1 Muzipempha Ena Kuti Azikuthandizani
“Mumpingo tili ndi anzathu omwe amatikonda komanso kutithandiza kwambiri. Iwo amationa ngati abale awo enieni.”—ANATERO LIZAAN, MAYI YEMWE AKULERA YEKHA ANA AKE AWIRI ACHINYAMATA.
Vuto.
Mayi wina dzina lake Alina, yemwe akulera yekha ana ake awiri aamuna, anati: “Nthawi zambiri ndimakhala wotopa komanso wotanganidwa.” Ndi mmenenso zilili ndi azimayi ambiri omwe akulera okha ana. N’chifukwa chake makolo ambiri amayesetsa kupeza anthu omwe angamasuke kuwapempha kuti awathandize.
Zimene mungachite.
Pemphani anzanu kapena achibale kuti azikuthandizani. Mungachite bwino kulemba mayina a anthu amene mungathe kuwapempha kuti azikuthandizani kaya ndi kusamalira ana, thiransipoti, kukonza zimene zawonongeka panyumba kapena kukulimbikitsani. Ndiponso mukhoza kusintha anthu amene angakuthandizeni mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa nthawiyo. Komanso mungafufuze kuti mudziwe ngati boma kapena mabungwe ena omwe si aboma angakuthandizeni.
Mayi wina, dzina lake Renata yemwe ndi wa Mboni za Yehova, amathandizidwa kwambiri ndi Akhristu anzake. Iye ananena kuti: “Nthawi zonse iwo amakhala okonzeka kundithandiza. Ndikukumbukira kuti nthawi ina ineyo ndi ana anga awiri a zaka 9 tinadwala chimfine moti sindikanakwanitsa kuphika. Abale ndi alongo mu mpingo mwathu atamva zimenezi, anakonza zoti tsiku lililonse kuzibwera munthu wodzatipatsa chakudya. Zimenezi zinandikumbutsa mawu opezeka m’Baibulo pa lemba la 1 Yohane 3:18 lomwe limati: ‘Ana anga okondedwa, tisamakondane ndi mawu okha kapena ndi pakamwa pokha, koma tizisonyezana chikondi chenicheni m’zochita zathu.’”
Bambo wa anawo angathandize. Ngati banja linathera kukhoti, ndipo khotilo linalamula kuti bambo wa anawo akhoza kumakawaona ndipo akufuna kuwathandiza, mayiyo angalole kuti aziwathandiza. Zimenezi zingakhale zothandiza chifukwa nthawi zina ana amafuna kucheza ndi bambo awo.a
Muziwaphunzitsa ntchito zapakhomo. Mukamawapatsa ana anu ntchito zogwirizana ndi msinkhu wawo, mumadzichepetsera ntchito. Anawo amaphunzira kuchita zinthu mwanzeru komanso zimawathandiza kuti azikonda ntchito ndipo zimenezi zingadzawathandize m’tsogolo.
a Makolo achikhristu ayenera kuyesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo pothandiza ana awo ndipo pochita zimenezi ayenera kuganizira zimene zingathandize anawo. Ayeneranso kutsatira zimene khoti linagamula.