Bakha Wam’madzi Wolira Mochititsa Chidwi
ANTHU ambiri omwe anaonapo bakha wam’madzi wotchedwa common loon amakumbukira kulira kwake kochititsa chidwi.a Abakhawa amapezeka kwambiri kunyanja komanso m’mitsinje ya ku Canada, Europe ndi kumpoto kwa dziko la United States.
Bakha ameneyu ndi wokongola kwambiri ndipo ndi chizindikiro choimira dera la Minnesota, ku United States komanso ali pandalama yachitsulo ya ku Canada. Bakhayu amakonda kusamukira m’madera ena ndipo m’nyengo yozizira, amapita ku madera a m’mphepete mwanyanja kum’mwera kwa dziko la United States. Komano n’chifukwa chiyani anthu amakonda kulira kwa bakha ameneyu?
Mmene Amalirira
Bakhayu amalira mosiyanasiyana. Mwachitsanzo, madzulo kapena usiku amalira momvetsa chisoni ndipo kulira kwake kumamveka patali kwambiri. Amaliranso mwamtundu wina akamaitana anzake kapena ana ake. Abakhawa akamauluka amaliranso mwamtundu wina pofuna kuchenjezana.
Abakha aamuna okha amaliranso mwamtundu wina. Magazini ina inanena kuti “n’kutheka kuti amalira chonchi pofuna kuteteza dera lawo.” Magaziniyi inanenanso kuti: “Bakha aliyense wamwamuna amalira mosiyana ndi abakha ena ndipo bakha wamkulu amaliranso ndi mawu amphamvu kwambiri. Komanso bakha wamwamuna akasamukira dera lina amasinthanso kaliridwe kake ndipo amayesetsa kuti kasakhale kofanana ndi mmene ankalirira ali kudera lina.”—BirdWatch Canada.
Mmene Amaonekera
Bakha ameneyu amakhala ndi mutu wakuda wooneka monyezimira. Maso ake amakhala ofiira ndipo ali ndi mlomo wakuda wosongoka. Komanso m’nyengo iliyonse bakhayu amasintha mmene amaonekera.
Chifukwa chakuti abakhawa ali ndi mapazi ophwatalala, amadziwa kwambiri kusambira komanso amatha kugwira nsomba ndi zakudya zina mosavuta. Bakha ameneyu amatha kumira m’madzi akuya mwina mamita 60 ndipo nthawi zina amatha kukhala pansi pa madzi kwa mphindi zingapo.
Koma bakhayu amavutika akafuna kuuluka kapena kutera m’madzi. Mwachitsanzo, akafuna kuuluka amafunika malo aakulu oti athamange kaye asanauluke. Amayamba kaye kukupiza mapiko kwinaku akuthamanga kwa mamita angapo n’cholinga choti auluke bwino. N’chifukwa chake abakhawa amapezeka kwambiri m’nyanja zikuluzikulu. Komanso akamatera amauluka ndi liwiro, miyendo yake ataitambasulira m’mbuyo. Zimenezi zimachititsa kuti atere pamadzi ndi mimba n’kudzikhwekhwereza mpaka pamene akaimirepo.
Ngakhale kuti abakhawa amadziwa kusambira kwambiri, amavutika kuima komanso kuyenda chifukwa choti miyendo yawo ili kumbuyo pang’ono. N’chifukwa chake amamanga zisa zawo pafupi ndi madzi kuti asamavutike kuyenda.
Bakha wamkazi akaikira mazira, nthawi zambiri bakha wamwamuna ndi wamkazi amathandizana kufungatira. Nthawi zambiri mazirawo amakhala awiri ndipo amaoneka agirini, a timawangamawanga takuda. Kawirikawiri amaswa pakatha masiku 29. Anapiye ake amayamba kusambira okha kapena kumira m’madzi pakangotha masiku awiri. Akatopa amangokwera pamsana pa makolo awo. Anapiyewo akatha miyezi iwiri kapena itatu amatha kuuluka bwinobwino ndipo amasiyana ndi makolo awo.
Abakhawa amadyedwa ndi mbalame zikuluzikulu monga ziombankhanga komanso tinyama tina. Koma mdani wamkulu wa abakhawa ndi anthu. Mwachitsanzo abakhawa amafa chifukwa cha poizoni wochokera ku tizitsulo timene amatimangirira ku mbedza kuti imire m’madzi komanso mafuta amene ataikira m’madzi. Ndiponso poizoni amene amabwera ndi mvula amapha nsomba zimene abakhawa amadya. Komanso zisa zawo zimakokoloka ndi mafunde amene amachitika maboti akamayenda. Kuwonjezera pamenepo, anthu akayamba kumanga nyumba m’mphepete mwanyanja zimapangitsa kuti abakhawa azisowa koikira mazira.
Ngakhale zili choncho, abakhawa alipo ambiri ndithu. Sitikukayika kuti anthu amene amakonda mbalame apitirizabe kusangalala ndi abakha okongola komanso olira mochititsa chidwi amenewa.
a Abakha amenewa amatchedwanso great northern diver komanso great northern loon.
Page 16, loon landing: Spectrumphotofile; page 17, loon chick: © All Canada Photos/SuperStock; loon vocalizing: © Roberta Olenick/age fotostock