Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yb17 tsamba 171
  • Akhristu Oona Amasonyeza Chikondi Chenicheni

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Akhristu Oona Amasonyeza Chikondi Chenicheni
  • Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2017
Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2017
yb17 tsamba 171

GEORGIA

Akhristu Oona Amasonyeza Chikondi Chenicheni

KAMTSIKANA kena dzina lake Sanel kasanabadwe, madokotala anauza makolo ake kuti mwanayo adzabadwa ndi vuto lalikulu. Ananenanso kuti n’zokayikitsa ngati angadzakhale ndi moyo. Mwanayo atangobadwa, ankafunika kupangidwa opaleshoni. Makolo ake ankakhala ku Abkhazia, dziko lomwe linaima palokha kuchoka ku dziko la Georgia. Makolo a Sanel sanapeze dokotala amene akanalola kuchita opaleshoni mwanayu popanda kumuika magazi m’dziko lawolo.

Makolowa anadziwitsa Komiti Yolankhulana ndi Achipatala za nkhaniyi.a Mwamwayi, abale a m’komitiyi anapeza dokotala yemwe akanachita opaleshoni mwanayu kulikulu la dziko la Georgia, ku Tbilisi. Koma pa nthawiyi, mayi a Sanel sankapeza bwino moti sakanakwanitsa kupita nawo ku Tbilisi. Choncho, anakonza zoti agogo ake awiri, amene ndi a Mboni za Yehova, apite ndi mwanayu ku Tbilisi.

Opaleshoni ya Sanel inayenda bwino kwambiri. Pasanapite nthawi yaitali opaleshoniyi itachitika, agogo ake anati: “Tinakhala m’chipatala kwa masiku 20. Pa nthawi imeneyi, abale ndi alongo a m’dziko la Georgia ankabwera kudzationa ndipo anatithandiza kwambiri. Zimenezi zinatikhudza zedi chifukwa tinali titawerengapo zokhudza chikondi chimene abale ndi alongo amachitira anzawo omwe sakuwadziwa. Koma pa nthawiyi tinaona zimenezi zikutichitikira.”

a Abale omwe ali m’Komiti Yolankhulana ndi Achipatala m’dziko la Georgia anapeza madokotala okwana 250 omwe amalola kuchita opaleshoni popanda kuika magazi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena