Kodi Ndinu Wokonzeka ‘Kudzalandira Dziko Lapansi’?
TONSEFE timayembekezera mwachidwi kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Yesu lakuti: “Odala ndi anthu amene ali ofatsa, chifukwa adzalandira dziko lapansi.” (Mat. 5:5) Odzozedwa adzalandira dziko lapansi pamene adzalamulire limodzi ndi Yesu kumwamba. (Chiv. 5:10; 20:6) Akhristu ambiri masiku ano amayembekezera kudzakhala padzikoli mpaka kalekale, mwamtendere, mosangalala komanso ali angwiro. Kuti zimenezi zidzatheke, iwo adzakhala ndi ntchito yambiri yoti adzagwire. Taganizirani ntchito zitatu izi: Kuyang’anira dziko lapansi, kuthandiza oukitsidwa kupeza zofunika komanso kuwaphunzitsa. Ganizirani zimene mungachite panopa posonyeza kuti mukufunitsitsa kudzagwira nawo ntchitozi.
KODI NDINU WOKONZEKA KUDZAGWIRA NAWO NTCHITO YOSAMALIRA DZIKOLI?
Pamene Yehova analamula anthu kuti ‘adzaze dziko lapansi ndipo aliyang’anire,’ ankatanthauza kuti n’kupita kwa nthawi dziko lonse lapansi lidzakhala malo abwino. (Gen. 1:28) Anthu omwe adzalandire dzikoli adzafunikanso kumvera lamulo limeneli. Popeza kuti munda wa Edeni kulibenso, anthu adzafunika kuyambiranso kukonza dzikoli kuti likhale Paradaiso. Pambuyo pa Aramagedo, padzakhala ntchito yokonza malo omwe panopa awonongeka. Imeneyitu idzakhala ntchito yaikulu kwambiri.
Zimenezi zikutikumbutsa ntchito yaikulu yomwe Aisiraeli anali nayo pamene anabwerera kwawo kuchoka ku Babulo. Dziko lawo linali lopanda wokhalamo kwa zaka 70. Koma Yesaya anali ataneneratu kuti Yehova adzawathandiza kuti akonzenso dzikolo. Ulosiwo unati: “Adzachititsa chipululu chake kukhala ngati Edeni ndi dera lake lachipululu kukhala ngati munda wa Yehova.” (Yes. 51:3) Aisiraeli anakwanitsadi kugwira ntchitoyi. Mofananamo, Yehova adzathandiza amene adzalandire dzikoli kuti akwanitse kulikonza. Palitu zomwe mungachite panopa posonyeza kuti mukufunitsitsa kudzagwira nawo ntchitoyi.
Njira imodzi yomwe mungasonyezere zimenezo ndi kuyesetsa kusamalira pakhomo panu. Muyenera kumachita izi ngakhale pamene oyandikana nawo nyumba sachita zimenezi. Mungathandizenso poyeretsa ndi kukonza Nyumba ya Ufumu yanu kapena Malo a Msonkhano. Ngati zinthu zili bwino kwa inu mungadziperekenso kuti muzigwira nawo ntchito yopereka thandizo pakachitika ngozi. Mukamachita zimenezo mumasonyeza kuti ndinu wokonzeka kuthandiza pamene kukufunika kutero. Mungadzifunse kuti, ‘Kodi pali luso linalake lomwe ndingaphunzire limene ndingadzagwiritse ntchito ndikadzalandira dziko lapansi?’
KODI NDINU WOKONZEKA KUDZASAMALIRA OUKITSIDWA?
Atangoukitsa mwana wamkazi wa Yairo, Yesu ananena kuti am’patse mwanayo chakudya. (Maliko 5:42, 43) Ziyenera kuti sizinali zovuta kusamalira mwana wa zaka 12 ameneyu. Koma taganizirani ntchito yomwe idzakhalepo Yesu akadzakwaniritsa lonjezo lake lakuti “onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu ake ndipo adzatuluka.” (Yoh. 5:28, 29) Ngakhale kuti Baibulo silinena zambiri, n’zoonekeratu kuti anthu oukitsidwa adzafunika kuthandizidwa kupeza chakudya, pokhala komanso zovala. Kodi mungasonyeze ngakhale panopa kuti mukufunitsitsa kudzathandiza? Pali mafunso angapo ofunika kuwaganizira.
Kodi mungachite chiyani panopa posonyeza kuti ndinu wokonzeka kudzalandira dziko lapansi?
Pakaperekedwa chilengezo chakuti woyang’anira dera adzachezera mpingo wanu, kodi mumakonza zoti mudzadye naye chakudya kunyumba kwanu? Atumiki a nthawi zonse omwe utumiki wawo wa pa Beteli wasintha akabwera mumpingo wanu, kapena woyang’anira dera akamaliza utumiki wake, kodi mungawathandize kupeza malo okhala? Ngati msonkhano wachigawo kapena wapadera uchitikire m’dera lanu, kodi mungadzipereke kuti mudzagwire nawo ntchito msonkhanowo usanayambe kapena pambuyo pake, kapenanso mungadzadzipereke kulandira alendo?
KODI NDINU WOKONZEKA KUDZAPHUNZITSA OUKITSIDWA?
Mogwirizana ndi zimene timawerenga pa Machitidwe 24:15, tikuyembekezera kuti anthu mabiliyoni adzaukitsidwa. Ambiri mwa anthuwa adzakhala omwe analibe mwayi wodziwa zambiri zokhudza Yehova. Iwo adzapeza mwayi umenewu akadzaukitsidwa.a Atumiki okhulupirika a Mulungu, omwe amadziwa zambiri adzagwira nawo ntchito yophunzitsayi. (Yes. 11:9) Charlotte yemwe wakhala akulalikira ku Europe, South America, ndi ku Africa akuyembekezera mwachidwi nthawi imeneyi. Mosangalala iye anati: “Ndikuyembekezera mwachidwi kudzaphunzitsa anthu omwe adzaukitsidwe. Ndikamawerenga za munthu winawake amene anakhalapo m’mbuyomu, nthawi zambiri ndimaganiza kuti, ‘Munthu ameneyu akanakhala kuti anadziwa Yehova, moyo wake sukanakhala wotere.’ Ndimafuna kudzauza oukitsidwa zokhudza Yehova komanso kuti zinthu zingamawayendere bwino ngati atamamutumikira.”
Ngakhale atumiki okhulupirika a Yehova, omwe anakhala ndi moyo Yesu asanabwere padzikoli adzakhala ndi zambiri zoti aphunzire. Taganizirani mmene zidzakhalire zosangalatsa kufotokozera Danieli kukwaniritsidwa kwa maulosi omwe analemba koma sankawamvetsa. (Dan. 12:8) Nanga bwanji pa nkhani yothandiza Rute ndi Naomi kudziwa kuti banja lawo linali mumzera wobadwira wa Mesiya? Zidzakhalatu zosangalatsa kugwira ntchito yophunzitsa anthu padziko lonse kulibe mavuto ndiponso zosokoneza zilizonse.
Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife okonzeka kudzagwira nawo ntchitoyi? Njira imodzi ndi kuyesetsa kuwonjezera luso lathu lophunzitsa komanso kugwira nawo nthawi zonse ntchito yophunzitsa anthu yomwe ikuchitika padziko lonse. (Mat. 24:14) Ngakhale kuti simungathe kuchita zambiri panopa chifukwa cha msinkhu wanu kapena zinthu zina, khama lanu lingasonyeze kuti mukufunitsitsa kudzaphunzitsa oukitsidwa.
Choncho funso lofunika kwambiri ndi lakuti, kodi inuyo mukufunitsitsa kudzalandira nawo dziko lapansi? Kodi mumasangalala kuti mudzagwira nawo ntchito yosamalira dzikoli komanso kuthandiza ndi kuphunzitsa oukitsidwa? Mungasonyeze kuti ndinu wokonzeka mukamagwira nawo ntchito zofanana ndi zomwe mudzagwire mukadzalandira dziko lapansi.
a Onani nkhani yakuti, “Kuthandiza Anthu Ambiri Kuti Akhale Olungama” mu Nsanja ya Olonda ya September 2022.