Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yp2 mutu 24 tsamba 199-207
  • Kodi Ndingatani Makolo Anga Akamakangana?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndingatani Makolo Anga Akamakangana?
  • Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • N’chifukwa Chiyani Makolo Amakangana?
  • Zimene Mungachite
  • Zimene Simuyenera Kuchita
  • Kodi Ndizitani Makolo Anga Akamakangana?
    Galamukani!—2007
  • Kodi Ndingachitenji ngati Makolo Anga Amenyana?
    Galamukani!—1989
  • Makolo Anga Akulekana—Kodi Ndichitenji?
    Galamukani!—1990
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndidziwane Bwino Ndi Makolo Anga?
    Galamukani!—2009
Onani Zambiri
Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
yp2 mutu 24 tsamba 199-207

Mutu 24

Kodi Ndingatani Makolo Anga Akamakangana?

Kodi makolo anu amakangana inu mulipo? Ngati amatero, kodi ndi nkhani iti pa zimene zili kumanjazi, imene amakonda kukangana kawirikawiri?

□ Ndalama

□ Ntchito zapakhomo

□ Achibale

□ Inuyo

Kodi mumafuna mutawauza chiyani makolo anuwo za mmene khalidwe lawolo limakukhudzirani? Lembani zimenezo m’munsimu.

․․․․․

MAKOLO anu akamakangana, n’zosakayikitsa kuti zimenezo zimakusokonezani maganizo. Izi zili choncho chifukwa chakuti mumawakonda ndiponso mumawadalira kuti akuthandizeni. Mwina mungavomerezane ndi zimene mtsikana wina dzina lake Marie ananena. Iye anati: “Zimandivuta kulemekeza makolo anga ndikamaona kuti iwowo salemekezana.”

Mukaona makolo anu akukangana mumazindikira kuti nawonso si angwiro, ndipo zimenezo zingakukhumudwitseni kwambiri ndiponso kukuchititsani mantha. Ngati makolowo amakangana kawirikawiri kapena ngati amakangana kwambiri, mwina mungayambe kuda nkhawa kuti banja lawo litha. Marie anati: “Ndikamaona makolo anga akukangana, ndimaganiza kuti banja lawo litha ndipo ine ndidzafunika kusankha kuti ndizikhala ndi ndani. Ndimadanso nkhawa kuti mwina ndingadzasiyane ndi azibale anga.”

N’chifukwa chiyani makolo amakangana, ndipo mungatani iwo akamakangana?

N’chifukwa Chiyani Makolo Amakangana?

Nthawi zambiri makolo anuwo ayenera kuti ‘amalolerana wina ndi mnzake m’chikondi.’ (Aefeso 4:2) Komabe, Baibulo limati: “Onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Makolo anu si anthu angwiro. Choncho, musamadabwe nthawi zina akamakwiyirana mpaka kufika pokangana.

Komanso kumbukirani kuti tikukhala “nthawi yovuta.” (2 Timoteyo 3:1) Motero, makolo amavutika kusamalira banja, kulipirira zinthu zosiyanasiyana, ndiponso chifukwa cha mavuto a kuntchito. Zimenezi zimabweretsa mavuto m’banjamo. Ndipo ngati makolo anu onse ali pantchito, nthawi zina angathe kukangana chifukwa cholephera kugawana bwino ntchito zapakhomo.

Dziwani kuti sinthawi zonse pamene banja lingathe, makolo anu akakangana. N’zosakayikitsa kuti iwo amakondanabe, ngakhale kuti angasemphane maganizo pankhani zina.

Tiyerekezere kuti mukuonera filimu ndi anzanu. Kodi nonse mungaikonde filimuyo mofanana? Ayi. Ngakhale anthu amene amagwirizana kwambiri amaonabe zinthu zina mosiyana. Zingakhalenso choncho ndi makolo anu. N’kutheka kuti iwo akufuna kupanga bajeti, koma aliyense angakhale ndi maganizo osiyana ndi a mnzake; onse akufuna kupita kutchuthi, koma ali ndi maganizo osiyana a kumene angapite; kapena onse akufuna kuti muzikhoza bwino kusukulu, koma aliyense akuganiza mosiyana za mmene angakulimbikitsireni.

Mfundo ndi yakuti, anthu ogwirizana safanana pachilichonse. N’zosatheka kuti anthu awiri amene amakondana kwambiri aziona zinthu mofanana nthawi zonse. Komabe, simungasangalale kuona makolo anu akukangana. Ndiyeno n’chiyani chimene mungachite kapena kunena, chomwe chingakuthandizeni kupirira?

Zimene Mungachite

Muziwalemekeza. Kukhala ndi makolo amene amakonda kukangana n’kosowetsa mtendere. Ndipotu makolo ndi amene amafunika kusonyeza ana awo chitsanzo chabwino. Komabe, kuwachitira mwano kungathe kungowonjezera mavuto m’banjamo. Ndipo mfundo yofunika kuikumbukira ndi yakuti, Yehova Mulungu amakulamulani kuti muziwalemekeza ndi kuwamvera, ngakhale kuti iwo amakonda kukangana.—Eksodo 20:12; Miyambo 30:17.

Koma kodi mungatani ngati makolo anuwo akukangana pankhani inayake yokhudza inuyo? Tiyerekezere kuti bambo kapena mayi anu okha ndiwo a Mboni za Yehova. Ngati mwasankha kukhala kumbali ya bambo kapena mayi anu amene ndi a Mboni za Yehova, nthawi zina m’banjamo mungabuke mavuto okhudza zimenezi. (Mateyo 10:34-37) Ngati ndi choncho, muzichita zinthu ndi “mtima wofatsa ndi mwa ulemu waukulu.” N’kutheka kuti nthawi ina m’tsogolo, bambo kapena mayi anuwo adzayamba kuphunzira choonadi chifukwa cha chitsanzo chanu chabwino.—1 Petulo 3:15.

Musakhale kumbali iliyonse. Kodi mungatani ngati makolo anu akukukakamizani kuti mulowerere pankhani imene sikukukhudzani? Pewani kukhala kumbali iliyonse. Mwina mungawafotokozere mwaulemu kuti: “Nonsenu ndimakukondani, koma nkhani imeneyi ndi yoti muthane nayo nokha. Choncho, ine sindilowererapo.”

Lankhulani nawo. Ndi bwino kuwafotokozera mmene mikangano yawoyo imakukhudzirani. Auzeni zimenezo panthawi imene mukuona kuti iwo angakumvetsereni ndipo afotokozereni kuti mumakhumudwa ngakhalenso kuchita mantha chifukwa cha mikangano yawoyo.—Miyambo 15:23; Akolose 4:6.

Zimene Simuyenera Kuchita

Musakhale ngati ndinu nkhoswe yawo. Popeza ndinu wachinyamata, siinu woyenerera kuthetsa mikangano ya makolo anu. Tiyerekezere kuti mwakwera ndege ndipo mukumva woyendetsa ndegeyo akukangana ndi womuthandizira wake. M’pomveka kuti mungachite mantha ndi zimenezo. Koma kodi chingachitike n’chiyani ngati mungaganize zowauza zochita anthu oyendetsa ndegewo kapena kukakamira kuti muyendetse ndi inuyo?

Mofanana ndi zimenezi, kuyesa kuthetsa mikangano ya makolo anu kungathe kungowonjezera mikanganoyo. Baibulo limati: “Kudzikuza kupikisanitsa; koma omwe anauzidwa uphungu ali ndi nzeru.” (Miyambo 13:10) Choncho, makolo anuwo angathetse okha mavuto awo mwa kukambirana.—Miyambo 25:9.

Musalowerere. Mkangano wa anthu awiri umasowetsa mtendere. Nanga zingakhale bwanji munthu wachitatu atalowererapo? Ngakhale kuti nkhani zina zingakuchititseni kufuna kulowererapo, dziwani kuti ndi udindo wa makolo anuwo kuthetsa mikangano yawo, osati wanu. Motero yesetsani kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti ‘muzisamala zanuzanu.’ (1 Atesalonika 4:11) Choncho musalowerere mkangano wawowo.

Musamawayambanitse. Achinyamata ena amachita kulimbikitsa makolo awo kuti azikangana. Mayi awo akawaletsa chinthu chinachake, amayesetsa kunyengerera bambo awo kuti awaloleze chinthucho. Ngakhale kuti kuchita zinthu motere kungakuthandizeni kupeza zimene mukufuna panthawiyo, koma m’kupita kwanthawi zingangowonjezera mavuto panyumbapo.

Musalole kuti khalidwe lawolo lisokoneze khalidwe lanu. Mnyamata wina dzina lake Peter anazindikira kuti zimene ankachitira bambo ake, omwe anali ankhanza, zinali zosagwirizana ndi makhalidwe amene Akhristu amafunika kukhala nawo. Iye anati: “Ndinkafuna kuwakhaulitsa. Ndinkadana nawo kwambiri chifukwa choti ankachitira nkhanza ineyo, mayi anga ndiponso mchemwali wanga.” Koma pasanapite nthawi yaitali, Peter analowa m’mavuto chifukwa cha zochita zakezo. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Mukakhala ndi khalidwe loipa, mungathe kungowonjezera mavuto m’banja mwanu.—Agalatiya 6:7.

Pamfundo zimene taonazi, lembani pamzere uwu mfundo imene mukufuna kuigwiritsa ntchito kwambiri. ․․․․․

N’zodziwikiratu kuti simungathetse mikangano ya makolo anu. Komabe, dziwani kuti Yehova angakuthandizeni kupirira mavuto amene amabwera chifukwa cha kukangana kwawoko.—Afilipi 4:6, 7; 1 Petulo 5:7.

Yesetsani kugwiritsa ntchito mfundo zimene taonazi. Mwina, m’kupita kwanthawi zimenezo zingalimbikitse makolo anuwo kuyesetsa kuthetsa mavuto awo. Mwinanso angadzafike posiyiratu kukanganako.

M’MUTU WOTSATIRA

Kodi mukuleredwa ndi bambo kapena mayi anu okha? Ngati zili choncho, kodi mungatani kuti muthane ndi mavuto amene angakhalepo m’banja mwanumo?

LEMBA LOFUNIKA

“Nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo.”—Akolose 4:6.

MFUNDO YOTHANDIZA

Ngati makolo anu amakonda kukangana kwambiri, auzeni mwaulemu kuti angachite bwino kupempha anthu ena kuti awathandize.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Anthu amene amakondana kwambiri amatha kukanganabe nthawi zina.

ZOTI NDICHITE

Makolo anga akayamba kukangana ndizichita izi: ․․․․․

Makolo anga atandipempha kuti ndilowerere pamkangano wawo, ndingawauze izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

● N’chifukwa chiyani makolo ena amakangana?

● Kodi n’chifukwa chiyani simungaimbidwe mlandu chifukwa cha mikangano ya makolo anu?

● Kodi mungaphunzirepo chiyani poona khalidwe la makolo anu?

[Mawu Otsindika patsamba 201]

“Kudziwa kuti makolo anga si anthu angwiro ndiponso kuti iwo amakumana ndi mavuto ngati ineyo, kwandithandiza kupirira iwowo akamakangana.”—Anatero Kathy

[Bokosi/Chithunzi pamasamba 206, 207]

Ndingatani Ngati Makolo Anga Analekana?

Ngati makolo anu analekana, kodi mungatani kuti muzichita zinthu mwanzeru ngakhale kuti zimene anachitazo zimakukhumudwitsani kwambiri? Taonani mfundo zotsatirazi:

● Musayembekezere zinthu zosatheka. Mwachibadwa, mungakhale ndi maganizo oti muthandize makolo anuwo kuti abwererane. Mtsikana wina dzina lake Anne anati: “Makolo anga atalekana, nthawi zina ankatitenga kupita koyenda. Ine ndi mkulu wanga tinkanong’onezana kuti, ‘Tiyeko titsogole, tiwasiye awa kuti azikambirana zawo.’ Koma zimenezo sizinathandize, chifukwa sanabwererane.”

Lemba la Miyambo 13:12 limati: “Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima.” Kudziwa kuti simungapangire makolo anuwo zochita, kungakuthandizeni kuti musamakhumudwe kwambiri ndi zimene iwo amachita. Kumbukirani kuti siinu amene munachititsa kuti iwo alekane, ndipo n’zodziwikiratu kuti si udindo wanu kuwathandiza kuti abwererane.—Miyambo 26:17.

● Musadane nawo. Kukwiyira bambo kapena mayi anu, kapena onse awiri kungakulowetseni m’mavuto amene mungafunike kulimbana nawo kwanthawi yaitali. Mnyamata wina dzina lake Tom amakumbukira mmene ankamvera pamene anali ndi zaka 12. Iye anati: “Ndinayamba kuwakwiyira kwambiri bambo anga. Sindikufuna kunena kuti ndinkadana nawo, koma sindinkasangalala nawo m’pang’ono pomwe. Ndinkaona kuti satikonda chifukwa choti anangotisiya ndi mayi okha.”

Komatu, makolo akalekana sizitanthauza kuti mmodzi pa awiriwo ndi wabwino kwambiri ndipo winayo ndi woipitsitsa. Dziwani kuti makolo anuwo sanakuuzeni zonse zokhudza ukwati wawo kapena zifukwa zonse zimene analekanirana. Ndipo n’kutheka kuti nawonso sakumvetsetsa zifukwa zake. Choncho, pewani kuwaweruza chifukwa chakuti simukudziwa zifukwa zonse zimene zinachititsa kuti alekane. (Miyambo 18:13) N’zoona kuti zingakuvuteni kuti musawakwiyire, ndipo sizingakhale zachilendo ngati mutamawakwiyira kwambiri nthawi zina. Koma, khalidwe lanu lingawonongeke kwambiri mukapitirizabe kuwakwiyira ndiponso kukhala ndi mtima wofuna kuwabwezera. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo.”—Salmo 37:8.

● Onani zinthu moyenera. Ngakhale kuti achinyamata ena amadana ndi bambo kapena mayi amene anawasiya, ena amaona makolo oterewa ngati chitsanzo chabwino choti atengere. Mwachitsanzo, bambo a mnyamata wina anali chidakwa komanso okonda akazi ndipo ankasiya mkazi wawo mobwerezabwereza mpaka anafika pothetsa banjalo. Koma mnyamatayu amakumbukira kuti ngakhale kuti bambo akewo ankachita zimenezi, iye ankawaona ngati munthu woyenera kumutsanzira.

Maganizo olakwika ngati amenewa si achilendo. M’dziko lina, achinyamata pafupifupi 90 pa 100 alionse amene banja la makolo awo linatha, amakhala ndi mayi awo ndipo kwa bambo awo amangopita kukacheza. Motero, nthawi zambiri mayi ndi amene amakhala ndi udindo wosamalira ndi kulangiza anawo. Ngakhale kuti abambo amapereka ndalama zothandizira anawo, amayi ambiri omwe banja lawo linatha amakhala m’mavuto a zachuma, pamene abambowo zinthu zimawayendera bwino. Chifukwa cha zimenezi, anawo akapita kukaona bambo awo, amapatsidwa mphatso zambiri ndiponso amasangalala kwambiri. Koma akakhala ndi amayi awo, amakhala ndi ndalama zochepa ndiponso amapatsidwa malamulo ambirimbiri. N’zomvetsa chisoni kuti achinyamata ena asiya kukhala ndi mayi awo achikhristu n’cholinga choti azikhala ndi bambo awo osakhulupirira omwe ndi olemera ndiponso olekerera kwambiri. Achinyamata enanso amasankha kukhala ndi mayi awo omwe si achikhristu pazifukwa ngati zomwezi.—Miyambo 19:4.

Ngati mukufuna kuchita zinthu ngati zimenezi, ganizirani mofatsa zolinga zanu. Musaiwale kuti mumafunika kutsogoleredwa ndiponso kulangizidwa bwino. Palibe chinthu china chofunika kwambiri kuposa malangizo abwino amene makolo angakupatseni, chifukwa angakuthandizeni kukhala wamakhalidwe abwino komanso moyo wabwino.—Miyambo 4:13.

[Chithunzi pamasamba 202, 203]

Wachinyamata amene amauza makolo ake mmene angathetsere mikangano yawo, ali ngati munthu amene wakwera ndege, n’kumauza zochita anthu oyendetsa ndegeyo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena