Baibulo Ndi Buku la Maulosi Olondola Gawo 7
“Mapeto Adzafika”
Nkhani zokwanira 8 zimene zikhale zikutuluka mu Galamukani!, zizifotokoza maulosi osiyanasiyana a m’Baibulo. Nkhanizi zikuthandizani kupeza mayankho a mafunso awa: Kodi maulosi a m’Baibulo analembedwa ndi anthu kapena pali umboni wakuti analembedwa ndi Mulungu? Kuwerenga nkhanizi kukuthandizani kudziwa zoona zenizeni.
KODI zimakupwetekani mukamaona maboma ankhanza akupondezera komanso kudyera masuku pamutu nzika zawo? Kodi mumaona kuti sichilungamo kuti makampani akuluakulu azibera anthu osauka n’cholinga cholemeretsa anthu omwe ali kale ndi ndalama zambiri? Kapena kodi zimakuwawani kuona atsogoleri achipembedzo akubera anthu a m’zipembedzo zawo komanso kuwaphunzitsa zabodza? Dziwani kuti Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amadana ndi makhalidwe oipa amenewa. M’nkhani ino tikambirana (1) Maulosi a m’Baibulo osonyeza kuti Mulungu athetsa zoipa zonse ndi kuwononga anthu onse oipa ndiponso (2) Chifukwa chake sitiyenera kukayikira maulosi amenewa.
Mulungu Athetsa Zoipa Zonse
Nkhani ya nambala 6 ya nkhani zino, inafotokoza za chizindikiro cha mbali zingapo chimene Yesu ananena chosonyeza kuti mapeto ayandikira. Mbali imodzi ya chizindikirochi ndi kulalikidwa kwa uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu. Ufumu umenewu ndi boma la Mulungu lomwe posachedwapa liyamba kulamulira dziko lapansi. (Danieli 2:44; Mateyu 24:3, 14) Yesu ananena kuti ntchito yolalikira uthenga umenewu ikadzatha, “mapeto adzafika.” Mungadabwe kudziwa kuti chinthu choyamba chimene Mulungu adzawononge ndi chipembedzo chonyenga, chomwe chimaphunzitsa zinthu zabodza zokhudza Mulunguyo. M’Baibulo, chipembedzo chonyenga amachiyerekezera ndi hule lalikulu lomwe ndi “Babulo Wamkulu.”—Chivumbulutso 17:1, 5; onani bokosi lakuti “Kodi Tingamudziwe Bwanji Babulo Wamkulu?” patsamba 13.
Ulosi woyamba:
“Miliri idzafika [pa Babulo Wamkulu]. Miliri yakeyo ndiyo imfa, kulira, ndi njala. Ndipo adzanyekeratu ndi moto chifukwa Yehova Mulungu, amene anamuweruza, ndi wamphamvu.”—Chivumbulutso 18:2, 8.
Kukwaniritsidwa kwake: Baibulo limasonyeza kuti Mulungu anasankha nthawi yoti adzachititse maboma apadziko lapansi kuukira Babulo Wamkulu n’kumuwononga. Limanena kuti mabomawa ‘adzamusakaza ndi kumusiya wamaliseche ndipo adzadya minofu yake.’ (Chivumbulutso 17:16) Zimenezi zikutanthauza kuti mabomawo adzaonetsa poyera zinthu zochititsa manyazi zimene huleli limachita ndipo adzalilanda chuma chake. Babulo Wamkulu adzawonongedwa mofulumira ndipo sipadzatsala chilichonse chosonyeza kuti analipo.—Chivumbulutso 18:21.
Nthawi imeneyo mabomawa azidzaona ngati iwowo aganiza okha zowononga Babulo Wamkulu. Koma zimene zidzachitike n’zimene zidzasonyeze kuti Mulungu ndi amene wachititsa kuti Babulo Wamkulu awonongedwe. Ponena za kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu, Baibulo limati, Mulungu adzaika ‘izi [maganizo owononga Babulo Wamkulu] m’mitima yawo [maboma] kuti achite monga mwa maganizo ake.’—Chivumbulutso 17:17.
Ulosi wachiwiri:
“M’masiku a mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu. . . . Ufumuwo . . . udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, [maboma a anthu] ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.”—Danieli 2:44.
Kukwaniritsidwa kwake: Mulungu akadzathana ndi chipembedzo chonyenga, adzawononganso mabungwe onse andale, amalonda komanso anthu onse ochita zoipa. (Miyambo 2:22; Chivumbulutso 19:17, 18) Mofanana ndi mwininyumba amene akuchotsa walendi woipa, Mulungu adzawononga anthu “amene akuwononga dziko lapansi.” Adzawononga anthu onse omwe amachita makhalidwe oipa monga chiwawa komanso chiwerewere.—Chivumbulutso 11:18; Aroma 1:18, 26-29.
Ndiye kodi ndani amene adzapulumuke? Baibulo limayankha kuti: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—Salimo 37:11; 72:7.
Kodi pali zifukwa zokhulupirira maulosi a m’Baibulo? Kodi pali zifukwa zomveka zokhulupirira kuti Mulungu adzathetsadi mavuto komanso zoipa zonse ndiponso kuti adzapulumutsa anthu olungama? Inde zilipo.
Maulosi a M’Baibulo Ndi Odalirika
A Mboni za Yehova amakhulupirira kuti Yehova Mulungu ndi amene analemba Baibulo komanso kuti adzachita zonse zimene analonjeza. (2 Timoteyo 3:16) Kodi pali chifukwa chokhulupirira zimenezi?
Tiyerekeze kuti muli ndi mnzanu yemwe munayamba kugwirizana naye kalekale ndipo amakukondani komanso sanayambepo wakunamizani. Ngati mnzanuyo wakulonjezani kuti akuchitirani zinazake zabwino ndipo mukudziwa kuti ali ndi mphamvu zochitira zimene walonjezazo, kodi mungamukayikire? N’zachidziwikire kuti simungamukayikire. Mulungu ndi wokhulupirika ndipo amakwaniritsa zonse zimene walonjeza kuposa mnzanu aliyense amene mungakhale naye. Baibulo limati Mulungu “sanganame.”—Tito 1:2.
N’zoonadi kuti Mlengi wathu adzawononga chipembedzo chonyenga, maboma opondereza komanso amalonda omwe amadyera anthu masuku pamutu. Kodi mungafune kudziwa zina zimene zidzachitike Mulungu akadzachita zimenezi? M’magazini yotsatira mudzakhala nkhani yomalizira ya nkhani zimenezi ndipo idzafotokoza zimene zidzachitike.