Sanataye Nane Mtima
Ndinkakonda kuchita zachiwawa komanso kumwa mowa mwauchidakwa. Kenako tsiku lina ndinalandira uthenga womvetsa chisoni womwe unachititsa kuti ndiganizire mofatsa za moyo wanga. Taimani ndikufotokozereni.
NDINABADWA m’chaka cha 1943, m’tauni ya Rubottom, ku Oklahoma m’dziko la United States. Kuyambira ndili mwana ndinkakonda kuchita zachiwawa. Kenako nditapita ku sekondale ndinayamba kumwa mowa mwauchidakwa. Chifukwa choti bambo anga analinso chidakwa komanso ankakonda zachiwawa, tinayamba kugwirizana kwambiri. Tinkapitira limodzi ku dansi komanso kumalo ena azisangalalo n’cholinga choti tikamwe komanso kuchita ndewu.
M’chaka cha 1966, ndinakwatirana ndi Shirley ndipo tinakhala ndi ana awiri, mayina awo Angela ndi Shawn. Koma ndinapitirizabe kumwa mowa kwambiri. Kuti ndizipeza ndalama ndinkalima komanso kugulitsa chamba. Ndinkagwiranso ntchito yaubaunsa m’mabala zomwe zinkandithandiza kuti ndizipeza mowa mosavuta komanso ndizichita ndewu. Nthawi imeneyo sindinkaopa aliyense kapena chilichonse ndipo sindinkasamala za wina aliyense.
“Usadzayerekeze Kubweretsa Aliyense Kuti Adzandilalikire”
Kenako msuweni wake wa Shirley anasamukira ku California komwe anayamba kuphunzira Baibulo ndipo pasanapite nthawi anakhala wa Mboni za Yehova. Atabwerera ku Oklahoma anayamba kumuuza mkazi wanga zimene ankaphunzira ndipo mkazi wangayo anazindikira kuti zinali zoona. Kenako Shirley anayamba kuphunzira Baibulo ndipo anabatizidwa mu 1976, n’kukhala wa Mboni za Yehova. Koma ine ndinalibe chidwi ndi chipembedzo chake. Nthawi zambiri ndinkamuuza kuti: “Usadzayerekeze kubweretsa aliyense kuti adzandilalikire. Ine sindingasinthe.”
Komabe Shirley sanasiye kutsatira mfundo za m’Baibulo ndipo anapitiriza kundikonda. Nthawi zambiri akamapita ku misonkhano yachikhristu ku Nyumba ya Ufumu ankandiuza mwaulemu kuti ndipite naye. Komanso mwana wanga Angela ankakonda kundiuza kuti: “Adadi, ifetu timafuna kuti muzipita nafe ku misonkhano.”
Nthawi zambiri ndinkayenda ndi mfuti chifukwa cha zimene ndinkachita. Komanso ndinkatha masiku ambiri ndisanafike pakhomo zomwe zinkakhumudwitsa mkazi wanga. Koma ndikabwera, ndinkaonetsetsa kuti ndizipita ku misonkhano maulendo angapo kuti mtima wake ukhazikike. Ku misonkhanoko a Mboni ankandilandira mwansangala ndipo zimene ankaphunzitsa zinkaoneka kuti ndi zomveka ndithu.
Nthawi ina mkulu wina mumpingowo anandipempha kuti aziphunzira nane Baibulo ndipo ndinavomera. Koma sindinkagwiritsa ntchito zimene ndinkaphunzirazo chifukwa ndinkapitiriza kucheza ndi anzanga omwe anali ndi makhalidwe oipa. Mkuluyo atazindikira zimenezo anandiuza mfundo zina za m’Baibulo zosonyeza mavuto amene angabwere chifukwa chogwirizana ndi anthu oipa. (1 Akorinto 15:33) Ngakhale kuti malangizo amenewa anali ochokera m’Baibulo, ineyo ndinakwiya nawo moti ndinasiya kuphunzira n’kumapitiriza kuchita makhalidwe oipa. Shirley ndi ana anga anakhumudwa kwambiri ndi zimenezi.
“Timakukondanibe Kwambiri”
Mu 1983, ndinalandira uthenga womvetsa chisoni woti mwana wa mlamu wanga, yemwe ndinkamukonda kwambiri, wamwalira. Imfa yake inandikhudza kwambiri moti ndinayamba kuganizira kwambiri za moyo wanga. Ndinazindikira kuti zimene ndinkachita zinkakhumudwitsa anthu a m’banja mwanga, omwenso ndinkawaona kuti ndi ofunika kwambiri. Zimenezi ndi zimene zinachititsa kuti ndisinthe. Pa mwambo wamalirowo, munthu wina wa Mboni yemwe anali wachikulire, dzina lake John, anandigwira paphewa n’kundiuza kuti: “Timakukondanibe kwambiri.” Mawu amenewa anandilimbikitsa kwambiri. Tsiku lotsatira ndinamuimbira mkuluyo foni n’kumuuza kuti ndikufuna ndiyambirenso kuphunzira Baibulo. Ndinkaona kuti ulendo uno ndikhoza kusintha.
Tsiku loyamba kuphunzira tinakambirana nkhani ya pemphero ndipo ndinamuuza John kuti ndiyesetsa kumapemphera. Tsiku lotsatira ndinayamba kufunafuna ntchito yabwino koma sindinaipeze. Ndili m’galimoto yanga ndinapemphera mokweza kuti, “Yehova, ngati mukufuna kuti ndipitirize kukhala m’dera lino, mundipezere ntchito.” Koma kenako ndinaganiza kuti, ‘N’zopusatu ndikuchitazi, kumangodzilankhulira ndekhandekha zoona?’ Zimenezi zinasonyeza kuti chikhulupiriro changa mwa Mulungu, yemwe ndi “Wakumva pemphero,” chinali chidakali chochepa. (Salimo 65:2) Koma n’zodabwitsa kuti tsiku lotsatira ndinapeza ntchito.
Nditaona kuti pemphero ndi lamphamvu, ndinayamba kukonda kwambiri Yehova komanso kumudalira
Kuyambira nthawi imeneyo, ndinayamba kupemphera kawirikawiri komanso mochokera pansi pa mtima. Nthawi zambiri ndinkaona kuti Yehova akundidalitsa. Kuyambira kale ndinkakhulupirira kuti kuli Mulungu koma zimene zinandichitikirazi zinandithandiza kuona kuti mawu a pa 1 Yohane 5:14 ndi oona. Lembali limati: “Chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.” Nditaona kuti pemphero ndi lamphamvu, ndinayamba kukonda kwambiri Yehova komanso kumudalira.—Miyambo 3:5, 6.
Nditayambiranso kupita ku misonkhano, a Mboni anandilandira bwino kwambiri. Komanso ndinayamba kuona kuti iwo amakondanadi “kwambiri kuchokera mumtima” ndipo zimenezi zinandikhudza kwambiri. (1 Petulo 1:22) Ndinamvetsanso mawu a pa Miyambo 13:20 omwe amati: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.”
Kwa zaka zambiri ndinkachita zinthu zimene zinkakhumudwitsa kwambiri banja langa komanso kuchititsa kuti lizikumana ndi mavuto. Koma tsopano ndinayamba kuyesetsa kumachita zinthu mwamtendere komanso kuti ndikhale mwamuna wabwino, bambo wabwino ndiponso munthu wosavuta kulankhula naye. Ndinayamba kutsatira mfundo ya m’Baibulo yakuti: “Amuna akonde akazi awo monga matupi awo” komanso yakuti: “Inu abambo, musamakwiyitse ana anu, kuti angakhale okhumudwa.”—Aefeso 5:28; Akolose 3:21.
Zinthu zinayamba kusintha kwambiri m’banja lathu chifukwa cha mmene ndinasinthira khalidwe langa. Chifukwa cha zimenezi ndinaonanso kuti mawu a Yesu a pa Mateyu 5:3 ndi oona. Lembali limati: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.” Zimenezi zinachititsa kuti ndizikhaladi wosangalala.
Mu June 1984, mwana wanga Angela anamufunsa mafunso pa nkhani ina imene inakambidwa pa msonkhano wapadera wa Mboni za Yehova. Iye anafotokoza mmene ndinalili poyamba komanso mmene ndasinthira. Anamaliza ndi kunena kuti anali wosangalala kwambiri kundiona ndili m’gulu la anthu omwe amabatizidwa tsiku limenelo.
Ndine wosangalala kwambiri kuti Yehova sataya mtima ndi anthu ngati ineyo. Komanso ndine wosangalala kwambiri kuti mkazi wanga Shirley limodzi ndi ana athu awiri sanataye nane mtima. Monga Mkhristu wokhulupirika, mkazi wanga ankatsatira kwambiri malangizo a pa 1 Petulo 3:1 omwe amati: “Akazi, muzigonjera amuna anu kuti ngati ali osamvera mawu akopeke, osati ndi mawu, koma ndi khalidwe lanu.” Chifukwa chakuti pa nthawi yonse imene ndinkachita zinthu zosalongosoka, mkazi wanga anali wokhulupirika, woleza mtima komanso wakhalidwe labwino, zinathandiza kuti ndisinthe khalidwe langa n’kuphunzira choonadi.
Kuyambira nthawi imene ndinabatizidwa, ndimagwiritsa ntchito chitsanzo cha mkazi wanga ndikafuna kulimbikitsa Akhristu amene ali ndi mwamuna kapena mkazi wosakhulupirira. Ndimawalimbikitsa kuti asataye nawo mtima. Nthawi zambiri ndimawauza kuti: “Nthawi ikadzakwana, Yehova adzagwiritsa ntchito Mawu ake, omwe ndi Baibulo, komanso khalidwe lanu labwino kuti mwamuna kapena mkazi wanuyo asinthe ngakhale kuti zingaoneke ngati sangasinthe.”