Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 12/10 tsamba 13-31
  • Zoti Banja Likambirane

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zoti Banja Likambirane
  • Galamukani!—2010
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Anaganiza Bwino?
  • KODI MUKUDZIWA ZOTANI ZOKHUDZA MTUMWI PETULO?
  • ZITHUNZI ZOTI ANA APEZE
  • KUCHOKERA M’MAGAZINI INO
  • MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31
  • Zoti Banja Likambirane
    Galamukani!—2010
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
    Galamukani!—2009
  • Zoti Banja Likambirane
    Galamukani!—2010
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
    Galamukani!—2008
Onani Zambiri
Galamukani!—2010
g 12/10 tsamba 13-31

Zoti Banja Likambirane

Kodi Anaganiza Bwino?

Werengani Numeri 13:1, 2, 25-33; 14:3, 6-12. Ndiyeno onani chithunzichi. Kenako lembani mayankho anu pamizere ili m’munsiyi.

1. N’chifukwa chiyani ambiri mwa anthu amene anakazonda dziko aja ananena zoipa za dzikolo?

․․․․․

2. Kodi chinachitika n’chiyani chifukwa cha zinthu zoipa zimene anthu 10 ozonda dzikowo ananena?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Numeri 14:26-38.

․․․․․

3. N’chifukwa chiyani Yoswa ndi Kalebe anali ndi chikhulupiriro chonse kuti apambana?

․․․․․

KAMBIRANANI:

Ngati banja lanu litakumana ndi mavuto, kodi mungatani kuti mukhale ngati Yoswa ndi Kalebe, osati ngati anthu ena 10 amene anakazonda dziko aja?

KODI MUKUDZIWA ZOTANI ZOKHUDZA MTUMWI PETULO?

4. Kodi Petulo amadziwika ndi mayina asanu ati m’Baibulo?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Mateyu 10:2; 16:16; Yohane 1:42; Machitidwe 15:14.

․․․․․

5. Kodi Petulo anakwatirapo?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 1 Akorinto 9:5.

․․․․․

KAMBIRANANI:

Fotokozani nkhani ina iliyonse yokhudza Petulo imene imakusangalatsani. Kodi ndi makhalidwe ati a Petulo amene mungafune kutsanzira, ndipo mungawatsanzire bwanji?

ZITHUNZI ZOTI ANA APEZE

Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Kenako fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

KUCHOKERA M’MAGAZINI INO

Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.

TSAMBA 7 Kodi tiyenera kulankhula chiyani ndi anzathu? Aefeso 4:․․․

TSAMBA 8 Kodi kudziwa choonadi kungakuthandizeni bwanji? Yohane 8:․․․

TSAMBA 11 Kodi n’chiyani chidzachitikire mdani womaliza? 1 Akorinto 15:․․․

TSAMBA 24 Kodi muyenera kuthawa chiyani? 1 Akorinto 6:․․․

● Mayankho ali pa tsamba 13

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31

1. Iwo anali ndi mantha ndipo analibe chikhulupiriro mwa Yehova.—Numeri 14:3, 11.

2. Amuna onse a zaka 20 kupita m’tsogolo anafa m’chipululu, kupatulapo Yoswa ndi Kalebe.

3. Ankadziwa kuti Yehova ali nawo.—Numeri 14:9.

4. Simoni, Petulo, Simoni Petulo, Kefa, Sumeoni.

5. Inde.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena