Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g04 4/8 tsamba 19
  • Kusamvana Pankhani ya Mose

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusamvana Pankhani ya Mose
  • Galamukani!—2004
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Moyo wa Mose Umakukhudzirani
    Galamukani!—2004
  • Kodi Ndimotani Mmene Yesu Kristu Analiri Mneneri Wofanana ndi Mose?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Mose Anali Ndani?
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Anaona Chitsamba Chikuyaka
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
Onani Zambiri
Galamukani!—2004
g04 4/8 tsamba 19

Kusamvana Pankhani ya Mose

AYUDA, Akristu, ndi Asilamu akhala akutsutsana pa nkhani zochuluka. Koma ngakhale samamvana pankhanizi, onseŵa amagwirizana pa chinthu chimodzi: onse amalemekeza kwambiri munthu wotchedwa Mose. Ayuda amati Mose ndi “mphunzitsi woposa aphunzitsi ena onse achiyuda,” ndipo ndiye tate wa mtundu wachiyuda. Akristu amati ndiye anatsogola pokonzekera kubwera kwa Yesu Kristu. Asilamu amaona kuti Mose ndi mmodzi mwa aneneri awo oyambirira ndiponso ofunika kwambiri.

Motero, Mose ali m’gulu la anthu otchuka kwambiri m’mbiri ya anthu. Komabe, kwa zaka zopitirira 100, anthu ophunzira ndiponso atsogoleri azipembedzo akhala akutsutsana kwambiri pa nkhani ya Mose. Ambiri si kuti amangotsutsa kuti Mose anachitadi zozizwitsa ndi kutsogolera Aisrayeli kuchoka ku Aigupto komanso amatsutsa zakuti anakhalako n’komwe. Buku lonena za Mose lotchedwa Moses—A Life, lolembedwa ndi Jonathan Kirsch, linati: “Zimene tinganene mosakayika zokhudza Mose wa m’mbiri yakale uja n’zakuti mwina kalekale, pa nthaŵi inayake ndiponso kumalo kwinakwake kosadziŵika kunalidi munthu winawake wangati munthu wa m’Baibuloyu. Ndipo mwina zimene iyeyu anachita n’zimene zinayambitsa tinthano timene takhala tikusimbidwa m’mbuyo monsemu mpaka kufika pomutchukitsa n’kumusandutsa Mose wolemekezeka ndiponso woyambanitsa anthu amene ali m’Baibuloyu.”

Poyamba, kukayikira kotereku kungaoneke ngati kuti n’komveka ndithu. Mwachitsanzo, anthu otsutsa kuti Mose anakhalakodi amati umboni ulipo m’zinthu zakale zokumbidwa pansi wosonyeza kuti anthu otchulidwa m’Baibulo monga mfumu ya Israyeli yotchedwa Yehu inakhalako, koma palibe umboni uliwonse wotere wosonyeza kuti Mose anakhalakodi. Komabe, zimenezi sizitsimikizira kuti Mose ndi munthu wa m’nthano chabe. Nthaŵi inayake, anthu okayikira ankati anthu ena otchulidwa m’Baibulo monga mfumu ya ku Babulo yotchedwa Belisazara ndi mfumu ya Asuri yotchedwa Sarigoni, nawonso ndi anthu a m’nthano chabe, mpaka pamene zinthu zakale zokumbidwa pansi zinadzatsimikizira kuti analikodi.

Jonathan Kirsch uja anati: “Zinthu zakale zokumbidwa pansi ku Israyeli zogwirizana ndi nthaŵi imene Baibulo linali kulembedwa zilipo zochepa kwambiri moti n’zosadabwitsa kapenanso kukayikitsa kuti palibe chinthu china kupatulako Baibulo chimene chinatchulapo za Mose.” Malingana ndi zimene ananena Kirsch, anthu ena amati zimenezi zikutanthauza kuti n’zosatheka kuti Mose akhale munthu wongopeka chabe, chifukwa chakuti “n’zovuta kungopeka nkhani ya moyo wa munthu yatsatanetsatane chonchi ndiponso yofotokoza makambitsirano osiyanasiyana a anthu komanso yofotokoza zinthu zina zambirimbiri . . . ”

Kaya ndinu achipembedzo chotani, n’zotheka kuti mumadziŵako ndithu zina n’zina zokhudza moyo wa Mose: monga za kukumana kwake ndi Mulungu pa chitsamba choyaka, za ulendo wautali wa Aisrayeli wochoka muukapolo ku Aigupto, ndiponso za kugaŵikana kwa Nyanja Yofiira. Koma kodi pali mfundo iliyonse yokhutiritsa munthu kukhulupirira kuti zimenezi zinachitikadi? Kapena kodi Mose ndi munthu wa m’nthano zakale zongopeka chabe? Nkhani yotsatirayi ilongosola mafunso ochititsa chidwi ameneŵa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena