Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rr tsamba 47
  • “Ndinkayangʼana Angelowo”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Ndinkayangʼana Angelowo”
  • Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi ‘Angelo Ankhope 4 Aliyense’ Akuimira Chiyani?
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • ‘Ufotokoze za Kachisiyu’
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • ‘Ika Mtima Wako pa’ Kachisi wa Mulungu!
    Nsanja ya Olonda—1999
  • “Ndinayamba Kuona Masomphenya a Mulungu”
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
Onani Zambiri
Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
rr tsamba 47
Chifaniziro chakale cha ng’ombe yamphongo yamapiko yokhala ndi mutu wa munthu.

BOKOSI 4A

“Ndinkayangʼana Angelowo”

N’zodziwikiratu kuti Ezekieli anaonapo zifaniziro zikuluzikulu za ng’ombe zamphongo zamapiko komanso mikango zomwe zinali ndi mitu ya anthu ataziimika kutsogolo kwa nyumba zachifumu komanso akachisi. Zifaniziro ngati zimenezi zinkapezeka paliponse kalero ku Asuri komanso ku Babeloniya. Mofanana ndi zimene aliyense angachite, Ezekieli ayenera kuti ankayang’anitsitsa modabwa zifaniziro zazikuluzi, zomwe zinali zazitali mamita pafupifupi 6. Komabe, ngakhale kuti zifanizirozi zinkaoneka zamphamvu, zinali zopanda moyo chifukwa zinali zogobedwa kuchokera kumwala.

NG’OMBE YAMPHONGO YAMAPIKO YOMWE INALI NDI MUTU WA MUNTHU

Akuyerekezera kutalika kwa munthu (wamtali pafupifupi mamita 1.8) ndi kutalika kwa ng’ombe yamphongo yamapiko yokhala ndi mutu wa munthu (yaitali pafupifupi mamita 4.42).

Chifaniziro chosema chimenechi cha ng’ombe yamphongo yamapiko yomwe inali ndi mutu wa munthu chinali pageti lolowera mumzinda wakale wa Asuri wa Khosabadi. Chifanizirochi anachipanga n’cholinga choti chiziteteza mzindawu kuti musalowe zinthu zoipa.

Mosiyana ndi zimenezi, angelo 4 amene Ezekieli anaona m’masomphenya anali amoyo. Kumenekutu kunali kusiyana kwakukulu. Zimene Ezekieli anaonazi zinamukhudza kwambiri moti anatchula mawu oti angelo maulendo oposa 10 m’mawu oyamba a ulosi wake. (Ezek. 1:5-22) Masomphenya a angelo 4 amene ankayenda mogwirizana pansi pa mpando wachifumu wa Mulungu ayenera kuti anathandiza Ezekieli kumvetsa mfundo yoti Yehova ndi amene akulamulira zinthu zonse zimene analenga. Masiku anonso masomphenya amenewa amatithandiza kumvetsa kuti Yehova ndi wamkulu ndiponso wamphamvu komanso kuti ulamuliro wake ndi waulemerero.​—1 Mbiri 29:11.

Mmodzi wa angelo 4 okhala ndi nkhope 4, watambasula mapiko ake.

Bwererani ku mutu 4, ndime 4

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena