Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lff phunziro 44
  • Kodi Zikondwerero Zonse Zimasangalatsa Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Zikondwerero Zonse Zimasangalatsa Mulungu?
  • Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • FUFUZANI MOZAMA
  • ZOMWE TAPHUNZIRA
  • ONANI ZINANSO
  • Khalani ndi Cholinga Choti Muzilambira Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Kodi Mulungu Amasangalala Ndi Zikondwerero Zonse?
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Sachita Nawo Maholide Ena?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Yesetsani Kuti Muzilambira Mulungu M’njira Yovomerezeka
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
Onani Zambiri
Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
lff phunziro 44
Phunziro 44. Anthu ambirimbiri akuulutsa nyale m’mwamba pachikondwerero chinachake.

PHUNZIRO 44

Kodi Zikondwerero Zonse Zimasangalatsa Mulungu?

Losindikizidwa
Losindikizidwa
Losindikizidwa

Yehova amafuna kuti tizisangalala ndi moyo komanso amafuna kuti nthawi zina tizichita zikondwerero. Koma kodi ndi zikondwerero komanso maholide onse amene amasangalatsa Mulungu? Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Yehova posankha zoyenera kuchita pa nkhani imeneyi?

1. N’chifukwa chiyani zikondwerero zambiri sizisangalatsa Yehova?

Mungadabwe kudziwa kuti zikondwerero zambiri sizigwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa ndipo zina zinayambitsidwa ndi zipembedzo zabodza. Zikondwerero zimenezi zingakhale zokhudzana ndi zamizimu kapena zinayamba chifukwa cha chikhulupiriro chakuti pali chinachake chimene chimapitiriza kukhala ndi moyo munthu akamwalira. Zikondwerero zina zinayamba chifukwa chokhulupirira zaufiti kapena chikhulupiriro chakuti zinthu zinazake zoipa zikhoza kuchitika ngati munthu sanatsatire miyambo inayake. Choncho Yehova anachenjeza atumiki ake kuti: “Musiyane nawo, . . . Musakhudze chinthu chodetsedwa.”​—2 Akorinto 6:17.a

2. Kodi Yehova amamva bwanji akaona anthu akuchita zikondwerero polemekeza anthu enaake?

Yehova amatichenjeza kuti tiyenera kupewa ‘kukhulupirira munthu mnzathu.’ (Werengani Yeremiya 17:5.) Maholide ena anakhazikitsidwa pofuna kulemekeza olamulira kapena asilikali. Koma maholide ndi zikondwerero zina zimachitika pokumbukira tsiku limene dziko linalandira ufulu wodzilamulira kapena pokondwerera zizindikiro za dziko lawo monga mbendera. (1 Yohane 5:21) Pomwe maholide ena amachitika pofuna kulemekeza magulu andale kapena mabungwe omenyera ufulu wa anthu. Kodi Yehova angamve bwanji ngati titamachita zikondwerero zolemekeza anthu enaake kapena mabungwe, makamaka amene amalimbikitsa mfundo zosiyana ndi zimene Mulungu amafuna?

3. Kodi ndi makhalidwe ati amene amachititsa kuti zikondwerero zina zikhale zosayenera?

Baibulo limaletsa zinthu monga ‘kumwa vinyo mopitirira muyezo, kukonda maphwando oipa komanso kupanga mipikisano yomwa mowa.’ (1 Petulo 4:3) Anthu akamachita zikondwerero zina amachita zinthu mosadziletsa komanso amachita zachiwerewere. Kuti tikhalebe pa ubwenzi ndi Yehova, tiyenera kupeweratu zikondwerero zimene zimalimbikitsa makhalidwe oipa ngati amenewa.

FUFUZANI MOZAMA

Onani zimene mungachite kuti muzisangalatsa Yehova posankha zinthu moyenera pa nkhani ya maholide komanso zikondwerero.

M’bale akupatsidwa mphatso ya Khirisimasi ndi munthu yemwe amagwira naye ntchito.

4. Musamachite nawo zikondwerero zomwe Yehova sasangalala nazo

Werengani Aefeso 5:10, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi tiyenera kutsimikizira chiyani kuti tidziwe ngati ndi zoyenera kuchita nawo chikondwerero chinachake?

  • Kodi ndi zikondwerero ziti zimene ndi zotchuka kumene mumakhala?

  • Kodi mukuganiza kuti Yehova amasangalala ndi zikondwerero zimenezo?

Mwachitsanzo, kodi munayamba mwaganizirapo kuti maganizo a Mulungu pa nkhani yokondwerera tsiku lakubadwa ndi otani? Baibulo silitchula mtumiki wa Yehova aliyense yemwe anakondwererapo tsiku lakubadwa. Koma limatchula anthu awiri okha omwe anachita zimenezi ndipo onse sankatumikira Mulungu. Werengani Genesis 40:20-22 ndi Mateyu 14:6-10. Kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi pa zikondwerero ziwiri zonsezi, panachitika chinthu chofanana chiti?

  • Mogwirizana ndi zimene tawerenga m’mavesi aja, kodi mukuona kuti maganizo a Yehova ndi otani pa nkhani yokondwerera masiku akubadwa?

Mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi Yehova angakhumudwe ngati nditachita nawo zikondwerero za masiku akubadwa kapena zikondwerero zina zosagwirizana ndi mfundo za m’Baibulo?’ Werengani Ekisodo 32:1-8. Kenako, onerani VIDIYO n’kukambirana mafunso otsatirawa:

VIDIYO: Maholide Komanso Zikondwerero Zimene Mulungu Sasangalala Nazo (5:07)

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kutsimikizira kaye ngati zimene tikufuna kuchita ndi zovomerezeka kwa Yehova?

  • Nanga tingachite bwanji zimenezi?

Kodi mungadziwe bwanji zikondwerero zimene Mulungu sasangalala nazo?

  • Kodi chikondwererochi ndi chogwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa? Kuti mudziwe, fufuzani mmene chinayambira.

  • Kodi chikondwererochi chimalemekeza anthu, mabungwe kapena zizindikiro zimene dziko limaziona kuti ndi zofunika kwambiri? Timafunika kulemekeza Yehova kuposa aliyense ndipo timakhulupirira kuti iyeyo ndi amene adzathetse mavuto onse padzikoli.

  • Kodi zimene anthu amachita pa chikondwererochi zimagwirizana ndi mfundo za m’Baibulo? Tiyenera kuyesetsa kukhalabe oyera pamaso pa Mulungu.

5. Muzithandiza ena kuti azilemekeza zimene mumakhulupirira

Zimakhala zovuta kuti munthu akane anthu ena akamamukakamiza kuti achite nawo zikondwerero zimene Yehova amadana nazo. Komabe, mungachite bwino kuwafotokozera modekha komanso mosamala chifukwa chake simungachite nawo zikondwererozo. Kuti muone chitsanzo cha mmene mungachitire zimenezi, onerani VIDIYO.

VIDIYO: Muzifotokoza Zimene Mumakhulupirira Mosamala (2:01)

Werengani Mateyu 7:12, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Mogwirizana ndi vesili, kodi muyenera kumauza achibale anu kuti asiye kuchita chikondwerero chinachake?

  • Kodi mungatsimikizire bwanji achibale anu kuti mumawakonda komanso mumawaganizira ngakhale kuti simuchita nawo chikondwerero chinachake?

6. Yehova amafuna kuti tizisangalala

Yehova amafuna kuti tizisangalala limodzi ndi achibale komanso anzathu. Werengani Mlaliki 8:15, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi vesili likusonyeza bwanji kuti Yehova amafuna kuti tizisangalala?

Yehova amafuna kuti anthu ake azisangalala. Onerani VIDIYO yosonyeza mmene zimenezi zimachitikira pamisonkhano yathu yamayiko.

VIDIYO: Kulandira Alendo pa Misonkhano ya Mayiko (5:40)

Werengani Agalatiya 6:10, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi tiyenera kumachita nawo maholide otchuka ngati njira ‘yochitira ena zabwino’?

  • Kodi chingakusangalatseni ndi chiti pa zinthu ziwirizi: Kukakamizidwa kuti mupereke mphatso pa chikondwerero chinachake kapena kupereka mphatso chifukwa chakuti ndi zimene inuyo mukufuna?

  • Nthawi zina, a Mboni ambiri amachitira ana awo zinthu zinazake zapadera. Ndipo nthawi zina, amawagulira mphatso zomwe samaziyembekezera. Ngati muli ndi ana, kodi ndi zinthu zapadera ziti zimene mungawachitire?

Mtsikana akulandira mphatso imene samaiyembezera kuchokera kwa makolo ake.

ANTHU ENA AMANENA KUTI: “Zilibe ntchito kuti holideyo inayamba bwanji. Chofunika n’choti pa nthawiyi timapeza mwayi wosangalala limodzi ndi achibale komanso anzathu.”

  • Kodi mungamufotokozere zotani munthu wotereyu?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Yehova amafuna kuti tizisangalala limodzi ndi achibale athu komanso anzathu. Komabe iye amafuna kuti tisamachite nawo zikondwerero zimene sizimamusangalatsa.

Kubwereza

  • Kodi tingadzifunse mafunso ati kuti tidziwe ngati chikondwerero chinachake chimasangalatsa Yehova kapena ayi?

  • Kodi tingathandize bwanji achibale ndi anzathu kuti amvetse chifukwa chake sitichita nawo maholide enaake?

  • Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova amafuna kuti tizisangalala?

Zoti Muchite

ONANI ZINANSO

Onani maholide ena omwe Akhristu sakondwerera nawo.

“N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Sachita Nawo Maholide Ena?” (Nkhani yapawebusaiti)

Onani zifukwa 4 zomwe zimatichititsa kukhulupirira kuti zikondwerero za masiku akubadwa sizisangalatsa Mulungu.

“N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Sakondwerera Masiku Akubadwa?” (Nkhani yapawebusaiti)

Onani zimene achinyamata amene amakonda Yehova amachita pofuna kumusangalatsa pa nthawi ya maholide.

Yehova Amakuona Kuti Ndiwe Wofunika (11:35)

Akhristu ambiri anasankha kuti asamakondwerere nawo Khirisimasi. Kodi amamva bwanji akaganizira zimene anasankhazi?

“Amasangalala Ngakhale Kuti Sachita Khirisimasi” (Nsanja ya Olonda, December 1, 2012)

a Onani Mawu Akumapeto 5 kuti mudziwe zimene mungachite pamene anthu ena akukondwerera holide inayake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena