Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Ndafika Poti N’kukhala ndi Chibwenzi?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
    • Mutu 1

      Kodi Ndafika Poti N’kukhala ndi Chibwenzi?

      “N’zovuta kwambiri kukhala wopanda chibwenzi, komanso masiku ano kuli tianyamata tambiri tooneka bwino.”—Anatero Whitney.

      “Tiatsikana tina timachita kundifunsira tokha, ndipo n’zovuta kukana. Koma ndikudziwiratu zomwe makolo anga anganene nditawauza zimenezi.”—Anatero Phillip.

      MAGANIZO ofuna kukhala ndi munthu winawake wapamtima amene ungamamukonde, komanso amene angamakukonde, angakhale amphamvu kwambiri ngakhale uli wamng’ono. Mtsikana wina dzina lake Jenifer anati: “Ndinayamba kufuna kwambiri kukhala ndi chibwenzi ndili ndi zaka 11.” Mtsikana winanso dzina lake Brittany anati: “Kusukulu, umadzimva wotsalira ngati ulibe chibwenzi. Kaya munthuyo akhale wotani, bola chibwenzi basi.”

      Nanga bwanji inuyo? Kodi mwafika poti n’kukhala ndi chibwenzi? Kuti mudziwe yankho la funso limeneli, choyamba tiyeni tikambirane funso lofunika kwambiri ili:

      Kodi “Kukhala ndi Chibwenzi” N’kutani?

      Chongani yankho lanu pamafunso otsatirawa:

      Mumakonda kuyenda ndi winawake amene si mnyamata kapena mtsikana mnzanu. Kodi ndiye kuti muli pachibwenzi?

      □ Inde

      □ Ayi

      Mwakopeka ndi munthu winawake amene si mnyamata kapena mtsikana mnzanu ndipo kangapo patsiku, mumalankhulana kapena kutumizirana mauthenga pafoni. Kodi ndiye kuti muli pachibwenzi?

      □ Inde

      □ Ayi

      Nthawi zonse mukakhala pagulu ndi anzanu, mumakhala pamodzi ndi munthu yemweyemweyo, koma si mnyamata kapena mtsikana mnzanu. Kodi ndiye kuti muli pachibwenzi?

      □ Inde

      □ Ayi

      N’zosakayikitsa kuti simunavutike kuyankha funso loyambalo, koma mwina munaganizira kaye mozama musanayankhe mafunso enawo. Kodi kukhala ndi chibwenzi n’kutani kwenikweni? Kukhala ndi chibwenzi kumatanthauza kucheza m’njira ina iliyonse ndi munthu mmodzi amene mwakopeka naye ndipo nayenso wakopeka nanu. Choncho yankho la mafunso onse atatu amene ali pamwambawa ndi lakuti inde. Ngati mumalankhulana nthawi zonse, kaya pafoni kapena pamasom’pamaso, kaya poyera kapena mobisa, ndipo inuyo ndi mnzanuyo mumadziwa kuti mumakondana m’njira yodziwa awirinu, ndiye kuti muli pachibwenzi. Koma kodi mwafika poti n’kuchita zimenezi? Kuganizira mafunso atatu otsatirawa kungakuthandizeni kupeza yankho la funsoli.

      N’chifukwa Chiyani Mukufuna Kukhala ndi Chibwenzi?

      M’madera ambiri anthu amaona kuti kukhala ndi chibwenzi ndi njira yovomerezeka yodziwirana bwino. Komatu cholinga chokhalira ndi chibwenzi chiyenera kukhala chabwino, chofuna kudziwana ngati ndinu anthu oyenerana kumanga banja.

      N’zoona kuti anzanu ena angamachite zibwenzi alibe cholinga chabwino. Mwinamwake amangosangalala kukhala ndi chibwenzi popanda cholinga chodzakwatirana. Ena amangoona chibwenzi chawocho ngati chinthu chinachake chodzitamira nacho, mwinanso ngati chikho chimene apambana pampikisano. Nthawi zambiri zibwenzi zotere sizichedwa kutha. Mtsikana wina, dzina lake Heather, anati: “Achinyamata ambiri amene amakhala ndi zibwenzi amathetsa zibwenzizo pakangotha mlungu umodzi kapena iwiri. Motero amayamba kuona chibwenzi ngati chinthu chosakhalitsa, ndipo tingati zimenezi zimawapangitsa kukhala ndi mtima wofuna kudzathetsa banja m’tsogolo, osati mtima wofuna kukhala ndi banja lolimba.”

      Dziwani kuti mukakhala pachibwenzi ndi munthu, maganizo ake onse amakhala pa inuyo. Choncho, onetsetsani kuti muli ndi cholinga chabwino mukamayamba chibwenzi. Taganizirani izi: Kodi mungamve bwanji munthu wina ataseweretsa maganizo anu ngati chidole choseweretsa ana? Mtsikana wina dzina lake Chelsea anati: “Nthawi zina ndimaganiza kuti anthu ayenera kuchita chibwenzi pofuna kungosangalala. Koma sizoona chifukwa mnzanuyo amazitenga kuti n’zenizeni.”

      Kodi Mwafika Zaka Zoti Mungakhale ndi Chibwenzi?

      Kodi mukuganiza kuti wachinyamata angakhale ndi chibwenzi ali ndi zaka zingati? ․․․․․

      Ndiyeno funsani bambo kapena mayi anu kapenanso onse pamodzi, kenaka lembani zimene akuyankheni. ․․․․․

      N’zosakayikitsa kuti zaka zimene inuyo munalemba n’zochepa kusiyana ndi zaka zimene makolo anu atchula. Kapena mwina sizinasiyane kwenikweni. Mwina muli m’gulu la achinyamata ambiri anzeru amene akudikira kuti adzakhale ndi chibwenzi akadzakula n’kufika podzidziwa bwinobwino. Izi n’zimene mtsikana wina wazaka 17, dzina lake Danielle, anaganiza kuchita. Iye anati: “Ndikakumbukira za mmene ndinkaganizira zaka ziwiri zapitazo ndimaona kuti zinthu zimene ndikanakonda mwa mwamuna woti ndikwatirane naye, n’zosiyana ndi zimene ndingakonde panopo. Ngakhale panopo sindikukhulupirira kuti ndingathe kusankha bwino pankhani imeneyi. Ndikadzafika poona kuti ndasiya kusinthasintha maganizo kwazaka zingapo, m’pamene ndidzayambe kuganiza zokhala pachibwenzi.”

      Kudikira n’kwabwino pachifukwa chinanso. Baibulo limatchula mawu oti ‘chimake cha unyamata’ pofotokoza nthawi imene chilakolako cha kugonana chimayamba kukhala champhamvu kwambiri. (1 Akorinto 7:36) Panthawi imeneyi, kumangocheza ndi munthu mmodzimodzi amene si mnyamata kapena mtsikana mnzanu kukhoza kukolezera chilakolako chimenechi mpaka kuchita tchimo. N’zoona kuti anzanu ena sangaone vuto lina lililonse kuchita zimenezi. Ambiri mwa iwo amafunitsitsa atagonana ndi munthu wina n’cholinga choti adziwe kuti zimakhala bwanji anthu akamagonana. Koma mukhoza kupewa maganizo amenewa. (Aroma 12:2) Ndipotu, Baibulo limakulimbikitsani kuti: “Thawani dama.” (1 Akorinto 6:18) Mukadikira mpaka kudutsa pachimake paunyamata, mukhoza kupewa “zoipa.”—Mlaliki 11:10.

      Kodi Mwafika Poti N’kulowa M’banja?

      Kuti muthe kuyankha funso limeneli, muyenera kuyamba mwadzidziwa bwino. Taganizirani izi:

      Mmene mumachitira zinthu ndi achibale anu. Kodi makolo anu ndiponso achibale anu mumakhala nawo bwanji? Kodi mumakonda kuwakwiyira, mwina kuwalankhula mawu okhadzula kapena achipongwe kuti amvetse mfundo yanu? Kodi iwowo anganene chiyani za inu pankhaniyi? Mmene mumachitira zinthu ndi achibale anu ndi mmenenso muzidzachitira zinthu ndi mwamuna kapena mkazi wanu.—Werengani Aefeso 4:31.

      Khalidwe lanu. Zinthu zikavuta, kodi mumataya mtima mwamsanga? Kodi ndinu wololera, kapena ndinu womva zanu zokha? Kodi mumatha kuchita zinthu moyenerera mukapanikizika? Kodi ndinu woleza mtima? Mukamayesetsa kukhala ndi zipatso za mzimu wa Mulungu panopa, zidzakuthandizani kukhala mwamuna kapena mkazi wabwino m’tsogolo.—Werengani Agalatiya 5:22, 23.

      Ndalama. Kodi mumatha kugwiritsa ntchito bwino ndalama? Kodi mumakhala ndi ngongole nthawi zonse? Kodi mungathe kukhalitsa pantchito? Ngati simungathe, n’chifukwa chiyani? Kodi n’chifukwa cha ntchitoyo kapena bwana wanu? Kapena n’chifukwa cha khalidwe linalake loipa limene muyenera kusintha? Ngati simutha kugwiritsa ntchito bwino ndalama pamene muli nokha, kodi mungadzakwanitse bwanji kugwiritsa ntchito bwino ndalama m’banja lanu?—Werengani 1 Timoteyo 5:8.

      Moyo wauzimu. Ngati ndinu wa Mboni za Yehova, kodi muli ndi makhalidwe otani auzimu? Kodi mumayesetsa panokha kuwerenga Mawu a Mulungu, kuchita utumiki, ndi kutenga nawo mbali pamisonkhano yachikhristu? M’pofunika kuti mukhale munthu wolimba mwauzimu, chifukwa chakuti munthu yemwe mungadzamange naye banja adzafunika munthu woteroyo.—Werengani Mlaliki 4:9, 10.

      Zimene Mungachite

      Kukakamizika kukhala ndi chibwenzi musanakonzekere, kuli ngati kukukakamizani kulemba mayeso omaliza a maphunziro enaake omwe mwangoyamba kumene kuphunzira. N’zodziwikiratu kuti zimenezi sizingakusangalatseni. Mungafunike kuphunzira mokwanira kuti mudziwe bwino zinthu zimene zingadzabwere pa mayesowo.

      N’chimodzimodzi ndi kukhala pachibwenzi. Monga mmene taonera, kukhala pachibwenzi si nkhani yamasewera. Choncho, musanayambe kuganiza zopeza chibwenzi, muyenera kuphunzira kaye zinthu zofunika kwambiri. Muyenera kuphunzira zimene mungachite kuti muzigwirizana bwino ndi anthu. Zimenezi zingakuthandizeni kuti pamene mwapeza munthu woyenera, chibwenzi chanu chidzayende bwino kwambiri. Ndipotu, kuti anthu akhale ndi ukwati wabwino amafunika kukhala mabwenzi abwino.

      Kudikira kaye musanakhale pachibwenzi, sikuti kumakupherani ufulu. M’malo mwake kumakupatsani ufulu wambiri woti ‘mukondwere ndi unyamata wanu.’ (Mlaliki 11:9) Ndipo mumakhala ndi nthawi yosintha kuti mukhale munthu wabwino ndiponso kuti moyo wanu wauzimu, womwe ndi wofunika kwambiri, ukhale wolimba.—Maliro 3:27.

      Pakalipano, mungasangalale kucheza ndi anyamata kapena atsikana osiyanasiyana. Kodi mungacheze nawo motani? Mungacheze nawo pagulu loyang’aniridwa bwino la anthu amisinkhu yosiyanasiyana. Mtsikana wina dzina lake Tammy anati: “Ndimaona kuti kucheza pagulu n’kosangalatsa kwambiri. Zimakhala bwino kukhala ndi anzako ambiri.” Monica nayenso anavomereza kuti: “Kucheza pagulu n’kwabwino kwambiri chifukwa mumatha kudziwana ndi anthu amakhalidwe osiyanasiyana.”

      Koma ngati muyamba mudakali wamng’ono kumangocheza ndi munthu mmodzimodzi, mukhoza kudzanong’oneza bondo m’tsogolo. Choncho, fatsani kaye. Gwiritsani ntchito nthawi imeneyi kuphunzira mmene mungakhalire ndi mabwenzi abwino nthawi yaitali. Ndiyeno mukadzayamba kuganiza zokhala ndi chibwenzi, mudzakhala mutadzidziwa bwino ndiponso mutadziwa bwino makhalidwe amene mungafune mwa munthu amene mudzakwatirane naye.

      WERENGANI ZAMBIRI PANKHANIYI M’BUKU LOYAMBA, MUTU 29 NDI 30

      M’MUTU WOTSATIRA

      Kodi mukuganiza zoyamba chibwenzi mobisa n’cholinga choti makolo anu asadziwe? Kuchita zimenezi kungakubweretsereni mavuto ambiri kuposa mmene mungaganizire.

      LEMBA LOFUNIKA

      “Wochenjera asamalira mayendedwe ake.”—Miyambo 14:15.

      MFUNDO YOTHANDIZA

      Kuti mukonzekere kukhala pachibwenzi komanso kulowa m’banja, werengani 2 Petulo 1:5-7 ndipo sankhani khalidwe limodzi limene mukufuna kuyesetsa kukhala nalo. Pakatha mwezi umodzi, onani zimene mwaphunzira za khalidwelo ndiponso zimene mwachita kuti mukhale nalo.

      KODI MUKUDZIWA . . . ?

      Kafukufuku wosiyanasiyana akusonyeza kuti anthu ambiri amene amalowa m’banja asanakwanitse zaka 20 zakubadwa, banja lawo limatha pasanapite zaka zisanu.

      ZOTI NDICHITE

      Pokonzekera kulowa m’banja, ndiyenera kuyesetsa kukhala ndi makhalidwe awa: ․․․․․

      Ndingayesetse kukhala nawo mwa kuchita izi: ․․․․․

      Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

      MUKUGANIZA BWANJI?

      ● Kodi ndi pamalo kapena pazochitika zotani pamene mungacheze moyenera ndi anthu amene si anyamata kapena atsikana anzanu?

      ● Kodi mungathandize bwanji m’bale wanu amene akufuna kuyamba chibwenzi adakali wamng’ono kwambiri?

      ● Ngati muli pachibwenzi koma mulibe cholinga chokwatirana, kodi zimenezo zingasokoneze motani maganizo a mnzanuyo?

      [Mawu Otsindika patsamba 18]

      “Ndikuganiza kuti munthu uyenera kukhala pachibwenzi ndi munthu yemwe umam’kondadi ndipo umaona kuti awirinu mungadzakhale ndi tsogolo labwino. Uyenera kukonda munthuyo osati kungofuna kukhala pachibwenzi.”​—Anatero Amber

      [Chithunzi pamasamba 16, 17]

      Mukakhala pachibwenzi popanda cholinga chokwatirana, mumafanana ndi mwana yemwe amaseweretsa chidole chake chatsopano kenako n’kuchitaya

  • Kodi kuchita Chibwenzi Mobisa N’koopsa Motani?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
    • Mutu 2

      Kodi kuchita Chibwenzi Mobisa N’koopsa Motani?

      Jessica anathedwa nzeru mnyamata wina wa m’kalasi mwake, dzina lake Jeremy, atayamba kusonyeza kuti akum’funa. Ponena za Jeremy, Jessica anati: “Anali mnyamata wooneka bwino kwambiri, ndipo anzanga ankandiuza kuti sindidzapezanso mnyamata wakhalidwe labwino ngati ameneyu. Panali atsikana angapo amene ankamusirira koma iye sankawafuna. Ankangofuna ineyo basi.”

      Pasanapite nthawi yaitali, Jeremy anafunsira Jessica. Jessica anauza Jeremy kuti iye ndi wa Mboni za Yehova, motero sangaloledwe kukhala pachibwenzi ndi mnyamata yemwe si wa Mboni. Jessica anati: “Nditamuuza zimenezi, Jeremy anatulukira nzeru inayake. Iye anati, ‘Tingathe kumangoyendetsa chibwenzi chathucho makolo ako osadziwa.’”

      KODI inuyo mungatani ngati munthu amene amakudololani atakuuzani nzeru yotereyi? Mwina mudabwa kumva kuti Jessica anamvera maganizo a Jeremy aja. Iye anati: “Ndinkaganiza kuti nditakhala naye pachibwenzi ndingathe kumuphunzitsa kuti ayambe kukonda Yehova.” Koma kodi zinaterodi? Chakumapeto kwa nkhaniyi tiona zimene zinachitika, koma choyamba tiyeni tione zimene zimachititsa ena kuchita chibwenzi mobisa.

      N’chifukwa Chiyani Amachita Zimenezi?

      Kodi achinyamata ena amachitiranji chibwenzi mobisa? Mnyamata wina dzina lake David ananena mwachidule kuti: “Iwowa amadziwa kuti makolo awo sangasangalale nazo.” Mtsikana wina dzina lake Jane anatchula chifukwa chinanso. Iye anati: “Ena amachita zibwenzi mobisa pofuna kutsimikizira kuti angathe kuchita zinthu paokha, popanda kuuzidwa zochita. Akamaona kuti sakupatsidwa ufulu wochita zinthu ngati munthu wamkulu, amaona kuti ndi bwino kungochita zimene akufuna popanda kuuza makolo awo.”

      Kodi mungaganizire zifukwa zina zimene zimapangitsa ena kuchita chibwenzi mobisa? Lembani m’munsimu zifukwazo.

      ․․․․․

      Mosakayikira, mukudziwa kuti Baibulo limati muyenera kumvera makolo anu. (Aefeso 6:1) Ndipotu ngati makolo anu akukuletsani kukhala pachibwenzi, ayenera kuti ali ndi zifukwa zomveka. Komabe musadabwe ngati mutakhala ndi maganizo otsatirawa:

      ● Ndimaona kuti ndine wotsalira chifukwa aliyense ali ndi chibwenzi kupatulapo ineyo.

      ● Munthu amene si wachipembedzo changa wandidolola.

      ● Ndimafuna kukhala pachibwenzi ndi Mkhristu mnzanga ngakhale kuti sindinafike pamsinkhu wolowa m’banja.

      N’kutheka kuti mukudziwiratu zimene makolo anu anganene pa maganizo amenewa. Ndipo pansi pamtima mungavomereze kuti makolo anuwo akunena zoona. Komabe, mwina mumamva ngati mmene ankamvera mtsikana wina dzina lake Manami, yemwe anati: “Ndimafuna kwambiri kukhala ndi chibwenzi moti nthawi zina ndimakayikira ngati ndi bwino kukhalabe wopanda chibwenzi. Achinyamata ambiri masiku ano, amaona kuti kukhala wopanda chibwenzi n’kutsalira kwambiri. Ndiponso palibe amene angafune kukhala yekhayekha.” Motero ena amachita chibwenzi mobisira makolo awo. Kodi amachita zimenezi motani?

      “Anatiuza Kuti Tisaulule”

      Mawu akuti “chibwenzi chobisa,” akusonyezeratu kuti pali zinazake zachinyengo. Ena amayendetsa chibwenzi chotere polankhulana pafoni kapena pa Intaneti. Akakhala pagulu, amangoonetsa ngati palibe chilichonse, koma mungadabwe kwambiri mutadziwa zimene amauzana pa Intaneti ndiponso pafoni.

      Njira inanso yobisira chibwenzi choterechi ndi yoti iwowa amaitana gulu la anzawo kuti akachite zinazake pamodzi, koma kenaka amene ali pachibwenziwo amangocheza awiri basi. James anati: “Nthawi ina, tinaitanidwa kuti tikacheze kwinakwake monga gulu, osadziwa kuti imeneyi inali njira yoti mnyamata ndi mtsikana winawake akacheze awiri, ndipo anatiuza kuti tisaulule.”

      Monga mmene James ananenera, nthawi zambiri anthu amathandizidwa ndi anzawo poyendetsa chibwenzi mobisa. Carol anati: “Mwina pamakhala mnzako mmodzi kapena awiri amene amadziwa za chibwenzicho koma sanena chilichonse chifukwa safuna kutchedwa kuti ndi apakamwa.” Nthawi zina, ena amachita kunena bodza lamkunkhuniza. Beth, wazaka 17, anati: “Ambiri amabisa zoti ali pachibwenzi ponamiza makolo awo za kumene akupita.” Misaki, mtsikana wazaka 19, anachita zimenezo. Iye anati: “Ndinkangopeka zoti ndiwauze. Komano pofuna kuti makolo anga asasiye kundikhulupirira, ndinkayesetsa kuti ndisamaname pa china chilichonse kupatulapo za chibwenzicho basi.”

      Kuopsa Kochita Chibwenzi Mobisa

      Ngati mukufuna kukhala ndi chibwenzi chobisa kapena ngati muli nacho kale, m’pofunika kuti muganizire mafunso awiri otsatirawa:

      Kodi khalidwe langali likandifikitsa kuti? Kodi muli ndi cholinga chokwatirana ndi munthuyo posachedwapa? Mnyamata wina wazaka 20 dzina lake Evan, anati: “Kukhala pachibwenzi popanda cholinga chomanga banja n’kofanana ndi kutsatsa malonda chinthu chinachake chimene sukuchigulitsa.” Mukatero, n’chiyani chingachitike? Lemba la Miyambo 13:12 limati: “Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima.” Kodi mungafune kuti munthu amene mumam’kondadi adwale mtima? Taonani chenjezo linanso: Kuchita chibwenzi mobisa kumakumanitsani mwayi woti makolo anu kapena achikulire ena okukondani akuthandizeni. Choncho, m’posavuta kuti muchite chiwerewere.—Agalatiya 6:7.

      Kodi Yehova Mulungu akumva bwanji ndi zimene ndikuchitazi? Baibulo limati: “Zinthu zonse zili pambalambanda ndi zoonekera poyera pamaso . . . pa uyo amene tidzayenera kuyankha kwa iye.” (Aheberi 4:13) Motero musadzinamize kuti mukubisa chibwenzi chanu kapena cha mnzanu, chifukwatu Yehova akuzidziwa kale zimenezo. Choncho, ngati mukuchita zachinyengo, dziwani kuti mukusewera paulimbo. Ndipotu, Yehova Mulungu amadana kwambiri ndi bodza. Moti “lilime lonama” lili m’gulu la zinthu zimene Baibulo linachita kuneneratu kuti iye amadana nazo.—Miyambo 6:16-19.

      Ululani

      N’chinthu chanzeru kuuza makolo anu kapena Mkhristu wamkulu wokhwima mwauzimu za chibwenzi chilichonse chimene mukuyendetsa mobisa. Ndipo ngati muli ndi mnzanu amene akuchita chibwenzi mobisa, musam’thandize chinyengo chakecho pomusungira chinsinsi. (1 Timoteyo 5:22) Komanso, kodi mungamve bwanji ngati mnzanuyo atagwa m’vuto chifukwa cha chibwenzicho? Kodi sitinganene kuti inuyo mwachititsa nawo vutolo?

      Tiyerekeze kuti muli ndi mnzanu amene amadwala matenda a shuga ndiyeno akudya zinthu zotsekemera kwambiri mobisa. Inuyo mutadziwa zimenezi, mnzanuyo akukupemphani kuti musaulule. Kodi mungatani? Kodi nkhawa yanu ingakhale pa kupulumutsa moyo wake kapena kumusungira chinsinsi?

      N’chimodzimodzinso ngati mukudziwa kuti mnzanu winawake akuchita chibwenzi mobisa. Musaope kuti mudana naye, muululeni. Ngati ali mnzanu weniwenidi, patsogolo pake adzazindikira kuti munatero chifukwa chomufunira zabwino.—Salmo 141:5.

      Mobisa Kapena Mosaonetsera?

      Sikuti nthawi zonse anthu akakhala pachibwenzi chimene anthu ena sakuchidziwa ndiye kuti akuchita zolakwika. Tayerekezerani kuti mnyamata ndi mtsikana akufuna kudziwana bwino, komano sakufuna kudzionetsera kwa kanthawi ndithu. N’kutheka kuti akutero pa chifukwa chofanana ndi chimene mnyamata wina dzina lake Thomas, ananena. Iye anati: “Iwo safuna kuti anthu aziwavutitsa ndi mafunso monga akuti: ‘Kodi mukwatirana liti?’”

      N’zoona kuti zonena za anthu ena zingathe kukulowetsani m’mavuto. (Nyimbo ya Solomo 2:7) Motero, anyamata ndi atsikana ena amaona kuti ndi bwino kusaonetsera akangoyamba kumene chibwenzi mpaka patapita nthawi ndithu. (Miyambo 10:19) Anna, yemwe ali ndi zaka 20, anati: “Kusaonetsera kumathandiza anthuwo kuti akhale ndi nthawi yokwanira yoona bwinobwino ngati onse atsimikizadi kumanga banja. Ndiyeno akatsimikizira zimenezi, m’pamene angayambe kuonetsera kwa anthu.”

      Komabe, dziwani kuti n’kulakwa kuwabisira anthu amene ayenera kudziwa za chibwenzicho, monga makolo anu komanso makolo a mnzanuyo. Ngati mukuona kuti simungauze munthu wina aliyense, dzifunseni chifukwa chake. Kodi n’kutheka kuti mukudziwa kuti makolo anu ali ndi zifukwa zomveka zokuletsani kutero?

      “Ndinadziwa Zoyenera Kuchita”

      Jessica, amene tam’tchula poyamba uja, anaganiza zothetsa chibwenzi chobisa ndi Jeremy atamva zimene zinachitikira mtsikana wina wachikhristu amenenso anachita chibwenzi mobisa. Jessica anati: “Nditamva mmene iye anathetsera chibwenzicho ndinadziwa zoyenera kuchita.” Kodi zinali zosavuta kuti Jessica athetse chibwenzi chakecho? Ayi. Jessica anati: “Uyutu anali mnyamata yekhayo amene ndinam’kondadi. Ndinkalira tsiku lililonse kwa milungu ingapo.”

      Komabe, Jessica ankadziwa kuti amakonda Yehova. Motero, ngakhale kuti anasokonezeka pang’ono, ankafunitsitsa kuchita zoyenera. Ndipo patapita nthawi, iye anasiya kuganiza za chibwenzicho. Jessica anati: “Tsopano ubwenzi wanga ndi Yehova walimba kwambiri. Ndikuyamikira kwambiri kuti iye amatipatsa malangizo ofunika panthawi yoyenera.”

      M’MUTU WOTSATIRA

      Tiyerekezere kuti mwafika poti n’kukhala ndi chibwenzi ndipo mwapeza munthu yemwe wakudololani. Kodi mungadziwe bwanji ngati munthuyo ndi wokuyenererani?

      LEMBA LOFUNIKA

      “Timafuna kuchita zinthu zonse moona mtima.”—Aheberi 13:18.

      MFUNDO YOTHANDIZA

      M’posafunika kuti muzingouza aliyense kuti muli pachibwenzi. Koma mufunikira kuuza anthu amene ali oyenera kudziwa. Anthu amenewa angakhale makolo anu ndiponso makolo a mnzanuyo.

      KODI MUKUDZIWA . . . ?

      Pamafunika kukhulupirirana kuti anthu akhale pa ubwenzi wokhalitsa. Kuchita chibwenzi mobisa kumachititsa kuti makolo anu asamakukhulupirireni, ndiponso chibwenzi choterocho chimakhala chopanda maziko abwino.

      ZOTI NDICHITE

      Ngati ndikuchita chibwenzi mobisa ndi Mkhristu mnzanga, ndiyenera kuchita izi: ․․․․․

      Ngati mnzanga akuchita chibwenzi mobisa, ndiyenera kuchita izi: ․․․․․

      Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

      MUKUGANIZA BWANJI?

      ● Taonani mawu omwe ali m’zilembo zakuda kwambiri patsamba 22 m’buku lino. Kodi ndi mawu ati omwe akufotokoza mmene inuyo mumamvera nthawi zina?

      ● Kodi mungathane bwanji ndi maganizo anuwo popanda kuchita chibwenzi mobisa?

      ● Kodi mungatani mutadziwa kuti mnzanu akuchita chibwenzi mobisa, ndipo n’chifukwa chiyani mungasankhe kuchita zimenezo?

      [Mawu Otsindika patsamba 27]

      “Ndinathetsa chibwenzi chomwe ndinkachita mobisa. N’zoona kuti zinali zovuta kwambiri kuchita zimenezi chifukwa tsiku lililonse ndikapita ku sukulu ndinkamuona mnyamatayo. Koma Yehova Mulungu amadziwa zonse ndipo amaona zimene ifeyo sitingathe kuona. Choncho, tiyenera kumudalira.’’—Anatero Jessica”

      [Chithunzi pamasamba 25]

      Kusaulula mnzanu amene akuchita chibwenzi mobisa kuli ngati kusaulula munthu wodwala matenda a shuga amene akudya zotsekemera kwambiri mobisa

  • Kodi Munthu Ameneyu Ndi Woyenera Kuti Ndimange Naye Banja?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
    • Mutu 3

      Kodi Munthu Ameneyu Ndi Woyenera Kuti Ndimange Naye Banja?

      Yankhani mafunso otsatirawa:

      Kodi ndi zinthu ndiponso makhalidwe ati amene panopa mukufuna kuti munthu wodzamanga naye banja akhale nawo? Pa zimene zili m’munsimu, lembani chizindikiro ichi ✔ pazinthu zinayi zimene mukuona kuti n’zofunika kwambiri.

      □ Wokongola □ Wokonda zinthu zauzimu

      □ Wochezeka □ Wokhulupirika

      □ Wotchuka □ Wakhalidwe labwino

      □ Wanthabwala □ Woganizira zam’tsogolo

      Pamene munali wamng’ono, kodi munakopekapo ndi munthu wina? Pa zimene zili m’mwambazi, lembani chizindikiro ichi ✘ pachinthu chimodzi chimene chinakukopani kwambiri panthawiyo.

      PALIBE cholakwika chilichonse ndi zinthu zimene zili pamwambazi, ndipo chilichonse pachokha chingakope munthu. Komabe, kodi simukuvomereza kuti achinyamata ambiri akakopeka ndi munthu, amatengeka kwambiri ndi zinthu zosafunika kwenikweni ngati zimene zili kumanzerezo?

      Koma munthu akamakula, nzeru zake zimakhwima ndipo amayamba kuganizira makhalidwe ofunika kwambiri ngati amene ali kumanjawo. Mwachitsanzo, amazindikira kuti mtsikana wokongola kwambiri m’dera lawo angathe kukhala wosakhulupirika, kapena mnyamata wotchuka kwambiri m’kalasi angathe kukhala wakhalidwe loipa. Ngati munthu wapitirira pachimake pa unyamata, amayamba kuganiza kwambiri za makhalidwe ofunika poyankha funso lakuti, “Kodi munthu ameneyu ndi woyenera kuti ndimange naye banja?”

      Dzidziweni Bwino Choyamba

      Musanayambe kuganiza za munthu amene angakhale woyenera kumanga naye banja, muyenera kudzidziwa bwino choyamba. Kuti muthe kuchita zimenezi, yankhani mafunso otsatirawa:

      Kodi ndi makhalidwe abwino ati amene ndili nawo? ․․․․․

      Kodi ndi zinthu ziti zimene sindichita bwino? ․․․․․

      Kodi ndikufuna kuti mwamuna kapena mkazi wanga azidzandichitira zotani ndipo ndikufuna kukhala ndi ubwenzi wotani ndi Mulungu? ․․․․․

      Kudzidziwa bwino kungakhale kovuta ndithu, koma mafunso ngati amenewa angakuthandizeni. Mukadzidziwa bwino, m’pamene mungathe kupeza munthu wokuyenerani yemwe angakuthandizeni kuti muzichita zinthu zabwino.a Ngati mukuona kuti mwapeza munthu woteroyo, kodi mungatani?

      Kodi Ndingangosankha Aliyense?

      “Kodi ungakonde kuti tikhale pachibwenzi?” Funso limeneli lingakupangitseni kuipidwa kapena kusangalala ndipo zimenezi zingadalire munthu amene wakufunsiraniyo. Tiyerekezere kuti mwalola. Kodi m’kupita kwanthawi, mungadziwe bwanji kuti mnzanuyo ndi wokuyenerani?

      Yerekezerani kuti mukufuna kugula nsapato. Mutalowa m’sitolo mwapeza nsapato zimene zakusangalatsani kwambiri. Koma mukukhumudwa chifukwa mutaziyesa, mukuona kuti zikukuthinani kwambiri. Kodi mungatani? Kodi mungagulebe nsapatozo? Kapena mungayang’ane zina? N’zodziwikiratu kuti mungasiye nsapatozo ndi kuyang’ana zina. Sichingakhale chinthu chanzeru kugula ndi kuvala nsapato zothina.

      Zimenezi n’zofanana ndi kupeza munthu woyenera kumanga naye banja. Pamoyo wanu mutha kukopeka ndi anyamata kapena atsikana angapo. Koma sikuti onsewo angakhale okuyenerani. Mosakayikira mungafune munthu amene mungadzakhale naye momasuka, wogwirizana ndi khalidwe lanu ndiponso zolinga zanu. (Genesis 2:18; Mateyo 19:4-6) Kodi munthu wotereyu mwam’peza? Ngati mwam’peza, kodi mungadziwe bwanji kuti ndi wokuyenererani?

      Onani Zinthu Zofunika Kwambiri

      Kuti mudziwe ngati munthuyo ndi wokuyenererani, ganizirani za moyo wake mofatsa. Koma m’pofunika kusamala chifukwa mungathe kukopeka naye n’kumanyalanyaza kuona zinthu zofunika kwambiri. Musapupulume, yesetsani kuona khalidwe lake lenileni. Kuchita zimenezi kumafuna khama, koma n’zimene muyenera kuchita. Mwachitsanzo, yerekezerani kuti mukufuna kugula galimoto inayake. Kodi mungatani kuti mudziwe ngati galimotoyo ili yabwino? Kodi mungakhutire ndi maonekedwe ake okha? Kodi simungachite bwino kufufuzanso zinthu zina zofunika kwambiri zokhudza galimotoyo, monga kulimba kwa injini yake?

      Kusankha munthu womanga naye banja ndi nkhani yaikulu kwambiri kuposa kusankha galimoto. Komabe anthu ambiri akakhala pachibwenzi, safufuza mokwanira za mnzawoyo. M’malo mwake amangotengeka ndi zinthu zimene onse awiri amakonda. Ndipo anganene kuti: ‘Timakonda nyimbo zofanana.’ ‘Timakonda kuchita zinthu zofanana.’ ‘Timagwirizana pa chilichonse.’ Monga taonera, ngati mwapitiriradi pa chimake cha unyamata, mudzayang’ana zinthu zofunika kwambiri. Mudzaona “munthu wa mkati, wa mu mtima.”—1 Petulo 3:4; Aefeso 3:16.

      Mwachitsanzo, m’malo mongoona mmene mumagwirizanirana pazinthu zina, mungachite bwino kuona zimene zimachitika mukasemphana maganizo ndipo zimenezi zingakuthandizeni kudziwana bwino. Mwina mungafune kudziwa kuti kodi amangoumirira zake zokha mpaka ‘kupsa mtima’ kapenanso kulankhula “mawu achipongwe”? (Agalatiya 5:19, 20; Akolose 3:8) Kapena kodi iye amasonyeza kuti ndi womvetsa zinthu ndiponso wololera maganizo a anthu ena pofuna kukhazikitsa mtendere, malinga ngati enawo sakuphwanya mfundo za m’Baibulo?—Yakobe 3:17.

      Mfundo inanso yofunika kuganizira ndi yakuti: Kodi mnzanuyo ndi wofuna zake zokha, wokonda kulamula kapenanso wansanje? Kodi amafuna kuti muzimuuza chilichonse chimene mukuchita kapena kulikonse kumene mukupita? Mtsikana wina dzina lake Nicole anati: “Ndamvapo za anthu akukangana ali pachibwenzi chifukwa wina sanauze mnzake kumene akupita. Ndikuganiza kuti zikamatere, ndiye kuti pali vuto lalikulu.”—1 Akorinto 13:4.

      Mfundo zimene taonazi zikukhudza umunthu ndi khalidwe. Komabe, m’pofunikanso kudziwa mbiri ya mnzanuyo. Kodi anthu ena amamuona bwanji? Mungachite bwino kufunsa anthu odalirika monga amumpingo wake, amene amudziwa munthuyo kwanthawi yaitali. Anthuwo adzakuthandizani kudziwa ngati mnzanuyo ali ndi mbiri yabwino.—Machitidwe 16:1, 2.

      Mungadziwe zambiri za mnzanuyo mwa kulemba zimene mwaona. Zimenezi zidzakuthandizani kudziwa ngati iye akukwanitsa zimene takambiranazi.

      Umunthu ․․․․․

      Khalidwe ․․․․․

      Mbiri ․․․․․

      Mungapindulenso mwa kuwerenga bokosi lakuti “Kodi Munthu Ameneyu Angadzakhale Mwamuna Wabwino?” patsamba 39 kapena lakuti “Kodi Munthu Ameneyu Angadzakhale Mkazi Wabwino?” patsamba 40. Mafunso amene afunsidwa m’mabokosiwa angakuthandizeni kudziwa ngati mnzanuyo alidi woyenera kumanga naye banja.

      Nanga bwanji ngati pambuyo poganiza bwinobwino mwaona kuti mnzanuyo sangakhale woyenera kumanga naye banja? Zikatero, mufunika kudzifunsa kuti:

      Kodi Ndithetse Chibwenzichi?

      Nthawi zina zingakhale bwino kuthetsa chibwenzi. Taganizirani zimene zinachitikira mtsikana wina dzina lake Jill. Iye ananena kuti: “Poyamba zinkandisangalatsa kwambiri kuona kuti bwenzi langa nthawi zonse ankafuna kudziwa kumene ndili, zimene ndikuchita, ndiponso anthu amene ndinali nawo. Koma zinafika poti sankafuna kuti ndizicheza ndi munthu wina koma iye yekha basi. Ndipo ankachita nsanje ngakhale ndikamacheza ndi anthu a m’banja lathu, makamaka bambo anga. Nditathetsa chibwenzicho ndinadzimva ngati kuti ndatula chimtolo cholemetsa.”

      Zinthu zoterezi zinam’chitikiranso Sarah. Iye anayamba kuona kuti John, mnyamata amene anali naye pachibwenzi, anali wachipongwe, wovuta ndiponso wamwano. Sarah anati: “Tsiku lina mnzangayo anafika kwathu atachedwa ndi maola atatu. Amayi anga atamutsegulira chitseko anangowanyalanyaza n’kundiuza kuti: ‘Tiye tizipita! Tachedwa.’ Iye sananene kuti ‘Ndachedwa,’ koma ‘Tachedwa.’ Iye anafunikira kupepesa kapena kufotokoza chifukwa chimene wachedwera. Komanso anayenera kuwapatsa ulemu amayi anga.” N’zoona kuti kuchita chinthu chokhumudwitsa kamodzi kokha kapena ngati munthuyo ali ndi khalidwe lina lokhumudwitsa si ndiye kuti chibwenzi chanu chithe. (Salmo 130:3) Koma Sarah atazindikira kuti John anali wamwano ndiponso kuti limeneli linalidi khalidwe lake, anasankha kuthetsa chibwenzicho.

      Mofanana ndi Jill ndi Sarah, kodi mungatani ngati mwazindikira kuti munthu amene muli naye pachibwenzi sadzakhala mwamuna kapena mkazi wabwino? Zitakero, musanyalanyaze maganizo anuwo. Zingakhale bwino kuthetsa chibwenzicho, ngakhale kuti kuchita zimenezi n’kovuta. Lemba la Miyambo 22:3 limati: “Wochenjera aona zoipa, nabisala.” Mwachitsanzo, ngati mnzanuyo akusonyeza chizindikiro chimodzi kapena zingapo zopezeka pa masamba 39 ndi 40 zosonyeza kuti pali vuto lalikulu, muyenera kuthetsa chibwenzicho, ngati mnzanuyo sakusintha. N’zoona kuti kuthetsa chibwenzi n’kovuta. Koma ukwati ndi mgwirizano wa moyo wonse. Choncho ndi bwino kuvutika maganizo kwa nthawi yochepa panopa, kusiyana ndi kuti mudzavutike maganizo kwa moyo wanu wonse.

      Mmene Mungamuuzire

      Kodi mungathetse bwanji chibwenzicho? Choyamba, sankhani malo ndi nthawi yabwino kuti mukambirane zimenezi. Kodi malo ndi nthawi yabwino zingakhale ziti? Ganizirani zimene inuyo mungakonde kuti akuchitireni zitakhala kuti akuthetsa chibwenzi ndi mnzanuyo. (Mateyo 7:12) Kodi mungakonde kukuuzirani pagulu? Ayi. Mungachite nkhanza kwambiri ngati mutathetsa chibwenzicho pafoni, kumulembera uthenga pafoni yam’manja, kapena kumutumizira uthenga pakompyuta, pokhapokha ngati pali zifukwa zomveka zochitira zimenezo. Choncho sankhani nthawi ndi malo abwino kuti mukambirane zimenezi.

      Kodi mungaiyambe bwanji nkhaniyi? Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu ‘kulankhula zoona’ wina ndi mnzake. (Aefeso 4:25) Choncho njira yabwino ndiyo kulankhula mosamala koma motsimikiza mtima. Fotokozani mosapita m’mbali chifukwa chimene inuyo mukuonera kuti chibwenzicho chithe. Simufunikira kumuyalira zolakwa zake zonse kapena kunena zinthu zambirimbiri zomunyoza. M’malo monena kuti, “Suchita” zakutizakuti kapena “Sunachitepo” zakutizakuti, zingakhale bwino kugwiritsa ntchito mawu osonyeza mmene inuyo mukumvera, monga akuti “Ineyo ndimafuna munthu amene . . . ” kapena “Ndikuona kuti chibwenzi chithe chifukwa chakuti . . . ”

      Imeneyi si nthawi yolankhula mokayikira kapena yololera maganizo a mnzanuyo. Kumbukirani kuti mwasankha kuthetsa chibwenzicho chifukwa chakuti pali vuto lalikulu. Choncho samalani ngati mnzanuyo akuchita zinthu kapena kulankhula mochenjera ndi cholinga choti musinthe maganizo. Mtsikana wina dzina lake Lori ananena kuti, “Nditathetsa chibwenzi, mnyamatayo anayamba kuchita zinthu ngati wasokonezeka maganizo kwambiri. Ndinadziwa kuti ankachita zimenezo kuti ndimumvere chisoni. Ngakhale kuti ndinamumveradi chisoni, sindinasinthe maganizo chifukwa cha zimenezo.” Mofanana ndi Lori, tsimikizirani kuti musasinthe zimene mwasankha. Mukati ayi akhaledi ayi.—Yakobe 5:12.

      Zimene Zingachitike Mutathetsa Chibwenzi

      Sizachilendo kukhala wokhumudwa kwambiri pambuyo pothetsa chibwenzi. Mwinanso mungamve ngati mmene anamvera wamasalmo amene anati: “Ndapindika, ndawerama kwakukulu; ndimayenda woliralira tsiku lonse.” (Salmo 38:6) Anzanu ena okufunirani zabwino angayese kukuthandizani mwa kukulimbikitsani kuti muyambirenso chibwenzicho. Koma samalani. Inuyo ndi amene mungadzavutike mukayambiranso chibwenzicho, osati anzanuwo. Choncho musalole kusintha maganizo, ngakhale kuti mungamve chisoni ndithu.

      Dziwani kuti m’kupita kwanthawi chisonicho chidzatha. Koma panthawi imeneyi yesani kuchita zinthu ngati zotsatirazi, zomwe zingakuthandizeni kupirira.

      Fotokozani maganizo anu kwa munthu amene mumamukhulupirira.b (Miyambo 15:22) Pempherani kwa Yehova za nkhaniyo. (Salmo 55:22) Yesetsani kukhala wotanganidwa ndi zinthu zina. (1 Akorinto 15:58) Musamadzipatule. (Miyambo 18:1) Chitani zinthu ndi anthu ena amene angakulimbikitseni. Yesetsani kumaganiza zinthu zolimbikitsa zokhazokha.—Afilipi 4:8.

      Patapita nthawi, mwina mungadzapeze chibwenzi china. Zikadzatero, mudzatha kuona zinthu bwinobwino chifukwa chakuti mwaphunzirapo kanthu. Mwinamwake nthawi imeneyo, mukadzadzifunsa kuti “Kodi munthu ameneyu ndi woyenera kuti ndimange naye banja?” mudzayankha kuti, inde!

      WERENGANI ZAMBIRI PANKHANIYI M’BUKU LOYAMBA, MUTU 31

      M’MUTU WOTSATIRA

      Mukakhala pachibwenzi, kodi muyenera kusonyezana chikondi mpaka pati?

      [Mawu a M’munsi]

      a Kuti mupeze mfundo zina zokuthandizani kudzidziwa bwino, onani Mutu 1, pakamutu kakuti “Kodi Mwafika Poti N’kulowa M’banja?”

      b Makolo anu kapena anthu ena achikulire monga akulu achikhristu angakuthandizeni. Mwinanso mungapeze kuti nawonso zinawachitikirapo zimenezi pamene anali achinyamata.

      LEMBA LOFUNIKA

      “Ngakhale mwana adziwika ndi ntchito zake; ngati ntchito yake ili yoyera ngakhale yolungama.”—Miyambo 20:11.

      MFUNDO YOTHANDIZA

      Chitani zinthu zotsatirazi zimene zingasonyeze makhalidwe anu enieni:

      ● Phunzirani Mawu a Mulungu pamodzi.

      ● Onani mmene mnzanuyo amachitira zinthu pamisonkhano ya mpingo ndi muutumiki.

      ● Gwirani nawo ntchito yoyeretsa ndiponso yomanga Nyumba za Ufumu.

      KODI MUKUDZIWA . . . ?

      Kafukufuku amasonyeza kuti maukwati a anthu osiyana zipembedzo nthawi zambiri amatha.

      ZOTI NDICHITE

      Nditakopeka ndi munthu wosakhulupirira, ndingachite izi: ․․․․․

      Kuti ndidziwe zambiri za khalidwe la munthu amene ndili naye pachibwenzi, ndingachite izi: ․․․․․

      Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

      MUKUGANIZA BWANJI?

      ● Kodi muli ndi makhalidwe abwino ati amene angadzathandize muukwati wanu?

      ● Kodi ndi makhalidwe abwino ati amene mungakonde kuti mnzanu woti mudzamange naye banja akhale nawo?

      ● Kodi pangakhale mavuto otani ngati mutakwatirana ndi munthu wosiyana naye chipembedzo?

      ● Kodi mungatani kuti mudziwe za khalidwe ndi mbiri ya munthu amene muli naye pachibwenzi?

      [Mawu Otsindika patsamba 37]

      “Mmene munthu amene muli naye pachibwenzi amachitira zinthu ndi achibale ake ndi mmenenso azidzachitira zinthu ndi inuyo.”​—Anatero Tony

      [Bokosi patsamba 34]

      “Musamangidwe M’goli ndi Osakhulupirira”

      Mosakayikira, mumaona kuti mfundo ya pa 2 Akorinto 6:14, yakuti, “musamangidwe m’goli ndi osakhulupirira,” ndi yothandiza. Ngakhale zili choncho, mungathe kukopeka ndi munthu wosakhulupirira. Chifukwa chiyani? Nthawi zina mungangokopeka ndi kukongola kwake. Mnyamata wina dzina lake Mark anati: “Panali mtsikana wina amene nthawi zonse ndinali kukumana naye kumalo ochitira masewera olimbitsa thupi. Nthawi zonse, mtsikanayu ankayesetsa kuti tizilankhulana. Zinali zosavuta kuti tiyambe kugwirizana.”

      Pazochitika ngati zimenezi, mungathe kuchita zinthu mwanzeru ngati mukudzidziwa bwino, mumadalira kwambiri mfundo za m’Baibulo komanso ngati mumachita zinthu mozindikira, osati chifukwa chongotengeka maganizo. Kunena zoona, munthu amene mungakopeke nayeyo, kaya akhale wokongola kapena wooneka ngati wamakhalidwe abwino, sadzakuthandizani kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Mulungu.—Yakobe 4:4.

      N’zoona kuti ngati mwayamba chibwenzi, n’zovuta kuchithetsa. Zimenezi n’zimene zinachitikira mtsikana wina dzina lake Cindy. Iye anati: “Ndinkalira tsiku ndi tsiku. Ndinkangoganiza za mnyamatayo nthawi zonse, ngakhale pamisonkhano yachikhristu. Ndinkamukonda kwambiri moti ndinkaganiza kuti kuli bwino kufa kusiyana ndi kuthetsa chibwenzicho.” Posapita nthawi, Cindy anaona kuti malangizo amene amayi ake anamupatsa, onena za kuipa kochita chibwenzi ndi munthu wosakhulupirira, anali anzeru. Iye anati: “Ndikusangalala kuti ndinathetsa chibwenzicho. Sindikukayikira kuti Yehova adzandipatsa chilichonse chimene ndikufuna.”

      Kodi zimene zinachitikira Cindy inunso zikukuchitikirani? Ngati ndi choncho, musayese kuthana nalo nokha vuto limenelo. Auzeni makolo anu zimenezi. Izi n’zimene Jim anachita atakopeka ndi mtsikana wina kusukulu. Iye anati: “Patapita nthawi, ndinauza makolo anga kuti andithandize. Izi zinandithandiza kwambiri kuchotsa maganizo olakwikawo.” Akulu kumpingo angathenso kukuthandizani. Bwanji osalankhula ndi mmodzi wa iwo ndi kumufotokozera zimene mukukumana nazo?—Yesaya 32:1, 2.

      [Bokosi/Chithunzi patsamba 39]

      Zimene Munalemba

      Kodi Munthu Ameneyu Angadzakhale Mwamuna Wabwino?

      Zinthu Zofunika Zokhudza Khalidwe Lake

      ◻ Kodi amasamalira bwanji udindo uliwonse umene ali nawo?—Mateyo 20:25, 26.

      ◻ Kodi zolinga zake n’zotani?—1 Timoteyo 4:15.

      ◻ Kodi panopa akuchita chilichonse kuti akwaniritse zolingazo?—1 Akorinto 9:26, 27.

      ◻ Kodi anthu a m’banja lake amakhala nawo bwanji?—Eksodo 20:12.

      ◻ Kodi anzake ndi otani?—Miyambo 13:20.

      ◻ Kodi amakonda kukamba nkhani zotani?—Luka 6:45.

      ◻ Kodi maganizo ake ndi otani pankhani ya ndalama?—Aheberi 13:5, 6.

      ◻ Kodi amakonda kusangalala ndi zinthu zotani?—Salmo 97:10.

      ◻ Kodi amasonyeza bwanji kuti amakonda Yehova?—1 Yohane 5:3.

      Zinthu Zofunika Kwambiri

      ◻ Kodi ndi wolimbikira ntchito?—Miyambo 6:9-11.

      ◻ Kodi amadziwa kugwiritsa ntchito bwino ndalama?—Luka 14:28.

      ◻ Kodi ali ndi mbiri yabwino?—Machitidwe 16:1, 2.

      ◻ Kodi ndi munthu woganizira ena?—Afilipi 2:4.

      Zinthu Zofunika Kusamala Nazo

      ◻ Kodi amapsa mtima msanga?—Miyambo 22:24.

      ◻ Kodi amakuumirizani kuchita zinthu zosayenera zokhudza kugonana?—Agalatiya 5:19.

      ◻ Kodi ndi wandewu kapenanso wolalata?—Aefeso 4:31.

      ◻ Kodi amaona kuti sangasangalale akapanda kumwa mowa?—Miyambo 20:1.

      ◻ Kodi ndi wansanje kapenanso wodzikonda?—1 Akorinto 13:4, 5.

      [Bokosi/Chithunzi patsamba 40]

      Zimene Munalemba

      Kodi Munthu Ameneyu Angadzakhale Mkazi Wabwino?

      Zinthu Zofunika Zokhudza Khalidwe Lake

      ◻ Kodi amasonyeza bwanji kuti ndi wogonjera m’banja lawo ndiponso mumpingo?—Aefeso 5:21, 22.

      ◻ Kodi anthu a m’banja lake amakhala nawo bwanji?—Eksodo 20:12.

      ◻ Kodi anzake ndi otani?—Miyambo 13:20.

      ◻ Kodi amakonda kulankhula za chiyani?—Luka 6:45.

      ◻ Kodi maganizo ake ndi otani pankhani ya ndalama?—1 Yohane 2:15-17.

      ◻ Kodi ali ndi zolinga zotani?—1 Timoteyo 4:15.

      ◻ Kodi panopa akuchita chilichonse kuti akwaniritse zolingazo?—1 Akorinto 9:26, 27.

      ◻ Kodi amakonda kusangalala ndi zinthu zotani?—Salmo 97:10.

      ◻ Kodi amasonyeza bwanji kuti amakonda Yehova?—1 Yohane 5:3.

      Zinthu Zofunika Kwambiri

      ◻ Kodi ndi wolimbikira ntchito?—Miyambo 31:17, 19, 21, 22, 27.

      ◻ Kodi amadziwa kugwiritsa ntchito bwino ndalama?—Miyambo 31:16, 18.

      ◻ Kodi ali ndi mbiri yabwino?—Rute 3:11.

      ◻ Kodi ndi munthu woganizira ena?—Miyambo 31:20.

      Zinthu Zofunika Kusamala Nazo

      ◻ Kodi ndi wolongolola?—Miyambo 21:19.

      ◻ Kodi amakuumirizani kuchita zinthu zosayenera zokhudza kugonana?—Agalatiya 5:19.

      ◻ Kodi ndi wolalata kapenanso wandewu?—Aefeso 4:31.

      ◻ Kodi amaona kuti sangasangalale akapanda kumwa mowa?—Miyambo 20:1.

      ◻ Kodi ndi wansanje kapenanso wodzikonda?—1 Akorinto 13:4, 5.

      [Chithunzi patsamba 30]

      Sikuti mungavale saizi iliyonse ya nsapato. N’chimodzimodzinso ndi munthu womanga naye banja, sikuti aliyense ndi wokuyenererani

      [Chithunzi patsamba 31]

      Pogula galimoto sikuti mungayang’ane kukongola kwake kokha, koma mungayang’anenso mbali zina zofunika. Ndiye kuli bwanji posankha munthu womanga naye banja?

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena