Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w18 December tsamba 8
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Muli ndi Chifukwa Chomveka Choyembekezera Paradaiso?
    Nsanja ya Olonda—2004
  • “Tidzaonana M’Paradaiso”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Tizithandiza Kukongoletsa Gulu la Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • “Iwe Udzakhala ndi Ine m’Paradaiso”
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
w18 December tsamba 8
Mtumwi Paulo

Mafunso Ochokera Kwa Owerenga

Kodi mawu oti Paulo “anakwatulidwira kumwamba kwachitatu” komanso ‘kulowa m’paradaiso’ amatanthauza chiyani?​—2 Akor. 12:2-4.

Pa 2 Akorinto 12:2, 3, Paulo ananena kuti munthu wina “anakwatulidwira kumwamba kwachitatu.” Kodi ankanena za ndani? M’kalata imene Paulo analembera mpingo wa ku Korinto, iye anasonyeza kuti anali mtumwi wosankhidwa ndi Mulungu. (2 Akor. 11:5, 23) Kenako ananena za “masomphenya ndi mauthenga ochokera kwa Ambuye.” Atanena zimenezi, Paulo sanatchule abale ena. Choncho ayenera kuti ankanenabe za iyeyo kuti ndi amene analandira masomphenya ndi mauthengawo.​—2 Akor. 12:1, 5.

Pa chifukwa chimenechi tinganene kuti Pauloyo ndi amene “anakwatulidwira kumwamba kwachitatu” komanso ‘kulowa m’paradaiso.’ (2 Akor. 12:2-4) Iye anagwiritsa ntchito mawu oti “masomphenya” posonyeza kuti zinthuzi ndi zoti zidzachitike m’tsogolo.

Kodi “kumwamba kwachitatu” kumene Paulo anaona n’chiyani?

M’Baibulo, mawu akuti “kumwamba” angatanthauze m’mlengalenga. (Gen. 11:4; 27:28; Mat. 6:26) Koma mawuwa amatanthauzanso zinthu zina. Mwachitsanzo, angatanthauze ulamuliro wa anthu. (Dan. 4:20-22) Angatanthauzenso ulamuliro wa Mulungu kapena Ufumu wake.​—Chiv. 21:1.

Koma Paulo anaona “kumwamba kwachitatu.” Kodi ankatanthauza chiyani? Nthawi zina Baibulo limatchula zinthu zina katatu pofuna kutsindika kapena kutsimikizira. (Yes. 6:3; Ezek. 21:27; Chiv. 4:8) Zikuoneka kuti pamene Paulo ananena za “kumwamba kwachitatu,” ankanena za ulamuliro wapamwamba kwambiri. Iye ankanena za Ufumu wa Mesiya umene olamulira ake ndi Yesu Khristu komanso anthu 144,000. (Onani buku lachingelezi la Insight on the Scriptures, Vol. 1, tsamba 1059, 1062.) Mogwirizana ndi zimene mtumwi Petulo analemba, tikuyembekezera “kumwamba kwatsopano” kumene Mulungu analonjeza.​—2 Pet. 3:13.

Ndiye kodi Paulo ankatanthauza chiyani pamene ananena za ‘paradaiso’?

Mawu oti ‘paradaiso’ angatanthauzenso zinthu zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, angatanthauze (1) paradaiso amene adzakhale padziko lapansi. Zili choncho chifukwa malo amene Mulungu anaika anthu oyambirira anali paradaiso. (2) Angatanthauze mtendere ndiponso mgwirizano umene tidzakhale nawo m’dziko latsopano. (3) Angatanthauzenso zinthu zosangalatsa zakumwamba zomwe zinatchulidwa kuti ‘paradaiso wa Mulungu’ pa Chivumbulutso 2:7.​—Onani Nsanja ya Olonda ya July 15, 2015, tsamba 8, ndime 8.

N’kutheka kuti Paulo ankanena za zinthu zitatu zonsezi pa 2 Akorinto 12:4, pamene ankafotokoza zimene zinamuchitikira.

Mwachidule tingati:

Mawu akuti “kumwamba kwachitatu” otchulidwa pa 2 Akorinto 12:2 ayenera kuti akutanthauza Ufumu wa Mesiya wolamuliridwa ndi Yesu Khristu komanso anthu 144,000, omwe ndi “kumwamba kwatsopano.”​—2 Pet. 3:13.

Ananena kuti “kumwamba kwachitatu” chifukwa chakuti Ufumuwo ndi ulamuliro wapamwamba kwambiri.

‘Paradaiso’ amene Paulo analowa m’masomphenya ayenera kuti akutanthauza (1) paradaiso amene adzakhale padziko lapansi, (2) paradaiso wauzimu amene tidzakhale naye m’tsogolo, yemwe adzakhale padziko lonse ndipo adzakhala wosangalatsa kwambiri kuposa mmene zilili panopa, komanso (3) angatanthauze ‘paradaiso wa Mulungu’ amene ali kumwamba yemwe adzakhale m’dziko latsopano pamodzi ndi zinthu zinazi.

Choncho tingati dziko latsopano lidzapangidwa ndi kumwamba kwatsopano komanso dziko lapansi latsopano. Zinthu zonse zidzakhala zatsopano, kuphatikizapo Ufumu wa kumwamba ndiponso anthu onse amene azidzatumikira Yehova m’paradaiso padziko lapansi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena