Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rr tsamba 120
  • Adzatithandiza Kuti Tiimirirenso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Adzatithandiza Kuti Tiimirirenso
  • Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • Nkhani Yofanana
  • “Mudzakhala Amoyo”
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • Mmene Yehova Amatithandizira Kukwaniritsa Utumiki Wathu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • ‘Ufotokoze za Kachisiyu’
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • ‘Ika Mtima Wako pa’ Kachisi wa Mulungu!
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
rr tsamba 120
M’bale wachikulire akuganizira mozama zimene wawerenga m’buku la Ezekieli.

BOKOSI 10C

Adzatithandiza Kuti Tiimirirenso

TINGALIMBIKITSIDWE tikamaganizira zimene tikuphunzira m’masomphenya ochititsa chidwi opezeka pa Ezekieli 37:1-14. Tingagwiritse ntchito zimene tikuphunzirazo pa moyo wathu. Kodi tikuphunzira chiyani?

Nthawi zina tingamade nkhawa kwambiri chifukwa cha mavuto komanso mayesero amene tikukumana nawo pa moyo wathu ndipo tingatope n’kumavutika kupirira. Koma pa nthawi ngati imeneyi tingalimbikitsidwe tikamaganizira za masomphenya obwezeretsa amene Ezekieli anawafotokoza momveka bwino. N’chifukwa chiyani tikutero? Ulosiwu ukutiphunzitsa kuti Mulungu amene ali ndi mphamvu zopereka moyo kwa mafupa opanda moyo, angathe kutipatsa mphamvu zoti tilimbane ndi mavuto amene tikukumana nawo ngakhale amene angaoneke ngati ndi osatheka kuwagonjetsa. Komanso amafunitsitsa kugwiritsa ntchito mphamvu zakezo pothandiza anthu ake.​—Werengani Salimo 18:29; Afil. 4:13.

Zimenezi zikutikumbutsa zomwe mneneri Mose ananena zaka zambiri nthawi ya Ezekieli isanafike, kuti Yehova ali ndi mphamvu komanso amafunitsitsa kugwiritsa ntchito mphamvu zakezo pothandiza anthu ake. Mose analemba kuti: “Mulungu ndi malo ako othawirapo kuyambira kalekale, iye wakunyamula mʼmanja ake omwe adzakhalapo mpaka kalekale.” (Deut. 33:27) Inde, tisamakayikire kuti tikamadalira Yehova pamene tikukumana ndi mavuto, iye adzatinyamula m’manja mwake n’kumatidzutsa pang’onopang’ono mpaka titaimiriranso.​—Ezek. 37:10.

M’bale wachikulire akuimba pamsonkhano wadera.

Bwererani ku mutu 10, ndime 15, 16

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena