Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 11/12 tsamba 9
  • 5 Aphunzitseni Kutsatira Mfundo za M’Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 5 Aphunzitseni Kutsatira Mfundo za M’Baibulo
  • Galamukani!—2012
  • Nkhani Yofanana
  • Makolo Phunzitsani Ana Anu Mwachikondi
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Makolo Olera Ana Ali Okha Amakhala ndi Mavuto Ambiri
    Galamukani!—2002
  • Makolo, Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikonda Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Makhalidwe Abwino Angakuthandizeni Kuti Muzisangalala
    Galamukani!—2013
Onani Zambiri
Galamukani!—2012
g 11/12 tsamba 9

5 Aphunzitseni Kutsatira Mfundo za M’Baibulo

“Poyamba sindinkatsatira mfundo za m’Baibulo ndipo zimenezi zinkachititsa kuti zizindivuta kulangiza ana anga. Koma masiku ano sizindivuta chifukwa ndimatsatira mfundo za m’Baibulo.”​—ANATERO ELIZABETH, WA KU SOUTH AFRICA.

Vuto.

Ana amakakamizidwa ndi anzawo kuti azichita zinthu zoipa kusukulu komanso mabanja ambiri akhoza kutengera makhalidwe oipa amene dzikoli limalimbikitsa. Choncho kuti ana asatengere makhalidwe amenewa, makolo ayenera kuwaphunzitsa makhalidwe abwino. Ngati makolo atalephera kuchita zimenezi ndiye kuti anawo sangakule bwino.

Zimene mungachite.

Makolo ambiri omwe akulera okha ana, kuphatikizapo makolo amene atchulidwa mu nkhani zino amayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo chifukwa amaona kuti ndi malangizo apamwamba kwambiri ochokera kwa Mulungu. Mwachitsanzo, taonani zimene Baibulo limanena pa nkhani ya chikondi, lomwe ndi khalidwe lofunika kwambiri.

“Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima. Chikondi sichichita nsanje, sichidzitama, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichisamala zofuna zake zokha, sichikwiya. Sichisunga zifukwa. Sichikondwera ndi zosalungama, koma chimakondwera ndi choonadi. Chimakwirira zinthu zonse, . . . chimayembekezera zinthu zonse, chimapirira zinthu zonse. Chikondi sichitha.”​—1 Akorinto 13:4-8.

Ngati makolo ali ndi chikondi chimenechi ana amakula bwino. Mayi wina wa ku France, dzina lake Colette, yemwe tamutchula poyamba uja ananena kuti: “Nthawi zambiri ndinkawauza ana anga kuti ndimawakonda komanso kuti iwo ndi oyenera kusamalidwa chifukwa ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Zimenezi zinathandiza kuti azindilemekeza komanso azilemekeza bambo awo ngakhale kuti banja lathu linatha. Komanso zathandiza kuti m’banja mwathu tizidalirana komanso kulemekezana.”​—Salimo 127:3.

Mayi winanso, dzina lake Anna, wa ku Poland, ananena kuti: “Ana anga akayambana, ndimawakumbutsa mawu a Yesu akuti, zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.” (Mateyu 7:12) Roberto, yemwe tamutchula kale uja anakumana ndi vuto limene makolo ambiri omwe akulera okha ana amakumana nalo. Iye anati: “Ana anga amasokonekeza kwambiri chifukwa amafunika kutsatira mfundo zanga komanso za mayi awo. Nthawi zambiri ndikawalangiza pogwiritsa ntchito Baibulo, amaona kuti mayi awo ndi abwino kuposa ineyo.” Kenako iye ananena kuti: “Nthawi zina mkazi kapena mwamuna amene unali naye pa banja angamapatse anawo mphatso n’cholinga choti azimukonda kwambiri. Zimenezi zimachititsa kuti nawenso ukakamizike kugula mphatso n’cholinga choti anawo azikukonda. Koma njira yabwino ndi kukambirana ndi anawo kuti aone kuti zimene mumachita powasamalira tsiku ndi tsiku komanso malangizo ochokera kwa Yehova amene mumawapatsa ndi ofunika kwambiri kuposa mphatso zimene angapatsidwe.”

N’zoona kuti kutsatira malangizo a m’Baibulo n’kovuta koma munthu amene amayesetsa kutsatira malangizowa amapeza madalitso ambiri. Mayi wina wa ku South Africa, dzina lake Sarah, yemwe akulera yekha ana, ananena kuti: “Ndimasangalala kuti ana anga akula akutsatira malangizo a Yehova. N’zoona kuti takhala tikukumana ndi mavuto koma taona kuti nthawi zonse Yehova wakhala akutithandiza kwambiri.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena