Ndaona Mphamvu ya Choonadi cha M’baibulo
Yosimbidwa ndi Vito Fraese
NKUTHEKA kuti simunamvepo dzina lakuti Trentinara. Limeneli ndi dzina la tauni ina ya kum’mwera kwa Naples m’dziko la Italy. Makolo anga ndiponso mkulu wanga dzina lake Angelo anabadwira m’tauni imeneyi. Mkulu wangayu atabadwa, makolo anga anasamukira ku United States ndipo anakakhala ku Rochester, ku New York, komwe ine ndinabadwira m’chaka cha 1926. Bambo anga anakumana koyamba ndi Mboni za Yehova m’chaka cha 1922, zomwe pa nthawiyo zinkadziwika kuti Ophunzira Baibulo. Pasanapite nthawi yaitali, bambo ndi mayi anga anakhala Ophunzira Baibulo.
Bambo anga anali munthu wofatsa komanso woganiza kwambiri koma zinthu za chinyengo zinkawakwiyitsa kwambiri. Iwo sankasangalala ndi atsogoleri a chipembedzo omwe ankachititsa kuti anthu asadziwe choonadi. Choncho, bambo anga ankagwiritsa ntchito mpata uliwonse kufotokoza choonadi cha m’Baibulo kwa ena. Atapuma pa ntchito anayamba utumiki wa nthawi zonse. Iwo anasiya utumikiwu ali ndi zaka 74 chifukwa cha kudwala ndiponso chifukwa cha nyengo yozizira kwambiri. Komabe ankalalikira kwa maola a pakati pa 40 ndi 60 mpaka pamene anali ndi zaka za m’ma 90. Chitsanzo cha bambo anga chinandilimbikitsa kwambiri. Ngakhale kuti nthawi zina ankachita tinthabwala, bambo anga sanali munthu wachibwana. Nthawi zambiri ankanena kuti: “Osachita chibwana ndi choonadi.”
M’banja lathu tinalipo ana asanu ndipo bambo ndi mayi anga ankayesetsa kutiphunzitsa Mawu a Mulungu. Ine ndinabatizidwa pa August 23, 1943 ndipo ndinayamba upainiya mu June, 1944. Mlongo wanga Carmela ankachita upainiya ku Geneva, ku New York, limodzi ndi mnzake dzina lake Fern, yemwe anali wansangala. Pasanapite nthawi yaitali ndinaona kuti sindingachitire mwina koma kukwatira Fern kuti ndikhale naye kwa moyo wanga wonse. Choncho tinakwatirana mu August, 1946.
Utumiki wa Umishonale
Utumiki woyamba umene tinachitira limodzi unali upainiya wapadera ku Geneva ndi ku Norwich, ku New York. Mu August 1948, tinalowa kalasi la nambala 12 m’Sukulu ya Gileadi. Kenako tinatumizidwa kumzinda wa Naples m’dziko la Italy limodzi ndi Carl ndi mkazi wake Joanne Ridgeway. Pa nthawiyi mumzinda wa Naples munali mavuto ena chifukwa unali utawonongedwa pa nthawi ya nkhondo. Zinali zovuta kupeza nyumba, choncho kwa miyezi ingapo tinkakhala m’kanyumba kena kokhala ndi zipinda ziwiri.
Makolo anga ankalankhula Chitaliyana cha ku Naples. Choncho ngakhale kuti ndinkamveka lilime la ku America, anthu ankamva Chitaliyana chimene ndinkalankhula. Fern anavutika kwambiri kuti aphunzire chinenerochi. Koma kenako anachiphunzira mwamsanga mpaka kundiposa.
Anthu achidwi oyamba kuwapeza anali banja la anthu anayi. Iwo ankagulitsa fodya woletsedwa. Teresa, yemwe anali m’banjali, ankasintha mochititsa chidwi tsiku ndi tsiku. M’mawa ankaoneka wonenepa kwambiri chifukwa cha ndudu zimene ankaziika m’matumba a siketi yake. Koma madzulo ankaoneka wowonda kwambiri. Choonadi chinasintha kwambiri anthu a m’banja limeneli. Patapita nthawi anthu 16 a m’banja limeneli anakhala a Mboni za Yehova. Tsopano mumzinda wa Naples muli Mboni pafupifupi 3,700.
Ntchito Yathu Inaletsedwa
Titangokhala ku Naples miyezi 9, akuluakulu a boma analamula anthu anayife kuti tichoke mumzindawo. Tinachoka n’kukakhala ku Switzerland kwa mwezi umodzi kenako tinabwerera ku Italy ngati anthu odzaona malo. Ine ndi Fern tinatumizidwa ku Turin. Poyamba tinkachita lendi chipinda chimodzi m’nyumba ya mayi wina ndipo tinkagwiritsa ntchito khitchini ndi bafa imodzi. Banja la Ridgeways litafika ku Turin, tinachita lendi nyumba ina n’kumakhala limodzi. Kenako mabanja asanu a amishonale ankakhala m’nyumba imodzi.
Pofika mu 1955, akuluakulu a boma anatilamula kuti tichoke ku Turin. Pa nthawiyi tinali titayala maziko a mipingo inayi m’derali. Abale ena a m’derali anali okonzeka kuyendetsa zinthu m’mipingoyi. Akuluakulu a bomawa anatiuza kuti: “Sitikukayikira ngakhale pang’ono kuti anthu a ku America inu mukachoka, ziphunzitso zanu zidzatha.” Koma chiwerengero cha Mboni za Yehova chinawonjezeka kwambiri ndipo uwu ndi umboni wakuti Mulungu ndi amene amadalitsa ntchitoyi. Masiku ano ku Turin kuli Mboni zoposa 4,600 ndiponso mipingo 56.
Mzinda wa Florence Ndi Wabwino Kwambiri
Kenako tinatumizidwa kukatumikira mumzinda wa Florence. Tinamvapo za mzindawu kwa mchemwali wanga Carmela ndi mwamuna wake Merlin Hartzler, omwe ankatumikira monga amishonale kumeneku. Kumeneku kuli malo monga Piazza della Signoria, Ponte Vecchio, Piazzale Michelangelo ndi Palazzo Pitti. Malo amenewa ndi amene anachititsa kuti mzindawu ukhale wokongola kwambiri. Zinali zosangalatsa kuona anthu a ku Florence akumvetsera kwambiri uthenga wabwino.
Tinayamba kuphunzira ndi banja lina ndipo makolo m’banjali anabatizidwa. Koma bambo a m’banjali ankasuta fodya. Mu 1973 Nsanja ya Olonda inanena kuti kusuta fodya ndi khalidwe lodetsa ndipo aliyense amene ankasuta anayenera kusiya. Ana akuluakulu a m’banjali ankapempha bambo awo kuti asiye kusuta. Iwo analonjeza kuti asiya koma sanasiye. Tsiku lina madzulo, mayi a m’banjali anauza ana awo a mapasa a zaka 9 kuti apite kukagona asanapemphere. Kenako mayiwo anayamba kudziimba mlandu n’kupita kuchipinda cha anawo. Atafika anapeza kuti iwo apemphera kale ndipo anawafunsa kuti: “Mwanena zotani m’pemphero lanulo?” Anawo anayankha kuti: “Tinanena kuti Yehova, chonde muthandize bambo athu kuti asiye kusuta.” Zitatero mayiwo anaitana amuna awo n’kuwauza kuti: “Tabwerani mudzamve pemphero la ana anu.” Bambowo atabwera ndi kumva pempherolo anayamba kulira n’kunena kuti: “Basi sindidzasutanso.” Kuyambira pamenepo sanasutenso ndipo tsopano anthu oposa 15 m’banjali ndi Mboni.
Kutumikira ku Africa
Mu 1959 anatitumiza ku Mogadishu, m’dziko la Somalia limodzi ndi Arturo Leveris ndi mchimwene wanga dzina lake Angelo. Pamene tinkafika m’dzikoli tinapeza kuti munali mavuto a za ndale. Bungwe la United Nations linalamula kuti boma la Italy lipereke ufulu ku dziko la Somalia koma zinthu zinkangoipiraipira. Anthu ena a ku Italy amene tinkaphunzira nawo anasamuka m’dzikoli ndipo zinali zovuta kukhazikitsa mpingo kuderali.
Pa nthawi imeneyi woyendera nthambi anandipempha kuti ndizimuthandiza pa ntchito yake. Ndiye tinayamba kuyendera mayiko apafupi. Anthu ena amene tinkaphunzira nawo anapita patsogolo koma kenako anasamuka chifukwa chotsutsidwa. Ena anakhalabe komweko ngakhale kuti ankazunzidwa kwambiri.a Timakhudzidwa kwambiri tikaganizira mmene amakondera Yehova komanso kupirira kwawo kuti akhalebe okhulupirika.
Ku Somalia ndi ku Eritrea kunkatentha kwambiri. Zakudya zina zimene ankatipatsa zinkachititsa kuti tizimva kutentha kwambiri. Tinadya zakudya za mtunduwu koyamba titapita kwa munthu amene tinkaphunzira naye Baibulo. Pa tsikuli mkazi wanga ananena moseka kuti makutu ake afiira kwambiri.
Pamene Angelo ndi Arturo anatumizidwa kudera lina, ife tinatsala tokha. Zinthu zinali zovuta kwambiri chifukwa panalibe munthu aliyense wotilimbikitsa. Komabe izi zinatithandiza kuyandikira kwambiri Yehova ndipo tinayamba kumudalira kwambiri. Tinkalimbikitsidwa kwambiri pamene tinkayendera abale m’mayiko amene choonadi chinali chotsekedwa.
Ku Somalia kunalinso mavuto osiyanasiyana. Tinalibe firiji, choncho tsiku lililonse tinkafunika kugula chakudya cha tsikulo monga nyama, nthuli za nsomba ya shaki, ndi zipatso monga mapapaya, manyumwa, kokonati ndiponso nthochi. Tinkavutikanso ndi tizilombo toulukauluka. Nthawi zina tinkatera pakhosi lathu tikamachititsa phunziro la Baibulo. Ubwino wake tinali ndi njinga yamoto yomwe inkatithandiza kuti tisamayende wapansi n’kumapsa ndi dzuwa kwa nthawi yaitali.
Kubwerera ku Italy
Anzathu anatithandiza kuti tipite ku Italy pa boti lonyamula nthochi kukachita nawo msonkhano wa mayiko ku Turin m’chaka cha 1961. Tili kumeneko anatidziwitsa zoti tisintha utumiki wathu. Mu September 1962, tinabwerera ku Italy, kumene ndinayamba kutumikira monga woyang’anira dera. Tinagula kagalimoto kakang’ono kamene tinakagwiritsa ntchito kwa zaka zisanu pamene tinkayendera madera awiri.
Titachoka ku Africa komwe kunali kotentha kwambiri tinakakhala kumalo komwe tinafunika kupirira chifukwa chakuti kunali kozizira kwambiri. Tsiku lina m’nyengo yozizira kwambiri tili kumpingo wina m’mphepete mwa phiri la Alps, tinagona m’chipinda chomwe anangounjika udzu n’kupanga bedi ndipo munali mopanda mbaula kapena magetsi. Kunkazizira koopsa moti tinakagona titavala majasi athu. Usiku umenewu nkhuku zinayi ndi agalu awiri anafa chifukwa cha kuzizira.
Kenako ndinatumikiranso ngati woyang’anira chigawo. M’zaka zimenezo tinazungulira m’dziko lonse la Italy. Tinafika m’madera monga Calabria ndi Sicily maulendo ambirimbiri. Tinalimbikitsa achinyamata kuti akule mwauzimu n’cholinga choti atumikire monga oyang’anira m’mipingo, oyang’anira oyendayenda kapena atumiki a pa Beteli.
Taphunzira zinthu zambiri kwa atumiki anzathu okhulupirika amene akhala akutumikira Yehova ndi mtima wonse. Timachita chidwi ndi makhalidwe awo monga kukhala okhulupirika kwambiri kwa Yehova zivute zitani, kuwolowa manja, kukonda abale, kukhala ololera zinthu zikasintha ndiponso mtima wodzipereka. Tapezekanso pa mwambo wa ukwati wa abale ndi alongo okhulupirika ambiri. Maukwatiwa ankamangitsidwa m’Nyumba za Ufumu ndi abale amene anali ovomerezeka ndi boma. Zinthu zimenezi zinali zosatheka zaka zingapo m’mbuyomo m’dzikoli. Masiku ano mipingo sichitanso misonkhano m’makhitchini a abale ndipo sakhalanso pamatabwa ngati mmene zinalili ku Turin. Mipingo yambiri ili ndi Nyumba za Ufumu zokongola kwambiri zimene zimalemekezetsa Yehova. Sitichitanso misonkhano m’mabwalo wamba koma m’Nyumba za Misonkhano zokhala ndi malo okwanira. Pamene tinkafika ku Italy kunali ofalitsa 490 okha. Koma n’zosangalatsa kuona kuti chiwerengero cha ofalitsa chawonjezeka kufika pa 243,000.
Tinasankha Bwino
Tinali ndi mavuto athu ena monga matenda ndiponso kulakalaka kupita kwathu. Nthawi zonse Fern akaona nyanja ankalakalaka kupita kumudzi. Iye anachitidwanso maopaleshoni akuluakulu atatu. Tsiku lina akupita kukachititsa phunziro la Baibulo munthu wina anamumenya ndi chifoloko cholimira. Izi zinachititsa kuti apitenso kuchipatala.
Ngakhale kuti nthawi zina tinkafooketsedwa, takhala ndi ‘mtima wodikira Yehova’ mogwirizana ndi lemba la Maliro 3:24. Iye ndi Mulungu wa chitonthozo. Tsiku lina titakhumudwa, Fern analandira kalata yochokera kwa M’bale Nathan Knorr. Iye analemba kuti akazi achidatchi a ku Pennsylvania ngati Fern anali amphamvu ndiponso akhama. Anadziwa zimenezi chifukwa chakuti nayenso anabadwira pafupi ndi Bethlehem ku Pennsylvania kumene Fern anayambira upainiya. Izi zinalidi zoona. Pa zaka zonsezi takhala tikulimbikitsidwa m’njira zosiyanasiyana ndi anthu ambiri.
Ngakhale kuti tinkakumana ndi mavuto, takhala tikuyesetsa kukhalabe achangu mu utumiki. Poyerekezera changu chathu ndi vinyo wokoma wonyezimira wotchedwa Lambrusco, wa ku Italy, Fern ankakonda kunena moseka kuti: “Tisalole kuti changu chathu chizirale n’kusiya kunyezimira.” Nditatumikira monga woyang’anira dera ndiponso chigawo kwa zaka zoposa 40, tinapatsidwa mwayi woyendera ndiponso kuyambitsa timagulu ndi mipingo ya zinenero zina. Magulu amenewa amalalikira kwa anthu ochokera ku Bangladesh, China, Eritrea, Ethiopia, Ghana, India, Nigeria, Philippines, Sri Lanka ndi mayiko ena. Taona kuti Mawu a Mulungu ndi amphamvu kwambiri ndipo amasintha moyo wa anthu amene alawa chifundo cha Yehova. N’zosatheka kulemba m’buku umboni wambirimbiri wotsimikizira mfundo imeneyi.—Mika 7:18, 19.
Tsiku lililonse timapempha Yehova kuti atipatse mphamvu kuti tithe kupirira nkhawa ndiponso mavuto ena a m’matupi athu kuti tipitirizebe kuchita utumiki. Chimwemwe cha Ambuye wathu ndicho mphamvu yathu. Chimatithandiza kukhala ndi chiyembekezo ndiponso otsimikizira kuti tinasankha bwino kukhala atumiki ofalitsa choonadi cha m’Baibulo.—Aef. 3:7; Akol. 1:29.
[Mawu a M’munsi]
a Onani 1992 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, masamba 95-184.
[Tchati/Chithunzi pamasamba 27-29]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Makolo anga ali ku Rochester, New York
1948
Tili ku South Lansing kumene tinakalowa kalasi la nambala 12 la sukulu ya Gileadi
1949
Ndili ndi Fern tisanapite ku Italy
Capri, Italy
1952
Tili pamodzi ndi amishonale anzathu ku Turin ndi ku Naples
1963
Fern ndi ena amene ankaphunzira nawo Baibulo
“Tisalole kuti changu chathu chizirale n’kusiya kunyezimira”