3 Muziyamba Kuchita Zinthu Zofunika Kwambiri
“Nthawi zambiri ndinkakhala wotopa ndipo zinkandivuta kugawa nthawi yopita kuntchito, kusamalira ana, kuchita zinthu zauzimu, kugwira ntchito zapakhomo komanso kupuma.”—ANATERO YOKO WA KU JAPAN.
Vuto.
Mayi wina yemwe ali ndi ana aamuna awiri, dzina lake Miranda, ananena kuti: “Vuto langa lalikulu ndi loti kuwonjezera pa kugwira ntchito, ndimafunikanso kusamalira ana anga kuti akule bwino, kuwalimbikitsa komanso kuwaphunzitsa mawu a Mulungu. Ndimafunika kuchita zonsezo ndekha popanda mwamuna wanga woti azindithandiza.”
Zimene mungachite.
Ganizirani zimene mukuona kuti ndi zofunikira kwambiri kwa inuyo komanso kwa ana anu, ndiye muziyambirira kuchita zimenezo.
Nthawi zonse muziyesetsa kuchita zinthu zofunika poyamba ndipo muzigwiritsa bwino ntchito nthawi yanu komanso ndalama zanu. Mwachitsanzo, thanzi la ana anu ndilofunika kwambiri. Pajatu kupewa kumaposa kuchiza. Choncho ndibwino kugwiritsa ntchito ndalama zanu pogula zakudya zopatsa thanzi kusiyana ndi kukalipira kuchipatala ana anu atadwala. Musanagule zinthu, muzilemba zokhazo zomwe zikufunikira. Zimenezi zimathandiza kuti musamangogula zinthu chifukwa choti mwaziona. Bambo wina wa ku United States, yemwe akulera yekha ana ake anayi, dzina lake Roberto, ananena kuti: “Ndimakonda kuphika m’malo mokagula zakudya zophikaphika. Ndaonanso kuti ndi bwino kuti ndizingogula zinthu zimene banja lathu likufunikiradi.”
Kupewa kumaposa kuchiza. Choncho ndibwino kugwiritsa ntchito ndalama zanu pogula zakudya zopatsa thanzi kusiyana ndi kukalipira kuchipatala ana anu atadwala
Tayani zinthu zosafunika zomwe simuzigwiritsa ntchito monga mabuku, zovala ndi zipangizo zamagetsi. Mayi wina anati: “Mukakhala ndi katundu wambiri mumakhalanso ndi nkhawa zambiri chifukwa mumafunika nthawi yambiri yoti muzimusamalira komanso kukonzetsa ngati wawonongeka. Choncho ngati mukufuna kuti musamakhale ndi nkhawa chifukwa cha katundu m’pofunika kungochepetsa katunduyo.”
Muwaphunzitse ana anu kuti azikonza bwinobwino chipinda chawo tsiku lililonse. Muzionetsetsa kuti asamangosiya zinthu zili mbwee m’nyumba. Zimenezi zimathandiza ana anu kuti aziona kuti ndi udindo wawo kusamalira malo amene amagona komanso nyumba yonse. Koma kuti ana anu atsatire malangizo amenewa muyenera kuyamba ndinu kusamalira panyumbapo.
Ngakhale kuti mungakhale ndi zambiri zochita, muzipeza nthawi yocheza ndi ana anu osati kumangocheza nawo mwa apo ndi apo. Ana anu amafuna kuti muzicheza nawo komanso kuwasonyeza kuti mumawakonda.—Deuteronomo 6:7.
Muziyesetsa kupeza nthawi yodyera limodzi chakudya monga banja ndipo nthawi imeneyo izikhala yosangalatsa. Mayi wina, yemwe ali ndi ana atatu, dzina lake Colette, ananena kuti: “Tinakonza kuti tizidyera limodzi chakudya chamadzulo aliyense alipo ndipo timaonetsetsa kuti pa nthawi imeneyi tizilimbikitsana ndi kukambirana zinthu zauzimu. Tonse timaona kuti nthawi imeneyi ndi yofunika kwambiri m’banja mwathu.”