PHUNZIRO 42
Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yokhala Pabanja Ndi Kusakhala Pabanja?
Anthu azikhalidwe zina amakhulupirira kuti munthu sangakhale wosangalala pokhapokha akhale pabanja. Komabe, si anthu onse omwe ali pabanja amene amasangalala. Komanso si anthu onse amene sali pabanja amene sasangalala. Baibulo limanena kuti kukhala pabanja komanso kusakhala pabanja, zonse ndi mphatso zochokera kwa Yehova.
1. Kodi kusakhala pabanja kuli ndi ubwino wotani?
Baibulo limati: “Amenenso wasiyana ndi moyo wokhala yekha n’kulowa m’banja wachita bwino, koma amene sanalowe m’banja wachita bwino kwambiri.” (Werengani 1 Akorinto 7:32, 33, 38.) N’chifukwa chiyani tinganene kuti munthu amene wasankha kusakhala pabanja “wachita bwino kwambiri”? Popeza kuti Mkhristu amene sali pabanja sakhala ndi udindo wosamalira mwamuna kapena mkazi wake, iye amakhala ndi ufulu wambiri. Anthu amene sali pabanja akhoza kuwonjezera utumiki wawo m’njira zambiri. Mwachitsanzo, angapite kudziko lina kuti akalalikire uthenga wabwino. Komanso chofunika kwambiri, amakhala ndi nthawi yambiri yolimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova.
2. Kodi kupanga ukwati wovomerezeka ndi boma kuli ndi ubwino wotani?
Mofanana ndi kusakhala pabanja, kukhala pabanja nakonso kuli ndi ubwino wake. Baibulo limanena kuti “awiri amaposa mmodzi.” (Mlaliki 4:9) Zimenezi ndi zimene zimachitika kwa Akhristu amene amatsatira mfundo za m’Baibulo m’banja mwawo. Anthu amene amapanga ukwati wovomerezeka ndi boma, amalonjeza kuti azikonda ndi kulemekeza mnzawoyo komanso kumuona kuti ndi wofunika kwambiri. Anthu amene ali m’banja lovomerezeka ndi boma amaona kuti ndi otetezeka kwambiri kusiyana ndi anthu amene amangotengana n’kumakhala limodzi. Ubwino winanso ndi wakuti ana amene abadwira m’banja limene makolo awo anapanga ukwati wovomerezeka ndi boma amakhala otetezeka.
3. Kodi maganizo a Yehova ndi otani pa nkhani ya banja?
Pamene Yehova ankayambitsa banja ananena kuti: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake.” (Genesis 2:24) Yehova amafuna kuti mwamuna ndi mkazi amene akwatirana azikondana n’kumakhala limodzi kwa moyo wawo wonse. Iye amalola munthu kuti athetse banja pokhapokha ngati mnzake wachita chigololo. Zikatere, Yehova amapereka mwayi kwa munthu wosalakwayo kuti asankhe kuthetsa banja kapena ayi.a (Mateyu 19:9) Yehova safuna kuti Akhristu azikhala pa mitala.—1 Timoteyo 3:2.
FUFUZANI MOZAMA
Onani zimene mungachite kuti muzisangalala komanso kusangalatsa Yehova kaya muli pabanja kapena ayi.
4. Muzigwiritsa ntchito bwino mphatso ya kusakhala pabanja
Yesu ankaona kuti kusakhala pabanja ndi mphatso. (Mateyu 19:11, 12) Werengani Mateyu 4:23, kenako mukambirane funso ili:
Kodi Yesu anagwiritsa ntchito bwanji mphatso ya kusakhala pabanja potumikira Atate ake komanso kuthandiza anthu ena?
Akhristu akhoza kumasangalala pogwiritsa ntchito mphatso yawo ya kusakhala pabanja ngati mmene Yesu ankachitira. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:
Kodi Akhristu angagwiritse ntchito bwanji mphatso yawo ya kusakhala pabanja?
Kodi mukudziwa?
Baibulo silinena kuti munthu ayenera kukwatira kapena kukwatiwa ali ndi zaka zingati. Komabe, limalimbikitsa kuti munthu ayenera kudikira mpaka ‘atapitirira pachimake pa unyamata.’ Pa nthawi imeneyi, wachinyamata amakhala ndi chilakolako champhamvu kwambiri cha kugonana zomwe zingachititse kuti alephere kusankha zinthu moyenera.—1 Akorinto 7:36.
5. Sankhani mwanzeru munthu amene mukufuna kukwatirana naye
Kusankha munthu yemwe mukufuna kukwatirana naye ndi nkhani yaikulu. Werengani Mateyu 19:4-6, 9, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani Mkhristu sayenera kuthamangira kulowa m’banja?
Baibulo lingakuthandizeni kuti musankhe bwino munthu yemwe mungakhale naye pabanja. Koma chofunika kwambiri ndi kusankha munthu yemwe amakonda Yehova.b Werengani 1 Akorinto 7:39 ndi 2 Akorinto 6:14. Kenako mukambirane mafunso awa:
N’chifukwa chiyani Mkhristu ayenera kukwatirana ndi Mkhristu mnzake?
Kodi mukuganiza kuti Yehova angamve bwanji ngati Mkhristu atakwatirana ndi munthu yemwe samutumikira?
Nyama zomwe ndi zosiyana zikamangidwa limodzi pagoli zingavutike kuchitira zinthu limodzi. Mofanana ndi zimenezi, Mkhristu amene wakwatirana ndi munthu wosakhulupirira angakumane ndi mavuto ambiri
6. Muziona ukwati mmene Yehova amauonera
Kale ku Isiraeli, amuna ena ankasiya akazi awo pa zifukwa zosamveka. Werengani Malaki 2:13, 14, 16, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani Yehova amadana ndi kuthetsa banja pa zifukwa zosagwirizana ndi mfundo za m’Baibulo?
Wina akachita chigololo kapenanso banja likatha zimabweretsa mavuto kwa munthu amene sanalakweyo komanso ana
Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.
Ngati munakwatirana ndi munthu yemwe satumikira Yehova, kodi mungatani kuti banja lanu liziyenda bwino?
7. Muzigwiritsa ntchito mfundo za Yehova zokhudza ukwati
Munthu angafunike kuchita khama kuti azigwiritsa ntchito mfundo za Yehova zokhudza ukwati.c Komabe Yehova amadalitsa anthu amene amayesetsa kuchita zimenezi. Onerani VIDIYO.
Werengani Aheberi 13:4, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi inuyo mukuona kuti mungakwanitse kutsatira mfundo zokhudza banja zimene Yehova anatipatsa? N’chifukwa chiyani mukutero?
Yehova amafuna kuti Akhristu amene akufuna kukwatirana azikalembetsa ukwati wawo kuboma komanso Akhristu amene akufuna kuthetsa banja, azikatenga chikalata chothetsera ukwati kuboma. Chifukwa zimenezi ndi zimene maboma amafuna kuti nzika zawo zizichita. Werengani Tito 3:1, kenako mukambirane funso ili:
Ngati muli pabanja, kodi munalembetsa ukwati wanu kuboma?
MUNTHU WINA ATAKUFUNSANI KUTI: “Kodi pali chifukwa chokalembetsera ukwati wanga kuboma? Si bola ngati tikukondana basi?”
Kodi munthu wotereyu mungamuyankhe bwanji?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Kukhala pabanja kapena kusakhala pabanja, zonse ndi mphatso zochokera kwa Yehova. Zonse zingathandize munthu amene akuchita zimene Yehova amafuna kukhala wosangalala.
Kubwereza
Kodi munthu angatani kuti azigwiritsa ntchito bwino mphatso yake ya kusakhala pabanja?
N’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti Mkhristu azikwatirana ndi Mkhristu mnzake?
Kodi Baibulo limanena kuti munthu akhoza kuthetsa banja pa chifukwa chiti?
ONANI ZINANSO
Kodi kukwatira kapena kukwatiwa “mwa Ambuye” kumatanthauza chiyani?
“Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” (Nsanja ya Olonda, July 1, 2004)
“Onerani vidiyo ya mbali ziwiri yomwe ingakuthandizeni kusankha zochita mwanzeru pa nkhani zokhudza chibwenzi komanso kukhala pabanja.
Onani chifukwa chake m’bale wina amaona kuti zimene Yehova wamupatsa ndi zamtengo wapatali kwambiri kuposa zinthu zonse zimene anasiya.
Ndinkakhulupirira Kuti Nayenso Akhoza Kuphunzira Choonadi 1:56
Kodi munthu ayenera kuganizira mfundo ziti akamafuna kupatukana kapena kuthetsa ukwati?
“Tizilemekeza ‘Chimene Mulungu Wachimanga Pamodzi’” (Nsanja ya Olonda, December 2018)
a Onani Mawu Akumapeto 4, pa nkhani ya kupatukana ngati wina sanachite chigololo.
b M’zikhalidwe zina, makolo amatha kusankhira mwana wawo munthu woti adzakwatirane naye. M’zikhalidwe zoterozo, makolo achikondi amaganizira zosankha munthu amene amakonda Yehova osati chuma chimene munthuyo ali nacho.
c Ngati mukukhala ndi munthu amene simunakwatirane naye, zili ndi inu kusankha kumusiya kapena kukwatirana naye.