GAWO 2
“Iwe Unaipitsa Malo Anga Opatulika”—Kulambira Koyera Kunadetsedwa
MFUNDO YAIKULU: Makhalidwe komanso moyo wauzimu wa anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu zinafika poipa
Yehova ankakonda komanso kusamalira Aisiraeli chifukwa anali ‘chuma chake chapadera.’ (Eks. 19:5) Koma Aisiraeliwo sanayamikire zimene Yehova anawachitira. M’malomwake iwo anayamba kulambira milungu yabodza m’kachisi amene ankadziwika ndi dzina lake. Iwo anakhumudwitsa kwambiri Yehova ndipo anachititsa kuti dzina lake lidetsedwe. N’chifukwa chiyani Aisiraeli anayamba kuchita zinthu zoipa choncho? Kodi tingaphunzire chiyani pa ulosi wa Ezekieli wokhudza kuwonongedwa kwa Yerusalemu? Nanga tingaphunzire chiyani pa zimene Aisiraeli ankachita ndi mitundu yowazungulira?