4 Muziika Malamulo Omveka Bwino
“Masiku ano, kulera ana si nkhani yamasewera, makamaka achinyamata chifukwa pali zinthu zambiri zimene zingawachititse kuti asamamvere makolo.”—ANATERO DULCE, WA KU SOUTH AFRICA.
Vuto.
Baibulo linanena kuti ‘m’masiku otsiriza, ana adzakhala osamvera makolo.’—2 Timoteyo 3:1, 2.
Zimene mungachite.
Buku lina lolembedwa ndi Brook Noel, linanena kuti: “Kuti ana akule bwino amafunika kudziwa malamulo a makolo awo komanso zimene makolowo amafuna kuti anawo azichita.” (The Single Parent Resource) Katswiri wina woona za mabanja, dzina lake Barry G. Ginsberg, ananena kuti: “Zinthu m’banja zimayenda bwino ngati pali malamulo omveka bwino. Ngati aliyense akudziwa bwino malamulo amene ayenera kutsatira, banja limakhala losangalala.” Komano kodi mungatani kuti mukhazikitse malamulo amenewa?
Inde wanu akhaledi inde ndipo ayi wanu akhaledi ayi. (Mateyu 5:37) Kafukufuku wina amene anachitika ku Australia, anasonyeza kuti nthawi zambiri ana samvera makolo awo ngati makolowo amalephera kuwaletsa komanso ngati amangowalekerera kuti azichita zofuna zawo. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Mwana womulekerera adzachititsa manyazi mayi ake.”—Miyambo 29:15.
Musamalekerere ana anu kuti azingochita zofuna zawo mwina powamvera chisoni kuti alibe kholo lina loti liziwathandiza. Yasmin amene tinamutchula m’nkhani yapita ija ananena kuti: “Nthawi zina ana anga akamachita zinthu zosayenera, ndimawamvera chisoni poganiza kuti akuchita zimenezi chifukwa choti ndikuwalera popanda bambo awo.” Komabe, monga mmene tionere m’ndime yotsatira, mayiyu sanalole kuti maganizo amenewa azimulepheretsa kupereka chilango kwa ana ake akalakwa.
Musamasinthesinthe. Buku lina linanena kuti: “Ana akadziwa kuti ngati atalakwitsa zinazake amapatsidwa chilango, amachita zinthu mwanzeru komanso amakhala ndi khalidwe labwino.” (American Journal of Orthopsychiatry) Yasmin uja ananena kuti: “Ndinakambirana ndi ana anga za kufunika kokhala ndi khalidwe labwino komanso chilango chimene ndingawapatse akalakwitsa. Ndiye akalakwitsa chinachake, ndimawapatsa chilango chomwe tinakambirana chija. Komabe ndimawamvetsera kaye akamalankhula kenako ndimawafotokozera mmene zimene achitazo zakhudzira banja lathu. Pamapeto pake m’pamene ndimawapatsa chilango.”
Musamapereke chilango mutakwiya. Ngakhale kuti mumafunika kupereka chilango ana anu akalakwitsa ndi bwinonso kuona ngati m’poyeneradi kupereka chilango. Lemba la Yakobo 3:17 limati: “Nzeru yochokera kumwamba . . . ndi . . . yololera.” Anthu ololera samachita zinthu atakwiya kapena mopupuluma. Komabe sikuti amangokakamira kutsatira malamulo nthawi zonse. M’malomwake amaganiza kaye, mwinanso kupemphera kumene, kenako n’kuchita zinthu modekha komanso moyenera.
Mukamasonyeza chitsanzo chabwino, kupereka chilango chimene munagwirizana, kukhala wololera komanso kupewa kulekerera ana, zidzathandiza kuti muteteze ana anu.