NKHANI YOPHUNZIRA 19
NYIMBO NA. 6 Kumwamba Kumalengeza Ulemerero wa Mulungu
Muzitsanzira Angelo Okhulupirika
“Tamandani Yehova, inu angelo ake onse.”—SAL. 103:20.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi tiona zimene tikuphunzira kwa angelo okhulupirika.
1-2. (a) Kodi anthufe timasiyana bwanji ndi angelo? (b) Kodi timafanana bwanji ndi angelo?
PAMENE Yehova anakuthandizani kuphunzira choonadi, anakukokerani m’banja la atumiki ake osiyanasiyana komanso achikondi omwe akuphatikizapo angelo mamiliyoni ambiri. (Dan. 7:9, 10) Tikamaganizira za angelo, nthawi zambiri timaganizira za kusiyana komwe kulipo pakati pa anthufe ndi iwowo. Mwachitsanzo, iwo akhala alipo kwanthawi yaitali kuposa ife. (Yobu 38:4, 7) Iwo ndi amphamvu kwambiri kuposa anthufe. Ndipo mosiyana ndi anthufe omwe si angwiro, iwo ndi oyera komanso olungama.—Luka 9:26.
2 Ngakhale kuti pali kusiyana kumeneku, timafanana nawo pa zinthu zambiri. Mwachitsanzo, mofanana ndi angelo, timatha kutsanzira makhalidwe a Yehova komanso timakhala ndi ufulu wosankha. Tilinso ndi mayina, makhalidwe komanso zochita zosiyanasiyana potumikira Yehova ndiponso tili ndi mtima wofuna kulambira Mlengi wathu.—1 Pet. 1:12.
3. Kodi tingaphunzire chiyani kwa angelo okhulupirika?
3 Popeza kuti timafanana ndi angelo pa zinthu zambiri, chitsanzo chawo chingatilimbikitse komanso kutithandiza. Ndipotu tingaphunzire zambiri kuchokera kwa iwo. Munkhaniyi tiona zimene tingachite kuti tizitsanzira kudzichepetsa kwa angelo okhulupirikawa, kukonda kwawo anthu komanso zimene amayesetsa kuchita kuti mpingo ukhale woyera.
ANGELO NDI ODZICHEPETSA
4. (a) Kodi angelo amasonyeza bwanji kudzichepetsa? (b) N’chifukwa chiyani angelo amadzichepetsa? (Salimo 89:7)
4 Angelo okhulupirika ndi odzichepetsa. Ngakhale kuti iwo amadziwa zambiri, ndi amphamvu komanso anzeru, amamvera malangizo a Yehova. (Sal. 103:20) Akamagwira ntchito zimene apatsidwa, iwo samadzitama chifukwa cha zimene achita kapena kudzionetsera ndi mphamvu zimene ali nazo. Amasangalala kuchita zimene Mulungu akufuna ngakhale kuti sangadziwike ndi mayina awo kuti ndi amene achita zinthuzo.a (Gen. 32:24, 29; 2 Maf. 19:35) Iwo samalola kulandira ulemerero umene umafunika kupita kwa Yehova. N’chifukwa chiyani angelo ali odzichepetsa kwambiri? Iwo amakonda Yehova komanso kumulemekeza kwambiri.—Werengani Salimo 89:7.
5. Kodi mngelo wina anasonyeza bwanji kudzichepetsa popereka malangizo kwa Yohane? (Onaninso chithunzi.)
5 Tiyeni tione nkhani imodzi yosonyeza kuti angelo ndi odzichepetsa. Cha m’ma 96 C.E., mngelo wina amene dzina lake silikudziwika anaonetsa mtumwi Yohane masomphenya odabwitsa. (Chiv. 1:1) Kodi Yohane anatani ataona masomphenyawo? Iye ankafuna kulambira mngeloyo. Koma mwamsanga mngelo wokhulupirikayo anamuletsa, ndipo anati: “Samala! Usachite zimenezo! Inetu ndangokhala kapolo mnzako ndi wa abale ako. . . . Lambira Mulungu.” (Chiv. 19:10) Apatu mngeloyu anadzichepetsa kwambiri. Iye sankafuna kupatsidwa ulemu kapena kutamandidwa. Nthawi yomweyo anauza Yohane kuti ayenera kulambira Mulungu. Pa nthawi imodzimodziyo, iye sankaona Yohane ngati munthu wosafunika kwenikweni. Ngakhale kuti mngeloyo anatumikira Yehova kwa zaka zambiri komanso anali wamphamvu kuposa Yohane, iye anadzichepetsa n’kunena kuti mtumwiyu anali kapolo mnzake. Ndipo ngakhale kuti mngeloyo ankafunika kudzudzula Yohane, sanamukalipire mtumwi wokalambayu. M’malomwake analankhula naye mokoma mtima ndipo anazindikira kuti zimene Yohane anaonazo zinamudabwitsa kwambiri.
Mngelo anasonyeza kudzichepetsa polankhula ndi Yohane (Onani ndime 5)
6. Kodi tingatsanzire bwanji kudzichepetsa kwa angelo?
6 Kodi tingatsanzire bwanji angelo pa nkhani ya kudzichepetsa? Ifenso tikapatsidwa zochita sitiyenera kudzitamandira kapena kufuna kupatsidwa ulemu chifukwa cha zimene takwanitsa kuchita. (1 Akor. 4:7) Kuwonjezera pamenepo, sitiyenera kumadziona kukhala oposa ena chifukwa chakuti tatumikira Yehova kwa nthawi yaitali kapenanso tili ndi maudindo ena. Ndipotu tikamachita zambiri potumikira Yehova m’pamenenso timafunika kumadziona ngati wamng’ono. (Luka 9:48) Mofanana ndi angelo timafuna kutumikira ena. Sitimafuna kuchititsa ena kuti aziona kuti ndife ofunika kwambiri.
7. Kodi tingasonyeze bwanji kudzichepetsa tikamapereka malangizo kapena kudzudzula munthu?
7 Nthawi zina timafunika kupereka malangizo amphamvu. Koma mofanana ndi mngelo amene anadzudzula Yohane mokoma mtima, ifenso tingapereke malangizo amphamvu popanda kukhumudwitsa munthu. Ngati sitimadziona kukhala oposa ena, tingapereke malangizo ochokera m’Baibulo mwaulemu komanso mwachikondi.—Akol. 4:6.
ANGELO AMAKONDA ANTHU
8. (a) Mogwirizana ndi Luka 15:10, kodi angelo amasonyeza bwanji kuti amakonda anthu? (b) Kodi angelo amathandiza bwanji pa ntchito yolalikira? (Onaninso chithunzi .)
8 Angelo samanyalanyaza zimene zimachitikira anthu kapenanso kumaganiza kuti ndife osafunika. Iwo amakonda anthu ndipo amasangalala wochimwa akalapa n’kubwerera kwa Yehova kapena munthu akasintha njira zake n’kuyamba kuphunzira choonadi. (Werengani Luka 15:10.) Iwo amatithandizanso tikamagwira ntchito yolalikira za Ufumu. (Chiv. 14:6) Ngakhale kuti iwo salalikira mwachindunji kwa anthu, angatsogolere wofalitsa kwa munthu amene akufuna kuphunzira za Yehova. Komabe si nthawi zonse pamene tinganene motsimikiza kuti angelo atitsogolera kwa munthu winawake. Ndipotu Yehova angagwiritse ntchito njira zina, monga kupereka mzimu wake kuti uthandize anthu amene akufuna kumudziwa kapena kutsogolera atumiki ake. (Mac. 16:6, 7) Komabe iye amagwiritsa ntchito kwambiri angelo ake potithandiza pa ntchito yolalikira. Choncho tikamalalikira uthenga wabwino tingakhale otsimikiza kuti angelo ake adzatithandiza.—Onani bokosi lakuti “Mapemphero Awo Anayankhidwa.”b
Banja langomaliza kumene kulalikira pamalo opezeka anthu ambiri. Pobwerera kunyumba mlongoyo akuona mayi wina yemwe akuoneka kuti ali ndi nkhawa. Kenako akupita kukamulimbikitsa mayiyo. (Onani ndime 8)
9. Kodi tingatsanzire bwanji angelo pa nkhani yokonda anthu?
9 Kodi tingatsanzire bwanji angelo n’kumakonda anthu? Tikamva chilengezo chakuti wina wabwezeretsedwa, tizisangalala ngati mmene angelo amachitira. Tizichita zonse zimene tingathe pomulandira ndi manja awiri komanso kumutsimikizira kuti timamukonda. (Luka 15:4-7; 2 Akor. 2:6-8) Tingatsanzirenso angelo pochita zimene tingathe pa ntchito yolalikira. (Mlal. 11:6) Angelo amatithandiza tikamalalikira uthenga wabwino choncho ifenso tizithandiza abale ndi alongo athu akamagwira ntchitoyi. Mwachitsanzo, tingakonze zoti tilalikire ndi wofalitsa amene sakudziwa zambiri. Tingathandizenso abale ndi alongo achikulire kapenanso amene akudwala kuti nawonso azilalikira.
10. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Sara?
10 Koma bwanji ngati sitingathe kuchita zambiri chifukwa cha mmene zinthu zilili pa moyo wathu? Tingathe kupezabe njira yakuti tizigwirira ntchito limodzi ndi angelo polalikira. Chitsanzo ndi mlongo wina wa ku India dzina lake Sara.c Atachita upainiya kwa zaka 20, Sara anadwala ndipo ankangokhala chigonere. Zimenezi zinamukhumudwitsa ndipo n’zomveka. Koma chifukwa chakuti ankawerenga Baibulo nthawi zonse komanso abale ndi alongo ake ankamuthandiza mwachikondi, pang’ono ndi pang’ono Sara anayambiranso kusangalala. Komabe iye ankafunika kupeza njira zatsopano zolalikirira mogwirizana ndi mmene zinthu zinalili pa nthawiyo. Popeza kuti sankatha kukhala pansi kuti alembe makalata, ankangolalikira pafoni. Ankati akaimbira anthu foni pa ulendo wobwereza, iwo ankamuuza za anthu enanso omwe akufuna kuphunzira. Pa miyezi yochepa chabe Sara anali ndi maphunziro a Baibulo okwana 70, omwe sakanatha kuwaphunzitsa. Choncho iye anapereka ena mwa anthuwo kwa abale ndi alongo mumpingo. Panopa ambiri mwa ophunzirawo amapezeka pamisonkhano. Angelo ayenera kuti amasangalala kwambiri kugwira ntchito ndi abale ndi alongo ngati Sara, omwe amachita zonse zomwe angathe pa ntchito yolalikira.
ANGELO AMAPIRIRA
11. Kodi angelo okhulupirika asonyeza bwanji kupirira?
11 Angelo okhulupirika ndi zitsanzo zabwino kwambiri pa nkhani ya kupirira. Iwo akhala akupirira zinthu zopanda chilungamo komanso zoipa kwa zaka masauzande ambiri. Iwo anaona Satana ndi angelo ena ambiri omwe ankatumikira nawo limodzi akuukira Yehova. (Gen. 3:1; 6:1, 2; Yuda 6) Baibulo limatiuza za mngelo wina wokhulupirika amene analimbana ndi chiwanda champhamvu. (Dan. 10:13) Kuwonjezera pamenepo, kwa zaka zambiri angelo akhala akuona anthu ochepa okha akusankha kulambira Yehova. Ngakhale zili choncho, angelo okhulupirikawa akupitirizabe kutumikira Yehova mosangalala komanso mwakhama. Iwo amadziwa kuti pa nthawi yoyenera Yehova adzachotsa zinthu zonse zopanda chilungamo.
12. N’chiyani chingatithandize kuti tizipirira?
12 Kodi tingatsanzire bwanji angelo pa nkhani ya kupirira? Mofanana ndi angelo, ifenso tingakumane ndi zinthu zopanda chilungamo kapena kutsutsidwa. Koma timakhulupirira kuti pa nthawi yoyenera Yehova adzachotsa zoipa zonse. Choncho mofanana ndi angelo okhulupirika, ‘sitisiya kuchita zabwino.’ (Agal. 6:9) Komanso Mulungu amalonjeza kuti adzatithandiza kupirira. (1 Akor. 10:13) Tizipempha Yehova kuti atipatse mzimu wake womwe ungatithandize kukhala oleza mtima ndiponso osangalala. (Agal. 5:22; Akol. 1:11) Koma bwanji ngati mukutsutsidwa? Muzidalira kwambiri Yehova ndipo musamatekeseke. Nthawi zonse adzakuthandizani komanso kukupatsani mphamvu.—Aheb. 13:6.
ANGELO AMATHANDIZA KUTI MPINGO UKHALE WOYERA
13. Kodi angelo apatsidwa ntchito yapadera iti m’masiku otsiriza ano? (Mateyu 13:47-49)
13 M’masiku otsiriza ano, Yehova wapereka kwa angelo ntchito yolalikira. (Werengani Mateyu 13:47-49.) Ntchitoyi imachititsa kuti anthu ambiri achite chidwi ndi uthenga wabwino. Ena mwa anthuwa amasintha mpaka kufika pokhala Akhristu oona, pomwe ena sasintha. Angelo apatsidwa ntchito yoti ‘achotse oipa pakati pa olungama.’ Izi zikutanthauza kuti ntchito yawo ikuthandiza kuti mpingo ukhale woyera. Koma sizikutanthauza kuti aliyense amene wasiya kusonkhana nafe pa zifukwa zosiyanasiyana sangabwerere. Sizitanthauzanso kuti mumpingo mudzakhala mopanda mavuto. Koma tingakhale otsimikiza kuti angelo akugwira ntchito mwakhama pothandiza kuti mpingo ukhale woyera.
14-15. Kodi tingatsanzire bwanji angelo pankhani yothandiza kuti mpingo ukhale woyera? (Onaninso zithunzi.)
14 Kodi tingatsanzire bwanji angelo pothandiza kuti mpingo ukhale woyera? Tingachite zimenezo poyesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino komanso kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Timayesetsa kuteteza mtima wathu posankha bwino anthu ocheza nawo komanso kupewa chilichonse chimene chingatisokoneze. (Sal. 101:3) Tingachite bwinonso kuthandiza Akhristu anzathu kuti akhalebe okhulupirika kwa Yehova. Mwachitsanzo, kodi tingatani ngati titamva kuti Mkhristu mnzathu wachita tchimo lalikulu? Chifukwa chomukonda tikhoza kumulimbikitsa kuti auze akulu. Ngati sanakanene, ifeyo tikhoza kuwauza akuluwo. Timafuna kuti Mkhristu aliyense amene ubwenzi wake ndi Yehova wayamba kusokonekera athandizidwe mwamsanga.—Yak. 5:14, 15.
15 N’zomvetsa chisoni kuti anthu ena amene amachita machimo akuluakulu amachotsedwa. Zikatero timasiya ‘kugwirizana’ nawo.d (1 Akor. 5:9-13) Zimenezi zimathandiza kuti mpingo ukhale woyera. Ndipotu tikasiya kucheza nawo timawasonyeza kukoma mtima. Kutsatira malangizo pa nkhaniyi kungawathandize kuganiza zobwerera kwa Yehova. Ndipo akabwerera, timasangalala limodzi ndi Yehova komanso angelo.—Luka 15:7.
Kodi tingatani ngati titadziwa kuti Mkhristu mnzathu wachita tchimo lalikulu? (Onani ndime 14)e
16. Kodi inuyo mudzayesetsa kutsanzira angelo m’njira iti?
16 Ndi mwayi waukulu kuti Yehova watilola kuti tiphunzire zokhudza angelo komanso makhalidwe awo abwino monga kudzichepetsa, kukonda anthu, kupirira komanso kuthandiza kuti mpingo ukhale woyera. Tikamatsanzira angelo okhulupirika, ifenso tidzakhala m’banja la atumiki ake mpaka kalekale.
NYIMBO NA. 123 Tizigonjera Mulungu Mokhulupirika
a Pali angelo mamiliyoni ambiri, koma amene amatchulidwa m’Baibulo ndi awiri okha, Mikayeli ndi Gabirieli.—Dan. 12:1; Luka 1:19.
b Mungapeze zitsanzo zina mu wp17.5 3 komanso bt mutu 7, ndime 17.
c Mayina asinthidwa.
d Monga anafotokozera mu Lipoti la Bungwe Lolamulira la Nambala 2 la 2024, ngati munthu wochotsedwa wafika pamisonkhano yampingo, wofalitsa angasankhe mogwirizana ndi chikumbumtima chake kupereka moni wachidule kapena kumulandira.
e MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo akulimbikitsa mnzake kuti akalankhule ndi akulu. Patapita nthawi, mnzakeyo atalephera kukalankhula ndi akuluwo, iye wapita kukawauza zomwe zachitika.