu ambiri aona kuti magazini ya Galamukani! ndi magazini yoyeneradi kulandira mphoto.”
Chifukwa chakuti padziko lonse pali nkhondo ndiponso anthu akuphana kwambiri, kodi munayamba mwaganizapo kuti lilipo boma limene lingadzabweretse mtendere padziko lonse? Nkhani ya boma limeneli ikulongosoledwa m’bulosha la masamba 32 limene limapereka umboni wamphamvu wakuti boma lotero lidzakhalapodi. Koma kodi lidzakhalapo motani? ndiponso liti?
Tikukupemphani kuti muŵerenge bulosha lakuti Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso. Mutha kuitanitsa buloshali polemba zofunika m’kabokosi kali pamunsika ndi kukatumiza ku adiresi imene ili pomwepo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.
□ Nditumizireni bulosha limeneli lakuti Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso
□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.