Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira February 28, 2011. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya January 3 mpaka February 28, 2011. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 20.
1. Kodi Hezekiya anakhazikitsa ntchito yotani kumayambiriro kwa ulamuliro wake, ndipo tingatengere bwanji chitsanzo chake masiku ano? (2 Mbiri 29:16-18) [w09 6/15 tsamba 9 ndime 13]
2. Kodi lemba la 2 Mbiri 36:21 limatithandiza bwanji kumvetsa kukwaniritsidwa kwa ulosi wa pa Yeremiya 25:8-11? [w06 11/15 tsamba 32 ndime 1-4]
3. Kodi lemba la Ezara 3:1-6 limapereka umboni wotani wa m’Malemba wosonyeza kuti kukhala kwa Yerusalemu zaka 70 ali wabwinja kunatha pa nthawi yake? [w06 1/15 tsamba 19 ndime 2]
4. N’chifukwa chiyani Ezara anakhumudwa atazindikira kuti Aisiraeli akukwatirana ndi anthu amitundu ina? (Ezara 9:1-3) [w06 1/15 tsamba 20 ndime 1]
5. Kodi “anthu otchuka” anali ndani, nanga ndi khalidwe lawo liti limene tiyenera kulipewa? (Neh. 3:5) [w06 2/1 tsamba 10 ndime 1; w86-E 2/15 tsamba 25]
6. Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti Bwanamkubwa Nehemiya ndi chitsanzo chabwino kwa oyang’anira achikhristu? (Neh. 5:14-19) [w06 1/1 tsamba 10 ndime 4]
7. Mofanana ndi Aisiraeli a m’masiku a Nehemiya, kodi tingatani kuti tipewe kunyalanyaza “nyumba ya Mulungu wathu?” (Neh. 10:32-39) [w98 10/15 tsamba 21-22 ndime 12]
8. Kodi kuganizira zimene Nehemiya anachita kungatichititse kudzifunsa mafunso ati? (Neh. 13:31) [w96 9/15 tsamba 17 ndime 3]
9. Kodi Esitere anachita chiwerewere ndi Mfumu Ahasiwero? (Esitere 2:14-17) [w91 1/1 tsamba 31 ndime 6]
10. N’chifukwa chiyani Moderekai anakana kuweramira Hamani? (Esitere 3:2, 4) [w06 3/1 tsamba 9 ndime 5]