Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yb17 tsamba 169-170
  • Anthu Ambiri Olankhula Chikadishi Akuphunzira Choonadi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anthu Ambiri Olankhula Chikadishi Akuphunzira Choonadi
  • Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2017
Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2017
yb17 tsamba 169-170
Mlongo akuphunzira Baibulo ndi mayi wina m’Chikudishi

GEORGIA

Anthu Ambiri Olankhula Chikadishi Akuphunzira Choonadi

MAYI wina dzina lake Gulizar anati: “Ndimathokoza Yehova chifukwa cholola kuti ndizimva uthenga wabwino m’chinenero changa.”

A Gulizar anasonkhana ndi a Mboni za Yehova kwa zaka 8, koma anabatizidwa atachita msonkhano wa m’chinenero chawo cha Chikadishi. Mayi ameneyu ndi mmodzi mwa anthu achikadi omwe aphunzira Baibulo ku Georgia zaka zingapo zapitazi. Tiyeni tione zinthu zina zokhudza anthu a mtundu umenewu.

Anthu a mtundu wachikadi akhala akupezeka ku Middle East kuyambira kale kwambiri. Akatswiri ena amaganiza kuti anthu a mtunduwu anachokera ku mtundu wakale wa Amedi, womwe umatchulidwa m’Baibulo. (2 Maf. 18:11; Mac. 2:9) Chinenero chawo chili m’gulu la zinenero za Chiirani.

Masiku ano, anthu ambiri achikadi akupezeka m’mayiko osiyanasiyana monga ku Armenia, Iran, Iraq, Syria komanso Turkey. M’dziko la Georgia muli Akadi pafupifupi 20,000. Anthuwa amaopa Mulungu kwambiri komanso amakonda zopemphera.

Ku Georgia kuli ofalitsa okwana 500 achikadi ndipo kuli mipingo itatu yachikadishi. N’zosangalatsa kwambiri kuti m’chaka cha 2014, ku Tbilisi kunachitika msonkhano woyamba wa m’Chikadishi. Pamsonkhanowu panali alendo ochokera ku Armenia, Germany, Turkey ndi Ukraine.

Ana olankhula Chikadishi akusangalala ndi mavidiyo a Kalebe ndi Sofiya
    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena