MFUNDO ZOTHANDIZA POPHUNZIRA
Muzikonzekeretsa Mtima Wanu
Tikamaphunzira Baibulo timafuna kuti maganizo a Yehova akhazikike mumtima mwathu. Ezara anatipatsa chitsanzo pomwe “anakonzekeretsa mtima wake kuti aphunzire Chilamulo cha Yehova.” (Ezara 7:10) Kodi tingamutsanzire bwanji pa nkhaniyi?
Muzipemphera. Nthawi zonse musanayambe kuphunzira muzipemphera. Muzimupempha Yehova kuti akuthandizeni kumvetsa komanso kugwiritsa ntchito zimene mukufuna kuphunzirazo.—Sal. 119:18, 34.
Muzikhala odzichepetsa. Mulungu amabisira choonadi anthu onyada omwe amadalira nzeru zawo. (Luka 10:21) Komanso musamafufuze n’cholinga chofuna kugometsa anthu ena ndi zomwe mukudziwa. Modzichepetsa, muzisintha kaganizidwe kanu mukaona kuti sikakugwirizana ndi kaganizidwe ka Mulungu.
Muzimvetsera nyimbo ya Ufumu. Nyimbo zili ndi mphamvu zotha kukonzekeretsa mtima wathu tikamafuna kulambira. Choncho kumvetsera nyimbo ya Ufumu musanayambe kuphunzira kungakuthandizeni kukonzekeretsa mtima wanu.