Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndizilankhula Momasuka ndi Makolo Anga?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
    • Mutu 1

      Kodi Ndingatani Kuti Ndizilankhula Momasuka ndi Makolo Anga?

      “Nkhani inayake itachitika, ndinayesetsa kwambiri kufotokozera makolo anga mmene ndinkamvera, koma ankangondidula mawu. Zinali zovuta kwambiri kuti ndilimbe mtima n’kuwauza mmene ndinkamvera, koma ngakhale kuti ndinayesetsa sizinathandize ngakhale pang’ono.”​—Anatero Rosa.

      N’KUTHEKA kuti muli mwana munkakonda kufunsa zinthu kwa makolo anu. Munkawauza chilichonse, ndi nkhani yaing’ono yomwe. Munkawafotokozera momasuka zakukhosi kwanu ndipo munkaona kuti malangizo awo ndi othandiza.

      Koma mwina masiku ano mumaona kuti makolo anu samakumvetsetsani. Mtsikana wina, dzina lake Edie, anati: “Tsiku lina tikudya chakudya chamadzulo ndinayamba kufotokoza mmene ndikumvera kwinaku ndikulira. Makolo anga ankamvetsera koma ankaoneka kuti sankandimvetsetsa.” Kenako mtsikanayu anafotokoza kuti: “Ndinangopita kuchipinda kwanga n’kukapitiriza kulira.”

      Achinyamata ambiri amaonanso kuti ndi bwino kubisira makolo awo nkhani zina. Mnyamata wina, dzina lake Christopher, anati: “Ndimauza makolo anga nkhani zambiri, koma pali nkhani zina zimene sindimawauza.”

      Kodi n’kulakwa kubisira makolo anu nkhani zina? Nthawi zina sikulakwa, bola ngati simukuchita zachiphamaso. (Miyambo 3:32) Komabe, kaya makolo anu amaoneka kuti sakumvetsetsani kapena inuyo simufuna kuwauza zinthu zina, dziwani mfundo iyi: Mwana amafunika aziuza makolo ake mmene akumvera ndipo makolo ayenera kumvetsera mwanayo akamalankhula.

      Musaleke Kulankhula Nawo

      Kulankhula ndi makolo anu tingakuyerekezere ndi kuyendetsa galimoto ndipo mavuto amene amalepheretsa kulankhulana tingawayerekezere ndi chikwangwani chosonyeza kuti msewu watsekedwa. Ngati mutapeza chikwangwani chosonyeza kuti msewu watsekedwa, simungabwerere koma mukhoza kungodzera msewu wina. Taganizirani zitsanzo ziwiri izi:

      VUTO LOYAMBA Inuyo mukufuna kulankhula ndi makolo anu, koma akuoneka ngati sakumvetsera. Mtsikana wina, dzina lake Leah, anati: “Zimandivuta kulankhulana ndi bambo anga. Nthawi zina ndimatha kuwafotokozera zinthu zambiri, koma kenako amanena kuti, ‘Pepa, kodi umalankhula ndi ine?’”

      FUNSO: Kodi Leah angatani ngati akufuna kuuza bambo ake vuto linalake? Pali njira zitatu zomwe angatsatire.

      Njira Yoyamba

      Akhoza kuwalusira bambo ake. Leah akulankhula mokalipa kuti: “Tamvetserani zimene ndikufuna ndikuuzenizi! Nkhani yake ndi yofunikatu!”

      Njira Yachiwiri

      Akhoza kusiya kulankhula nawo. Leah akusiya kulankhula ndi bambo ake.

      Njira Yachitatu

      Akhoza kudikira kuti alankhule ndi bambo akewo nthawi ina. Leah akudikira kaye kuti alankhule ndi bambo akewo nthawi ina kapena akuwalembera kalata yofotokoza vuto lakelo.

      Kodi inuyo mukuganiza kuti Leah asankhe njira iti? ․․․․․

      Tiyeni tikambirane njira iliyonse kuti tione zotsatira zake.

      Bambo a Leah atanganidwa ndi zinthu zina zomwe zachititsa kuti asadziwe zoti mwana wawoyo wakhumudwa. Choncho ngati Leah atasankha Njira Yoyamba, bambo akewo sangamvetse zimene zachititsa kuti mwana wawoyo aluse. Ndipo kuchita zimenezi sikungapangitse kuti bambo akewo amumvetsere komanso zingasonyeze kuti samawalemekeza. (Aefeso 6:2) Choncho, njira imeneyi singathandize ngakhale pang’ono.

      Njira Yachiwiri ingakhale yosavuta koma si yothandiza. Tikutero chifukwa chakuti “zolingalira sizikwaniritsidwa ngati anthu sakambirana moona mtima, koma aphungu akachuluka zimakwaniritsidwa.” (Miyambo 15:22) Kuti athetse vuto lakelo Leah akufunika kulankhulana ndi bambo ake koma n’zovuta kuti bambo akewo amuthandize ngati sakudziwa zimene zikumuchitikira. Choncho, kusiya kulankhula nawo n’kosathandiza.

      Njira Yachitatu, Leah sanasankhe kungosiya kulankhula ndi bambo ake chifukwa chakuti sakumumvetsera. M’malomwake iye waona kuti ndi bwino kuti alankhule nawo nthawi ina. Ndipo kulembera kalata bambo akewo kungamuthandize kumvako bwino, ngakhale asanamuyankhe. Komanso kulemba kalata kungamuthandize kuti afotokoze bwino vuto lakelo komanso mwaulemu. Bambo ake akawerenga kalatayo akhoza kudziwa zimene mwana wawo akufuna kuwafotokozera, zomwe zingawathandize kumvetsa vuto lakelo. Choncho njira yachitatuyi ingathandize Leah komanso bambo ake.

      Kodi pali njira zinanso zimene Leah angatsatire? Ganizirani njira imodzi ndipo ilembeni m’munsimu. Kenako lembani zimene zingachitike atatsatira njira imeneyi.

      ․․․․․

      VUTO LACHIWIRI Makolo anu akufuna kulankhula nanu koma inuyo simukufuna. Mtsikana wina, dzina lake Sarah, anati: “Palibe chimandikwana kwambiri ngati kufunsidwa mafunso ambirimbiri pambuyo poti ndatopa ndi za kusukulu. Ndimafuna kuiwalako za kusukulu koma nthawi yomweyo makolo amandifunsa kuti, ‘Waswera bwanji? Kusukulu kunali bwanji?’” Makolo a Sarah ayenera kuti amafunsa mafunso amenewa chifukwa choti amamukonda. Koma iye amadandaula kuti, “Sindimafuna kulankhula za kusukulu ndikatopa.”

      FUNSO: Kodi Sarah angatani? Mofanana ndi chitsanzo choyamba chija, pali njira zitatu zimene angatsatire.

      Njira Yoyamba

      Asalankhule nawo. Sarah anene kuti: “Ndisiyeni, sindikufuna zolankhula.”

      Njira Yachiwiri

      Alankhulebe nawo ngakhale asakufuna. Ngakhale kuti wakhumudwa, Sarah akuyankhabe zimene makolo akewo afunsa koma monyinyirika.

      Njira Yachitatu

      Asinthe nkhani, m’malo mokamba za kusukulu ayambitse nkhani ina. Sarah waona kuti ndi bwino kusiya kaye nkhani za kusukulu kuti adzakambirane nthawi ina maganizo ake atakhala m’malo. Kenako akunena kuti: “Ndaswera. Kaya inuyo tsiku lanu linali bwanji?”

      Kodi inuyo mukuganiza kuti Sarah asankhe njira iti? ․․․․․

      Tiyeni tikambiranenso njira iliyonse kuti tione zotsatira zake.

      Sarah watopa ndipo sakufuna zolankhula. Ndiye ngati atasankha Njira Yoyamba, sizingasinthe chilichonse chifukwa angakhalebe wotopa komanso angamadziimbe mlandu chifukwa choti anawalusira makolo akewo.​—Miyambo 29:11.

      Makolo a Sarah sangasangalale ngati mwana wawo atasiya kulankhula nawo komanso akhoza kukhumudwa ngati atawalusira. Iwo akhoza kuganiza kuti pali chinachake chimene mwana wawoyo akuwabisira. Ndipo angayesetse kwambiri kukakamiza mwana wawoyo kuti afotokoze zimene zili kukhosi kwake, zomwe zingamuchititse kuti akhumudwe kwambiri. Choncho, njira imeneyi singathandize makolowo komanso mwanayo.

      Njira Yachiwiri ndi yabwinoko poyerekeza ndi njira Yoyamba. Tikutero chifukwa onse akulankhulana. Komabe, kulankhulana kwawo n’kosathandiza chifukwa akungolankhula modzikakamiza.

      Koma Njira Yachitatu ndi yothandiza kwa Sarah chifukwa akusintha nkhaniyo n’kuyambitsa nkhani ina. Ndipo makolo ake angasangalale kwambiri kuti wayesetsa kulankhula nawo. Njira imeneyi ingathandize kwambiri chifukwa aliyense akuyesetsa kutsatira mfundo ya pa Afilipi 2:4 yakuti: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”

      Muzisamala Ndi Zimene Makolo Anu Angaganize

      Dziwani kuti nthawi zina zimene makolo anu angamve zingakhale zosiyana ndi zimene inuyo mwanena. Mwachitsanzo, ngati makolo anu atakufunsani kuti mwakwiya chifukwa chiyani, mungayankhe kuti, “Sindikufuna kuti tikambirane nkhani imeneyi.” Makolo anu angaganize kuti mukutanthauza kuti: “Sindikukhulupirirani ndiye sindingakuuzeni. Kulibwino ndikauze anzanga m’malo mouza inuyo.” Lembani zimene mukuganiza m’munsimu. Yerekezani kuti mwakumana ndi vuto linalake ndipo makolo anu akufuna kukuthandizani.

      Ngati mutayankha makolo anu kuti: “Musadandaule. Ndithana nalo ndekha vuto limeneli.”

      Makolo anu angaganize kuti mukunena kuti: ․․․․․

      Njira yabwino ndi kunena kuti: ․․․․․

      Koma mfundo yofunika kwambiri yomwe muyenera kuikumbukira ndi yakuti: Muziyamba mwaganiza kaye musanalankhule ndipo muzilankhula mwaulemu. (Akolose 4:6) Muziona makolo anu ngati anzanu, osati ngati adani anu. Ndipotu mumafunika kukhala ndi anthu amene angakuthandizeni kuti muthane ndi mavuto onse amene mungakumane nawo.

      M’MUTU WOTSATIRA

      Koma bwanji ngati nthawi iliyonse mukamalankhula ndi makolo anu mumakangana?

      LEMBA

      “Zonena zanga zikusonyeza kuwongoka kwa mtima wanga, ndipo milomo yanga imanena nzeru moona mtima.”​—Yobu 33:3.

      MFUNDO YOTHANDIZA

      Ngati mumaona kuti mumavutika kukambirana ndi makolo anu za vuto linalake mutakhala pansi, mukhoza kukambirana nawo poyenda, mukamapita kwinakwake pa galimoto kapena pokagula zinthu.

      KODI MUKUDZIWA . . . ?

      Ngati inuyo mumavutika kukambirana ndi makolo anu nkhani zinazake, dziwani kuti nawonso amavutika komanso samasuka kukambirana nanu nkhani zomwezo.

      ZOTI NDICHITE

      Ulendo wotsatira ndikadzakhala kuti sindikufuna kulankhula ndi makolo anga, ndidzachita izi: ․․․․․

      Makolo anga akadzandikakamiza kulankhula nawo nkhani inayake imene siikundisangalatsa ndidzanena kuti: ․․․․․

      Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi: ․․․․․

      KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

      ● Kodi kusankha nthawi yabwino yolankhulirana n’kofunika motani?​—Miyambo 25:11.

      ● N’chifukwa chiyani muyenera kuyesetsa kulankhula ndi makolo anu?​—Yobu 12:12.

      [Mawu Otsindika patsamba 10]

      “Nthawi zina kulankhula ndi makolo kumakhala kovuta, koma ukamayesetsa kulankhulana nawo umamva kupepukidwa mumtima.”​—Anatero Devenye

      [Chithunzi patsamba 8]

      Msewu ukatsekedwa mukhoza kupeza njira ina imene mungadutse. N’zothekanso kupeza njira yolankhulirana ndi makolo anu

  • N’chifukwa Chiyani Ndimangokhalira Kukangana ndi Makolo Anga?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
    • Mutu 2

      N’chifukwa Chiyani Ndimangokhalira Kukangana ndi Makolo Anga?

      Pa mkangano umene uli kumayambiriro kwa mutuwu, Rachel wachita zinthu zitatu zomwe zakolezera mkanganowu. Kodi mungathe kuzitchula? Lembani mayankho anu m’munsimu kenako muwayerekezere ndi mayankho amene ali m’bokosi lakuti “Mayankho” patsamba 20.

      ․․․․․

      Madzulo a Lachitatu, Rachel, yemwe ali ndi zaka 17, wamaliza ntchito zake ndipo akuganiza zoti apume. Akuyatsa TV n’kukhala pampando womwe amaukonda.

      Nthawi yomweyo, mayi ake akutulukira ndipo akuoneka kuti akwiya. Akumufunsa kuti: “Rachel! N’chifukwa chiyani ukuwononga nthawi kuonera TV m’malo moti uzikamuthandiza mwana kulemba homuweki? Siumamva chifukwa chiyani kodi iwe?”

      Rachel akuyankha mwamwano kuti: “Mwayambapotu zanu zija.”

      Mayi ake akumuyandikira n’kufunsa kuti: “Wati chani?”

      Rachel akuyankha mwamwano kuti: “Kaya.”

      Mayi ake akukwiya kenako akumuuza kuti: “Iwe usamalankhule choncho ndi ine!”

      Rachel akuyankha kuti: “Mukundinena ine, nanga inuyo?”

      Zikatero mkangano wayamba ndipo kupuma kuja kwathera pomwepo.

      KODI zimene zili pamwambazi zinakuchitikiranipo? Kodi inuyo mumakangana ndi makolo anu kawirikawiri? Ngati zili choncho, taganizirani izi. Kodi ndi nkhani ziti zimene mumakonda kukangana? Ikani chizindikiro ichi ✔ m’kabokosi komwe kali ndi nkhani zimene mumakonda kukangana kapena lembani nkhani yomwe mumakangana pamene alemba kuti “Zina.”

      □ Khalidwe

      □ Ntchito zapakhomo

      □ Zovala

      □ Nthawi yofika pakhomo

      □ Zosangalatsa

      □ Anthu ocheza nawo

      □ Nkhani ya anyamata kapena atsikana

      □ Zina ․․․․․

      Kaya mumakangana ndi makolo anu pa nkhani yanji, kukangana kumachititsa kuti nonse mukhumudwe. N’zotheka kungokhala phee n’kumaoneka ngati mukugwirizana ndi zimene makolo anu akunena. Koma kuchita zimenezi si nzeru chifukwa si zimene Mulungu amafuna kuti muzichita. N’zoona kuti Baibulo limati: “Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.” (Aefeso 6:2, 3) Koma limalimbikitsanso kuti muziyesetsa “kuganiza bwino” panokha komanso “kugwiritsa ntchito luntha [lanu] la kuganiza.” (Miyambo 1:1-4; Aroma 12:1) Mukamachita zimenezi, mungayambe kuona zinthu zina mosiyana ndi mmene makolo anu amazionera. Komabe, m’mabanja amene amatsatira mfundo za m’Baibulo, zimatheka makolo ndi ana kukambirana mwamtendere ngakhale kuti angamaone zinthu zina mosiyana.​—Akolose 3:13.

      Kodi mungafotokoze bwanji maganizo anu popanda kuyambitsa mkangano? Mwina munganene kuti: “Si ine amene ndimayambitsa mkangano. Makolo anga ndi amene ali ndi vuto chifukwa nthawi zonse amangondiuza zochita.” Koma taganizirani izi: Kodi inuyo mungathe kusintha maganizo a anthu ena, kuphatikizapo makolo anu? Ayi, inuyo ndi amene muyenera kusintha maganizo anu. Ndipo chosangalatsa n’chakuti ngati inuyo mutayesetsa kupewa mkangano, nawonso makolo anu angayambe kumaugwira mtima komanso kumakumvetserani mukamalankhula nawo.

      Choncho tiyeni tikambirane zomwe mungachite kuti musamangokhalira kukangana. Yesetsani kutsatira mfundo zomwe zili m’munsizi, ndipo mudzadabwa kuona kuti mwayamba kukambirana bwinobwino ndi makolo anu popanda kukangana.

      ● Muziganiza kaye musanayankhe. Ngati mukuona kuti makolo anu akukukalipirani musamangolankhula chilichonse chomwe chabwera m’maganizo mwanu. Mwachitsanzo, ngati mayi anu atanena kuti: “N’chifukwa chiyani sunatsuke mbale? Bwanji kodi iwe suumva?” Mwina yankho limene lingabwere mwamsanga m’maganizo mwanu lingakhale lakuti, “Inu musanditopetse.” Koma muziganiza kaye musanalankhule. Yesetsani kuganizira zimene zachititsa mayi anu kunena mawu amenewa. Nthawi zambiri munthu akanena kuti “sumachita chakutichakuti” satanthauza kuti suchitadi zomwe akunenazo. Koma pamakhala kuti pali chinthu chinachake chimene chawachititsa kunena zimenezo. Kodi chingakhale chiyani?

      N’kutheka kuti mayi anu atopa ndipo akuona kuti ali ndi ntchito yambiri yoti agwire pakhomopo. Akhozanso kukhala kuti akungofuna kuti inuyo muwatsimikizire kuti muwathandiza kugwira ntchito zina ndi zina. Ngati zili choncho, kuwayankha kuti “Inu musanditopetse” kungachititse kuti mungokanganapo. Mwina mungachite bwino kuwakhazika mtima pansi. Mwachitsanzo, mungawayankhe kuti: “Musadandaule amayi. Mbalezo nditsuka pompanopompano.” Komabe muyenera kusamala: Musanene zimenezi mwamwano. Ngati mutayankha mosonyeza kuti mukuwaganizira, mayi anu akhoza kuugwira mtima komanso akhoza kukuuzani chimene chawapangitsa kukulankhulani choncho.a

      Lembani zomwe mayi kapena bambo anu anganene, zimene zingakukwiyitseni ngati inuyo simungawayankhe bwino.

      ․․․․․

      Kenako ganizirani yankho labwinoko lomwe mungawayankhe lomwe lingathandize makolo anuwo kunena chomwe chawachititsa kukulankhulani choncho.

      ․․․․․

      ● Muzilankhula mwaulemu. Zimene zinachitikira Michelle zinamuthandiza kudziwa kuti ayenera kulankhula bwino ndi mayi ake. Iye anati: “Pa nkhani iliyonse imene tingakambirane, mayi anga amaoneka kuti sasangalala ndi mmene ndimawayankhira.” Ngati inunso zimakuchitikirani, yesetsani kulankhula modekha komanso mtima uli m’malo ndipo muzipewa kuchita zinthu zimene zingasonyeze kuti mwaboweka. (Miyambo 30:17) Ngati mukuona kuti mwayamba kukwiya, muzipereka pemphero lachidule la mumtima. (Nehemiya 2:4) Cholinga cha pempherolo chisakhale kupempha Mulungu kuti akuthandizeni kuwina mkanganowo koma kuti akuthandizeni kuugwira mtima kuti musanene zinthu zomwe zingapangitse kuti mkanganowo ufike poipa.​—Yakobo 1:26.

      Lembani m’munsimu mawu komanso zinthu zina zomwe muyenera kupewa polankhula ndi makolo anu.

      Mawu amene mungayankhe:

      ․․․․․

      Zomwe mungachite ndi nkhope yanu kapena thupi lanu posonyeza kukwiya:

      ․․․․․

      ● Muzimvetsera. Baibulo limati: “Pakachuluka mawu sipalephera kukhala zolakwa.” (Miyambo 10:19) Choncho, yesetsani kupereka mpata wolankhula kwa mayi komanso bambo anu ndipo inuyo muzimvetsera ndi mtima wonse. Musamawadule mawu n’cholinga choti mudziikere kumbuyo. Muzingomvetsera. Kenako, akamaliza kulankhula mungakhale ndi nthawi yokwanira yowafunsa mafunso kapena kufotokozapo maganizo anu. Koma ngati mutapupuluma kufotokoza maganizo anu nthawi yomwe akulankhulayo, mungangowonjezeranso mkanganowo. Ngakhale mutakhala ndi zambiri zolankhula, nthawi imeneyo ndi “nthawi yokhala chete.”​—Mlaliki 3:7.

      ● Khalani wokonzeka kupepesa. Nthawi zonse ndi bwino kupepesa pa chilichonse chomwe mwachita chimene chachititsa kuti mkanganowo uyambe. (Aroma 14:19) Mungapepesenso chifukwa chakuti pali kusemphana maganizo. Ngati mukuona kuti n’zovuta kupepesa pamasom’pamaso, mukhoza kungolemba kakalata kachidule. Ndipo m’malo mongopepesa chabe, mungachitenso bwino kusintha khalidwe lililonse lomwe layambitsa mkanganowo. (Mateyu 5:41) Mwachitsanzo, ngati makolo anu akwiya chifukwa choti simunagwire ntchito inayake, mungachite bwino kungogwira ntchitoyo. Ngakhale zitakhala kuti ntchitoyo sikusangalatsani, kuli bwino kungogwira ntchitoyo kusiyana n’kuti akukalipireni chifukwa choti simunagwire ntchitoyo. (Mateyu 21:28-31) Muziganizira phindu limene mungapeze ngati mutayesetsa mbali yanu kupewa kukangana ndi makolo anu.

      Mabanja amene amayenda bwino amasemphananso maganizo nthawi zina koma amakambirana mwamtendere. Yesetsani kutsatira malangizo amene takambirana m’mutu umenewu ndipo mudzaona kuti n’zotheka kukambirana bwinobwino nkhani zovuta ndi makolo anu popanda kukangana.

      M’MUTU WOTSATIRA

      Kodi mungatani ngati mumaona kuti makolo anu samakupatsani mpata wokwanira wochitira zinthu zina?

      [Mawu a M’munsi]

      a Kuti mudziwe zambiri, werengani Mutu 21 m’Buku Lachiwiri.

      LEMBA

      ‘Munthu wolungama amayamba waganiza asanayankhe.’​—Miyambo 15:28.

      MFUNDO YOTHANDIZA

      Ngati makolo anu ayamba kukulankhulani mukumvera nyimbo kapena kuwerenga, muyenera kuzimitsa kaye nyimbozo komanso kusiya zomwe mumawerengazo ndipo muziwayang’ana.

      KODI MUKUDZIWA . . . ?

      Kuyesetsa kupewa komanso kuthetsa kusamvana kungapangitse kuti moyo wanu uziyenda bwino. Ndipotu Baibulo limanena kuti munthu “wosonyeza kukoma mtima kosatha amapindulitsa moyo wake.”—Miyambo 11:17.

      ZOTI NDICHITE

      Pa mfundo zonse zomwe ndawerenga m’mutu umenewu ndikufuna ndiyesetse kwambiri kutsatira mfundo iyi: ․․․․․

      Ndikufuna ndiyambe kutsatira mfundo imeneyi pa (lembani deti) ․․․․․

      Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi: ․․․․․

      KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

      ● N’chifukwa chiyani anzanu amaona kuti ndi bwino kuyesetsa kuwina mkangano?

      ● N’chifukwa chiyani Yehova amaona kuti munthu wokonda mkangano ndi wopusa?​—Miyambo 20:3.

      ● Kodi mungapindule bwanji ngati mutamayesetsa kupewa kukangana ndi makolo anu?

      [Mawu Otsindika patsamba 18]

      “Nthawi zina mayi anga amandipepesa n’kundihaga ndipo ndimamva bwino kwambiri. Zimenezi zimachititsa kuti tonse tiiwale zimene tinasemphanazo. Nanenso ndimayesetsa kutengera chitsanzo chawo. Kudzichepetsa ndiponso kupepesa kuchokera pansi pa mtima n’kothandiza kwambiri ngakhale kuti sikophweka.”—Anatero Lauren

      [Bokosi patsamba 20]

      Mayankho

      1. Mawu amwano amene ananena (“Mwayambapotu zanu zija”) anangokolezera mkwiyo wa mayi ake.

      2. Zimene akuchita (kuyang’ana moderera) zikukwiyitsa mayi ake.

      3. Zimene anawayankha (“Mukundinena ine, nanga inuyo?”) nthawi zonse amayambitsa mkangano.

      [Chithunzi patsamba 19]

      Kukangana ndi makolo kuli ngati kumangothamanga pamodzimodzi. Mumangowononga mphamvu zanu koma muli pamalo amodzimodzi

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena