Kodi Mukudziwa?
Kodi ansembe a pakachisi ankatani ndi magazi a nyama zomwe zaperekedwa nsembe paguwa?
CHAKA chilichonse, ansembe ku Yerusalemu ankapereka nsembe nyama zambirimbiri paguwa la pakachisi. Wolemba mbiri wina dzina lake Josephus ananena kuti pa tsiku la Pasika nkhosa zoposa 250,000 zinkaperekedwa nsembe, zomwe zinkachititsa kuti paguwalo pakhale magazi ambiri. (Lev. 1:10, 11; Num. 28:16, 19) Ndiye kodi magazi onsewo ankapita kuti?
Ofufuza zinthu zakale, apeza kuti kachisi wa Herode yemwe ankagwira ntchito mpaka pamene kachisiyo anawonongedwa mu 70 C.E, anali ndi ngalande yaikulu. Zikuoneka kuti ngalandeyo ndi yomwe munkadutsa magazi ochokera paguwa lansembe.
Tiyeni tione zinthu ziwiri zomwe zinkachititsa kuti paguwalo pazikhala pa ukhondo:
Maenje omwe anali kunsi kwa guwa lansembe: Buku lina limene linalembedwa chitadutsa chaka cha 200 C.E., lomwe limafotokoza malamulo ndi miyambo ya Chiyuda, linanena za ngalande yomwe inali paguwa la nsembe. Bukulo linati: “Kukona ya kum’mwera chakumadzulo kwa guwa la nsembe kunali maenje awiri . . . komwe magazi amene athiridwa paguwa ankadutsa limodzi ndi madzi omwe ankatsukira paguwapo kenako n’kukatuluka kupita kumtsinje wa Kidironi.”
Zimene akatswiri ofufuza zinthu zakale apeza zikusonyeza kuti zimene bukuli linanena ndi zoona. Buku lina lofotokoza mbiri ya Chiyuda linanena kuti akatswiri anapeza ngalande pafupi ndi kachisi zomwe n’kutheka kuti zinkagwiritsidwa ntchito pochotsa magazi a nsembe nyama zomwe zaperekedwa nsembe komanso madzi ochoka paguwa.—The Cambridge History of Judaism
Madzi okwanira: Ansembe ankafunika madzi ambiri kuti paguwapo komanso ngalandeyo zizikhala zaukhondo. Kuti ansembewo agwire ntchito yofunikayi, ankapeza madzi kuchokera mumzinda. Madziwo ankachokera m’madamu ndi m’zitsime ndipo ankadutsa m’ngalande popita kukachisi. Katswiri wina wofukula zinthu zakale dzina lake Joseph Patrich ananena kuti: “Pa nthawiyo panalibenso kachisi wina yemwe anali ndi njira yabwino kwambiri ngati imeneyi yotumizira madzi otsukira paguwa komanso ngalande zake.”