Zimene Achinyamata Amadzifunsa
Kodi Ndingatani Ngati Ndapanikizika Maganizo?
Pa mawu amene ali m’munsimu, kodi ndi mawu ati amene akusonyeza mmene mulili?
Ndapanikizika maganizo koopsa
Zafika poti sindingathe kupirira
Ndapanikizika pang’ono
Sindinapanikizikepo maganizo
MUNTHU amene akulimbana ndi vuto lopanikizika maganizo, tingamuyerekezere ndi galimoto. Galimoto yaikulu ngati thiraki ikhoza kuyenda mosavuta ulendo wautali ikukoka ngolo yolemera kwambiri. Koma galimoto yaing’ono ingavutike kuchita zimenezi ndipo ikhoza kuwonongeka ngati itakoka ngoloyo ngakhale pa kamtunda kochepa. Mofanana ndi zimenezi, munthu amene wapanikizika maganizo amakumana ndi mavuto ambiri.
Ndiye kodi munthu angatani ngati wapanikizika maganizo? Choyamba angafunike kuchepetsa zochita kapena kupeza njira zina zoti asamapanikizike kwambiri. Tiyeni tione mmene angachitire zimenezi.
Kuchepetsa Zochita
VUTO: Kudzipanikiza ndi zochita zambiri.
“Nthawi zambiri anthu amakonda kundipempha kuti ndiwathandize zinazake kapena kuti tipite kocheza pa nthawi imene ndili ndi zochita zina. Koma ndimangovomera chifukwa sindifuna kuwakhumudwitsa.”—Anatero Karina.a
ZIMENE MUNGACHITE: Nthawi zina muzikana.
Baibulo limanena kuti: “Nzeru zimakhala ndi anthu odzichepetsa.” (Miyambo 11:2) Munthu wodzichepetsa amadziwa zimene sangakwanitse kuchita. Choncho nthawi zina amakana ngati anthu ena amupempha kuchita zinthu zimene akuona kuti sangakwanitse.
Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti muzingokana chilichonse munthu akakupemphani. Mwachitsanzo, simuyenera kukana ngati makolo anu akukumbutsani kuti mugwire ntchito zapakhomo. Koma mukamangolola zilizonse zimene munthu wakupemphani kuchita, mukhoza kupanikizika kwambiri. Ndipotu ngakhale thiraki yamphamvu kwambiri, imakhala ndi malire pa katundu amene inganyamule.
Mfundo yothandiza: Ngati mumachita manyazi kukana zinthu zina zimene munthu wakupemphani kuchita, mungamuuze kuti: “Ndikuyankhanibe.” Ndiyeno musanakamuyankhe mudzifunse kuti: ‘Kodi ndili ndi nthawi komanso mphamvu zochitira zimene wandipemphazi?’
VUTO: Kuzengereza
“Ndikaona kuti ntchito inayake imene ndikufunika kugwira ndi yovuta, ndimangoinyalanyaza. Koma mumtima ndimasowa mtendere chifukwa ndimadziwa kuti ndikufunikabe kuigwira. Koma ndikayamba kuigwira, ndimaigwira mothamanga, zomwe zimachititsa kuti ndipanikizike maganizo.”—Anatero Serena.
ZIMENE MUNGACHITE: Muziyamba nthawi yomweyo.
Baibulo limatichenjeza kuti: “Musakhale aulesi pa ntchito yanu.” (Aroma 12:11) Ntchito yovuta imachititsa munthu kuvutika maganizo. Koma akamazengereza kugwira ntchitoyo, m’pamene amapanikizika kwambiri.
Kuti musamachite ulesi, mungachite bwino kulemba ndandanda ya ntchito zimene mukufunika kugwira. Ntchito zikuluzikulu muzigawe m’zigawo zing’onozing’ono n’cholinga choti mukwanitse kuzigwira. Mtsikana wina, dzina lake Carol, ananena kuti: “Ndimakonda kugwira ntchito motsatira ndandanda. Ndimalemba ntchito zonse kenako n’kuthetha zimene sizimandisangalatsa. Zimenezi zimandithandiza kuti ndizichita zinthu zimene zimandisangalatsa.”
Mfundo yothandiza: Ngati zimakuvutani kuti muyambe kugwira ntchito inayake, mungatchere wotchi mwina kuti mugwire ntchitoyo kwa mphindi 10 kapena 15 ndipo mukatero muyambe kuigwira nthawi yomweyo. Mphindi zimenezi zikatha mungakhale mutagwira mbali yaikulu ya ntchitoyo. Zikatero sizikhala zovuta kuti muimalize.
Muzionetsetsa kuti m’chipinda mwanu ndi mosamalidwa bwino. Nkhawa zingawonjezereke ngati zinthu zili mbwee m’chipinda mwanu moti mukuchita kuvutika kupeza zovala zoyera kapena pamene pali homuweki yanu. Choncho mungachite bwino kukonzeratu zinthu m’chipinda mwanu musanagone kuti m’mawa musamavutike kupeza zinthu zanu.
Pezani Njira Zina
Muzisamalira thanzi lanu.
Akatswiri azachipatala amanena kuti munthu amafunika kudya zakudya zopatsa thanzi, kuchita masewera olimbitsa thupi komanso kugona mokwanira kuti asamapanikizike maganizo.b Ndipotu kusamalira thanzi lanu sikuchita kufunika zinthu zambiri. Mwachitsanzo, pa nkhani yogona, mungafunike kuchita zotsatirazi.
Muzigona mokwanira. Muzionetsetsa kuti mukugona ndi kudzuka nthawi yofanana tsiku lililonse makamaka mkati mwa mlungu.
Musamadzichulukitsire zochita mukatsala pang’ono kugona. Mukachita masewera olimbitsa thupi, muzionetsetsa kuti padutse maola atatu musanapite kogona. Komanso musamadye kwambiri, kumwa tiyi kapena khofi mukatsala pang’ono kugona.
Mukamagona muzionetsetsa kuti m’chipinda chanu muli mdima, mulibe phokoso komanso muzionetsetsa kuti mwagona pabwino.
Muzipempha anthu ena kuti akuthandizeni.
Musamachite manyazi kupempha makolo kapena anzanu kuti akuthandizeni. Ndipotu kafukufuku akusonyeza kuti anthu amene apanikizika maganizo akalimbikitsidwa ndi ena, mtima wawo, mitsempha yamagazi komanso chitetezo chawo cha m’thupi chimakhala champhamvu.
Zimenezi zikugwirizana ndi zimene Baibulo limanena kuti: “Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauweramitsa, koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa.” (Miyambo 12:25) Mukakhala ndi “nkhawa mumtima” anzanu angakuuzeni “mawu abwino” omwe angakulimbikitseni.
Ngati mukufuna mfundo zina zokuthandizani ngati mwapanikizika maganizo, werengani mitu yotsatirayi m’buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa—Buku Lachiwiri, ndi lakuti Questions Young People Ask—Answers That Work, Volume 1, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
VOLUME 1
Chapter 18: How Can I Cope With Stress at School?
Chapter 21: How Can I Manage My Time?
BUKU LACHIWIRI
a Tasintha mayina ena m’nkhani ino.
FUNSANI MAKOLO ANU
Kodi inuyo mumati mukapanikizika maganizo zimafika pati? Nanga ndi njira iti imene imakuthandizani kwambiri mukapanikizika maganizo?