Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Zinthu Padzikoli Zafika Poipa Kwambiri Kapena Ayi?
    Galamukani!—2017 | No. 6
    • Wotchi Yosonyeza Nthawi ya Kutha kwa Dziko

      NKHANI YA PACHIKUTO | KODI ZINTHU PADZIKOLI ZAFIKA POIPA KWAMBIRI

      Kodi Zinthu Padzikoli Zafika Poipa Kwambiri Kapena Ayi?

      PAMENE chaka cha 2017 chinkayamba, gulu la akatswiri a sayansi linapereka uthenga wochititsa mantha. M’mwezi wa January, a sayansiwa analengeza kuti dziko lapansili latsala pang’ono kutha. Akatswiriwa ali ndi wotchi yongoyerekezera yosonyeza nthawi imene yatsala kuti dzikoli lithe ndipo anasunthira kutsogolo muvi wa maminitsi wa wotchiyi ndi masekondi 30. Wotchiyi ataikokera, inayamba kusonyeza kuti kwatsala 2 minitsi ndi hafu kuti nthawi ikwane 12 koloko ya usiku yomwe amati ikuimira nthawi yomwe dzikoli lidzathe. Panopa nthawiyi imaoneka yaifupi kwambiri poyerekeza ndi mmene inkaonekera chikhazikitsireni wotchiyi zaka zoposa 60 zapitazo.

      Akatswiri asayansiwa akuganiza kuti mu 2018 adzaonenso kuti nthawi yoti dzikoli lithe yayandikira bwanji. Koma kodi wotchiyo idzawathandizadi kudziwa kuti dzikoli litha liti? Inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinthu padzikoli zafikiratu poipa kwambiri? Mwina mukuona kuti funsoli ndi lovuta kuyankha. Koma si inu nokha, ngakhalenso akatswiri ali ndi maganizo osiyana pa nkhaniyi chifukwa si onse omwe amakhulupirira kuti nthawi ina dzikoli lidzatha.

      Pali anthu enanso ambiri omwe amaona kuti zinthu zidzakhala bwino mtsogolo. Anthuwa amanena kuti pali umboni woti anthufe komanso dzikoli lidzakhalapobe mpaka kalekale. Amanenanso kuti pa nthawiyo moyo wa anthu udzakhala wabwino kwambiri. Kodi umboni wa anthuwa ndi womveka? Kodi zinthu padzikoli zafikadi poipa kwambiri?

      Magazini ina inanena kuti: “Wotchi Yosonyeza Nthawi ya Kutha kwa Dziko ndi yongoyerekezera ndipo inapangidwa ndi akatswiri asayansi a m’mayiko osiyanasiyana. Akatswiriwa anapanga wotchiyi n’cholinga chofuna kusonyeza nthawi yomwe yatsala kuti dzikoli liwonongeke chifukwa cha zochita za anthu. Chinthu choyambirira chomwe amaona kuti chingadzawononge dzikoli ndi mabomba a nyukiliya. Palinso zinthu zina zomwe anthu amachita kaya mwadala kapena mosadziwa zomwe zikuika dzikoli komanso moyo wa anthu pangozi. Zinthuzi ndi monga kusintha kwa nyengo, njira zamakono za ulimi ndi zachipatala komanso luso la zopangapanga.”​—Bulletin of the Atomic Scientists.

  • Kufufuza Mayankho
    Galamukani!—2017 | No. 6
    • NKHANI YA PACHIKUTO | KODI ZINTHU PADZIKOLI ZAFIKA POIPA KWAMBIRI

      Kufufuza Mayankho

      NGATI mumachita mantha mukawerenga kapena kumva nkhani inayake yoopsa, dziwani kuti si inu nokha. Mu 2014, a Barack Obama omwe anali mtsogoleri wa dziko la United States ananena kuti nkhani zochititsa mantha zomwe zikumalembedwa m’manyuzi, zikuchititsa anthu kuona kuti dzikoli lafika poipa kwambiri moti palibenso zomwe anthu angachite.

      Komabe patangopita nthawi yochepa atalankhula mawuwa, mtsogoleriyu anafotokoza njira zatsopano zofuna kuthana ndi mavuto omwe akuchitika padzikoli. Mtsogoleriyu anayamikira zimene mayiko ena akuyesetsa kuchita pothana ndi mavutowa. Ananenanso kuti akutsimikiza kuti zinthu ziyambanso kuyenda bwino. Choncho tingati mtsogoleriyu anasonyeza kuti zinthu zomwe anthu akuyesetsa kuchita, zingateteze dzikoli n’kulipangitsa kukhala malo abwino kwambiri.

      Ambiri amagwirizana ndi zomwe a Obama ananena. Mwachitsanzo pali anthu ambiri omwe amakhulupirira kuti njira za sayansi komanso kupita patsogolo kwa luso la zopangapanga, kungathandize kuthetsa mavuto omwe akuchitika padzikoli. Katswiri wina wa luso la zopangapanga ananena motsimikiza kuti podzafika chaka cha 2030, “luso la zopangapanga lidzakhala litafika patali ndipo pofika mu 2045 zinthu zidzakhala bwino kwambiri.” Katswiriyu ananenanso kuti: “Panopa tikuchita bwino ndithu. Ngakhale kuti pali mavuto ena ndi ena koma sikuti n’zochita kudetsa nkhawa. Njira zolimbana ndi mavutowa zikuyenda bwino kwambiri.”

      Kodi zinthu zaipa kufika pati? Kodi ndi zoona kuti dzikoli litha posachedwa? Ngakhale kuti asayansi ndi andale ena akunena kuti zinthu zikhala bwino, palinso anthu ambiri omwe akukayikira ngati zinthu zingakhaledi bwino kutsogoloku. N’chifukwa chiyani zili choncho?

      Bomba la Nyukiliya laphulika

      ZIDA ZA NKHONDO ZOMWE ZINGAPHE ANTHU AMBIRI. Bungwe la United Nations komanso mabungwe ena akhala akuyesetsa kuthetsa zida za nyukiliya, koma izi sizikuthandiza. Pali atsogoleri a mayiko ena omwe akukana kutsatira malamulo othetsa zidazi. Mayiko omwe kuchokera kalekale ankadziwika kuti ali ndi zida za nyukiliya, panopo akuziwonjezera mphamvu ndipo akupanganso zina zoopsa kwambiri kuposa zakalezo. Mayiko ena omwe poyamba analibe zida zoopsa, panopa ayamba kusunga zida zoopsa zomwe zingaphe anthu ambiri nthawi imodzi.

      Mayiko akusunga zida zoopsa kwambiri pokonzekera kuti nthawi ina kutha kudzabuka nkhondo ya nyukiliya. Zimenezi zikuchititsa kuti anthu padzikoli azikhala mwamantha kwambiri ngakhale pamene zikuoneka ngati zinthu ziliko bwino. Magazini ina inachenjezanso kuti: “Chodetsanso nkhawa kwambiri ndi zida za nkhondo zoopsa kwambiri zomwe zinapangidwa kuti zizigwira ntchito pazokha popanda kuwongoleredwa ndi anthu.”​—Bulletin of the Atomic Scientists.

      Munthu amugoneka kuchipatala

      MATENDA. Asayansi sangatilonjeze zoti tingakhale ndi moyo wathanzi nthawi zonse. Zinthu zodetsa nkhawa monga kuthamanga kwa magazi, kunenepa kwambiri, kuwonongeka kwa mpweya komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, zikuwonjezeka kwambiri. Anthu ambiri akumwalira ndi matenda a khansa, a mtima komanso a shuga. Anthu enanso ambiri akulumala chifukwa cha matenda ena kuphatizapo matenda a maganizo. Zaka zaposachedwa kwabukanso matenda oopsa ngati a Ebola komanso a Zika. Koma zoona zake n’zakuti, anthu sangathe kuthetsa matenda ndipo palibe chiyembekezo choti adzawathetsa.

      Kuwonongeka kwa mphweya komanso madzi

      KUWONONGA CHILENGEDWE. Mafakitale akupitirizabe kuwononga mpweya. Anthu ambirimbiri akumwalira chaka chilichonse chifukwa chopuma mpweya woipa.

      Anthu komanso mabungwe a boma akupitirizabe kutaya zonyansa za kuchipatala, zinthu zapulasitiki ndi zinyalala zina m’nyanja. Buku lina linanena kuti: “Zinthu zomwe amatayazi zimakhala ndi poizoni ndipo zimawononga zomera ndi zamoyo zina zam’madzi. Komanso anthu omwe amadya zomera komanso zamoyo zam’madzizi amaika moyo wawo pangozi.”​—Encyclopedia of Marine Science.

      Madzi abwino ayamba kutha. Katswiri wina wa ku Britain amene amalemba mabuku asayansi dzina lake Robin McKie, anachenjeza kuti: “Madzi abwino ayamba kusowa ndipo kutsogoloku vutoli lidzakhala la padziko lonse.” Akatswiri andale amavomereza kuti vuto la kusowa kwa madzi, linayambitsidwa ndi anthu ndipo likuika moyo wa anthu ambiri pangozi.

      Mphepo ya mkuntho

      NGOZI ZADZIDZIDZI. Mphepo zamkuntho ndi zivomerezi zikuchititsa kugumuka kwa nthaka, kusefukira kwa madzi komanso ngozi zina zadzidzidzi. Panopo anthu akufa kapena kuvutika kwambiri ndi ngozi zamtunduwu. Kafukufuku amene bungwe lina la ku United States loona za maulendo a pandege ndi sayansi ya mlengalenga linachita, anapeza kuti kutsogoloku kukhala kukuchitika mphepo zamkuntho, chilala komanso kusefukira kwa madzi. Ndipo ananena kuti zikhala zoopsa kwambiri kuposa panopa. Kodi ndiye kuti anthu adzatha onse padzikoli chifukwa cha ngozi zadzidzidzi zimenezi?

      N’kutheka kuti mukudziwa zinthu zinanso zomwe zikuika moyo wathu pangozi. Komabe kungoona zinthu zoopsa zomwe zikuchitika panopo si kungakuthandizeni kudziwa zamtsogolo. Ndipo ena anganene kuti zimenezi n’zofanana ndi kumvetsera zolankhula za akatswiri asayansi ndi a ndale. Koma monga mmene tanenera m’nkhani yoyamba ija, anthu ambiri apeza mayankho okhutiritsa a mafunso ofuna kudziwa za tsogolo la dzikoli komanso chifukwa chake padzikoli pakuchitika zinthu zoopsa chonchi. Kodi mayankho a mafunsowa amapezeka kuti?

  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?
    Galamukani!—2017 | No. 6
    • Munthu ali m’dziko lapansi latsopano

      Dzikoli silidzawonongeka ndi zochita za anthu chifukwa Mulungu akulonjeza kuti zinthu zidzakhala bwino kwambiri mtsogolo

      NKHANI YA PACHIKUTO | KODI ZINTHU PADZIKOLI ZAFIKA POIPA KWAMBIRI

      Kodi Baibulo Limanena Zotani?

      ZAKA zambirimbiri m’mbuyomo, Baibulo linaneneratu za zinthu zoipa zomwe zikuchitika masiku ano. Koma chosangalatsa kwambiri n’chakuti linaneneratunso kuti anthu adzakhala ndi moyo wabwino kwambiri mtsogolo. Zomwe Baibulo linanenazi tiyenera kuzikhulupirira ndi mtima wonse chifukwa maulosi ake ambiri akhala akukwaniritsidwa mochititsa chidwi kwambiri.

      Mwachitsanzo, taganizirani za maulosi awa:

      • “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina. Kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo osiyanasiyana.”​—Mateyu 24:7.

      • “Koma dziwa kuti, masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, osakonda achibale awo, osafuna kugwirizana ndi anzawo, onenera anzawo zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, achiwembu, osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.”​—2 Timoteyo 3:1-4.

      Zinthu zoipa zomwe anthu akuona masiku ano, zikukwaniritsa zomwe Baibulo linaneneratu kalekale. Zinthu zafikadi poipa kwambiri padzikoli moti anthu sangathe kuthetsa zomwe zikuchitikazi. Baibulo limanena kuti anthu alibe mphamvu komanso nzeru zoti angathetsere zinthu zoipazi. Malemba awa akufotokoza bwino zimenezi:

      • “Pali njira yooneka ngati yowongoka kwa munthu, koma mapeto ake ndi imfa.”​—Miyambo 14:12.

      • “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.”​—Mlaliki 8:9.

      • “Munthu . . . alibe ulamuliro wowongolera njira ya moyo wake.”​—Yeremiya 10:23.

      Ngati anthu atapitiriza kuchita zilizonse zomwe akufuna, zinthu zikhoza kufikadi poipa kwambiri. Koma si kuti zochita za anthuzi zingadzapangitse kuti dzikoli lithe. N’chifukwa chiyani tikutero? Baibulo limanena kuti:

      • Mulungu ‘anakhazikitsa dziko lapansi pamaziko olimba. Silidzagwedezeka mpaka kalekale, mpaka muyaya.’​—Salimo 104:5.

      • “M’badwo umapita ndipo m’badwo wina umabwera, koma dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale.”​—Mlaliki 1:4.

      • “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”​—Salimo 37:29.

      • “Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.”​—Salimo 72:16.

      Malemba a m’Baibulowa akutithandiza kupeza mayankho. Si kuti kuwonongeka kwa chilengedwe, kusowa kwa chakudya ndi madzi komanso kuchuluka kwa matenda, zingadzafike poipa mpaka anthu onse kutha padzikoli. Dzikoli silidzatha ndi nkhondo ya mabomba a nyukiliya. Tikutero chifukwa tsogolo la dzikoli lili m’manja mwa Mulungu. Mulungu anapatsa anthu ufulu wopanga zomwe akufuna. Komabe, anthuwa adzakolola mogwirizana ndi zochita zawo. (Agalatiya 6:7) Dzikoli silili ngati galimoto yopanda mabuleki yomwe ikuthamanga kwambiri moti dalaivala wake akulephera kuiwongolera. Mulungu anaikira anthu malire ndipo sadzawalola kuwononga dzikoli mpaka kalekale.​—Salimo 83:18; Aheberi 4:13.

      Mulungu adzabweretsa “mtendere wochuluka” padzikoli. (Salimo 37:11) Nkhaniyi yangofotokoza zinthu zochepa zomwe zidzachitike mtsogolo. A Mboni za Yehova amaphunzira nkhani zambiri m’Baibulo zofotokoza zinthu zochititsa chidwi zomwe zidzachitike kutsogoloku.

      A Mboni za Yehova ndi anthu a misinkhu komanso zikhalidwe zosiyanasiyana ndipo amachokera m’mayiko osiyanasiyananso. Amapembedza Mulungu m’modzi woona ndipo Baibulo limati dzina lake ndi Yehova. A Mboniwa sachita mantha ndi zinthu zamtsogolo chifukwa Baibulo limanena kuti: “Pakuti Yehova, Mlengi wa kumwamba, Mulungu woona, amene anaumba dziko lapansi ndi kulipanga, amene analikhazikitsa mwamphamvu, amene sanalilenge popanda cholinga, amene analiumba kuti anthu akhalemo, wanena kuti: ‘Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina.’”​—Yesaya 45:18.

      M’nkhaniyi taona zomwe Baibulo limanena zokhudza tsogolo la dzikoli komanso mmene moyo wa anthu udzakhalire mtsogolo. Kuti mudziwe zambiri pa nkhaniyi, werengani mutu 5 m’kabuku kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu. Kabukuka ndi kofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova ndipo mungakapeze pa www.jw.org/ny

      Mungaonerenso vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Mulungu Analenga Dziko Lapansi? pawebusaiti ya www.jw.org/ny. (Pitani pomwe alemba kuti MABUKU > MAVIDIYO)

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena