Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g16 No. 1 tsamba 12-13
  • Dziko la Liechtenstein

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko la Liechtenstein
  • Galamukani!—2016
Galamukani!—2016
g16 No. 1 tsamba 12-13
Mlatho wamatabwa wokhala ndi denga wa ku Liechtenstein

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Liechtenstein

Mapu a dziko la Liechtenstein komanso malire a dziko la Switzerland komanso Austria

DZIKOLI lili m’gulu la mayiko aang’ono kwambiri padziko lonse ndipo lili m’chigawo cha mapiri pakati pa dziko la Switzerland ndi Austria. Anthu a mitundu yosiyanasiyana monga Aselote, Alatiyani, Aroma komanso Alemani akhala m’dzikoli kwa zaka zambiri. Koma panopa Alemani ndi amene alipo ochuluka kwambiri, ndipo akhala m’dzikoli kwa zaka pafupifupi 1,500.

Chiyankhulo chachikulu cha m’dzikoli ndi Chijeremani koma anthu amayankhulanso mosiyanasiyana malinga ndi madera. M’dzikoli anthu amakonda kudya chakudya china chotchedwa Tüarka-Rebel. Chakudya chimenechi chimapangidwa kuchokera ku chimanga. Amakondanso chakudya china chotchedwa Käsknöpfle chomwe amachiphika posakaniza tchizi ndi zakudya zinazake zopangidwa ndi tirigu.

Mitundu iwiri ya zakudya za anthu a ku Liechtenstein

Käsknöpfle

Mayi komanso kamtsikana atavala zovala zachikhalidwe za ku Liechtenstein

Zovala zachikhalidwe

Anthu ochokera m’mayiko ena amakonda kupita kudzikoli kukaona malo chifukwa choti lokongola kwambiri. Alendowa amaona zigwa zokongola, minda ya mpesa, zomera za mitundu yosiyanasiyana komanso mapiri okongola omwe amaoneka oyera chifukwa kumagwa chisanu. Mwachitsanzo, ngakhale kuti dzikoli ndi laling’ono kwambiri, muli mitundu pafupifupi 50 ya maluwa am’tchire okongola kwambiri. M’dzikoli mulinso malo osungira zinthu zakale, malo ochitira masewero komanso malo ambiri opangira vinyo. Chifukwa cha zimenezi, alendo amabwera m’dzikoli m’nthawi yotentha ngakhalenso yozizira.

M’dzikoli mwakhala muli a Mboni za Yehova kuyambira m’ma 1920. Panopo m’dzikoli muli a Mboni za Yehova pafupifupi 90 ndipo amaphunzira Baibulo ndi anthu a m’dzikolo komanso alendo ochokera m’mayiko ena.

Buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? limapezeka m’Chijeremani chomwe ndi chiyankhulo chachikulu m’dziko la Liechtenstein. Bukuli likupezekanso pawebusaiti ya www.jw.org.

MFUNDO ZACHIDULE

  • Chiwerengero cha anthu: 37,000

  • Likulu: Vaduz

  • Chinenero chachikulu: Chijeremani

  • Chipembedzo: Anthu ambiri ndi Akatolika

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

Kodi ndi ziganizo ziti zimene zikunena zoona zokhudza dziko la Liechtenstein?

  1. Ndi limodzi mwa mayiko awiri padziko lonse amene ali pakatikati pa mayiko omwe ali kutali ndi Nyanja yaikulu.

  2. Kumapezeka mitundu ya nyama za m’gulu loyamwitsa yopitirira 50.

  3. Kumapezeka mitundu ya zomera pafupifupi 1,600.

  4. Dzikoli lilibe asilikali.

Yankho: Ziganizo zonsezi ndi zoona.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena