PHUNZIRO 37
Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani ya Ntchito Komanso Ndalama
Kodi munayamba mwadapo nkhawa ndi nkhani zokhudza ntchito komanso ndalama? Kunena zoona nthawi zina zimakhala zovuta kuti tichite zonse zomwe tingathe kuti tizilambira Yehova kwinaku tikuyesetsa kugwira ntchito kuti tipeze zofunika pa moyo. Komabe, Baibulo lili ndi malangizo amene angatithandize pa nkhaniyi.
1. Kodi Baibulo limanena zotani pa nkhani ya ntchito?
Yehova amafuna kuti tizisangalala ndi ntchito yomwe tikugwira. Baibulo limati: “Palibe chabwino kwa munthu kuposa . . . kusangalala chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama.” (Mlaliki 2:24) Yehova amagwira ntchito mwakhama. Choncho, ifenso tikamagwira ntchito mwakhama timasangalatsa Yehova komanso timasangalala.
N’zoona kuti ntchito ndi yofunika komabe sitiyenera kuiona kuti ndi yofunika kwambiri kuposa kulambira Yehova. (Yohane 6:27) Mulungu anatilonjeza kuti tikamaika zinthu zokhudza kulambira pamalo oyamba, adzatipatsa zomwe timafunikira.
2. Kodi Baibulo limanena zotani pa nkhani zokhudza ndalama?
Baibulo limanena kuti ‘ndalama zimateteza.’ Komabe, limanenanso kuti ndalama sizingatithandize kukhala osangalala. (Mlaliki 7:12) M’pake kuti limatichenjeza kuti tisamakonde ndalama ndipo limatilimbikitsa kuti ‘tizikhutira ndi zimene tili nazo pa nthawiyo.’ (Werengani Aheberi 13:5.) Tikamakhala okhutira ndi zimene tili nazo, timapewa nkhawa zimene zimabwera chifukwa cha mtima wofuna kukhala ndi zinthu zambiri. Komanso timapewa ngongole zosafunikira. (Miyambo 22:7) Timapewanso mavuto amene amabwera chifukwa chotchova juga ndiponso kuchita nawo mabizinesi omwe amalimbikitsa anthu kulemera mwachangu.
3. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife owolowa manja pogwiritsa ntchito ndalama zathu?
Yehova ndi Mulungu wowolowa manja ndipo tingasonyeze kuti tikumutsanzira pokhala “owolowa manja komanso okonzeka kugawira ena.” (1 Timoteyo 6:18) Tingachite zimenezi popereka ndalama zathu kuti zithandize pampingo ndiponso pothandiza amene akuvutika makamaka abale ndi alongo athu. Yehova amasangalala kwambiri akamaona cholinga chimene timaperekera ndalama zathu, osati kuchuluka kwa ndalamazo. Tikamapereka ndalama zathu mowolowa manja, timakhala osangalala komanso timasangalatsa Yehova.—Werengani Machitidwe 20:35.
FUFUZANI MOZAMA
Onani ubwino wokhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ntchito komanso ubwino wokhutira ndi zimene tili nazo.
4. Mukamalimbikira ntchito mumalemekeza Yehova
Kukonda Yehova kungatithandize kuti tizikhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ntchito. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso awa:
Muvidiyoyi, n’chiyani chimene chakusangalatsani ndi zimene Jason amachita akakhala kuntchito komanso mmene amaonera ntchitoyo?
Kodi anachita zotani kuti ntchito isamamulepheretse kuchita zinthu zofunikira kwambiri?
Werengani Akolose 3:23, 24, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ntchito n’kofunika?
Ntchito ndi yofunika. Komabe, sitiyenera kuiona kuti ndi yofunika kwambiri kuposa kulambira Yehova
5. Tikamakhutira ndi zimene tili nazo timakhala osangalala
Anthu ambiri amachita chilichonse chomwe angathe kuti apeze ndalama zambiri. Koma Baibulo silimatilimbikitsa kuchita zimenezi. Werengani 1 Timoteyo 6:6-8, kenako mukambirane funso ili:
Kodi Baibulo limatilimbikitsa kuchita chiyani?
Ngakhale titakhala ndi zinthu zochepa, tikhoza kumakhala osangalala. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.
N’chiyani chikupangitsa mabanjawa kukhala osangalala ngakhale kuti amapeza ndalama zochepa?
Kodi pangakhale vuto lotani ngati tili ndi zinthu zambiri koma tikufunanso kuwonjezera zina? Yesu ananena fanizo lomwe limasonyeza kuopsa kwa mtima umenewu. Werengani Luka 12:15-21, kenako mukambirane funso ili:
Kodi mwaphunzira zotani mufanizo la Yesuli?—Onani vesi 15.
Werengani Miyambo 10:22 ndipo muyerekezere ndi 1 Timoteyo 6:10. Kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi mukuganiza kuti chofunika kwambiri n’chiyani, kukhala pa ubwenzi ndi Yehova kapena kukhala ndi ndalama zambiri? N’chifukwa chiyani mukutero?
Kodi munthu amene amangokhalira kufunafuna ndalama amakumana ndi mavuto otani?
6. Yehova adzatipatsa zomwe timafunikira
Kusowa kwa ntchito komanso mavuto azachuma zingatithandize kudziwa ngati timakhulupirira Yehova kapena ayi. Onerani VIDIYO kuti muone zomwe tingachite tikakumana ndi mavuto oterewa kenako mukambirane mafunso otsatirawa.
Muvidiyoyi, kodi m’baleyu anakumana ndi mavuto otani?
Kodi anachita zotani kuti akwanitse kuthana ndi mavutowo?
Werengani Mateyu 6:25-34, kenako mukambirane funso ili:
Kodi Yehova analonjeza kuti anthu omwe amaika zofuna zake pamalo oyamba adzawachitira zotani?
ANTHU ENA AMANENA KUTI: “Ndimafunika kugwira ntchito mwakhama kuti ndisamalire banja langa ndiye sindingakwanitse kupita kumisonkhano mlungu uliwonse.”
Ndi lemba liti limene limakutsimikizirani kuti kuika zinthu zokhudza kulambira pamalo oyamba ndi chinthu chanzeru chimene munthu angachite pa moyo wake?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Ntchito ndiponso ndalama ndi zofunika koma tisalole kuti zizitilepheretsa kulambira Yehova.
Kubwereza
N’chiyani chingakuthandizeni kuti muziona ntchito moyenera?
Kodi kukhutira ndi zimene muli nazo kungakuthandizeni bwanji?
Mungasonyeze bwanji kuti mumakhulupirira zimene Yehova analonjeza zakuti adzasamalira atumiki ake?
ONANI ZINANSO
Fufuzani kuti muone ngati Baibulo limanena kuti ndalama ndi zoipa.
“Kodi Ndalama ndi Zimene Zimabweretsa Mavuto Onse?” (Nkhani yapawebusaiti)
Onani mmene tingagwiritsire ntchito ndalama zathu kuti tizisangalatsa Mulungu.
“Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kupatsa?” (Nkhani yapawebusaiti)
Kodi kutchova juga kulibe vuto lililonse?
“Zimene Baibulo Limanena—Kutchova Juga” (Galamukani!, March 2015)
Onani zimene zinathandiza munthu wina kusiya kutchova juga komanso kuba.
“Ndinkakonda Kwambiri Mpikisano wa Mahatchi” (Nsanja ya Olonda, November 1, 2011)