Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Yohane
21 Pambuyo pa izi, Yesu anaonekelanso kwa ophunzilawo ku nyanja ya Tiberiyo. Kuonekela kwake kunali motele. 2 Kumeneko kunali Simoni Petulo, Thomasi (wochedwa Didimo), Natanayeli wa ku Kana wa ku Galileya, ana a Zebedayo, ndi ophunzila ake ena awili, onsewa anali pamodzi. 3 Simoni Petulo anauza anzakewo kuti: “Ine ndikupita kukapha nsomba.” Iwo anamuuza kuti: “Ifenso tipita nawe.” Iwo anapita kukakwela bwato n’kupita naye, koma usiku umenewo sanaphe kalikonse.
4 Pamene kunali kuca, Yesu anaimilila m’mbali mwa nyanja, koma ophunzilawo sanazindikile kuti anali Yesu. 5 Yesu anawafunsa kuti: “Ana inu, kodi muli ndi cakudya ciliconse?”* Iwo anayankha kuti: “Ayi!” 6 Iye anawauza kuti: “Ponyani ukonde wanu kudzanja lamanja la bwatolo ndipo mupezako kanthu.” Iwo anaponyadi ukondewo, koma sanakwanitse kuuguzila m’bwatolo cifukwa ca kuculuka kwa nsomba. 7 Kenako, wophunzila amene Yesu anali kumukonda anauza Petulo kuti: “Ndi Ambuye!” Ndiyeno Simoni Petulo atamva kuti ndi Ambuye, anavala covala cake cakunja, cifukwa anali malisece,* ndipo analumphila m’nyanja. 8 Koma ophunzila enawo anabwela m’bwato laling’ono akukoka ukonde wodzala ndi nsomba, cifukwa sanali kutali kwenikweni ndi mtunda, panali cabe mtunda wa mamita pafupifupi 90.
9 Atafika kumtunda anaona moto wamalasha, ndipo pa motowo panali nsomba ndi mkate. 10 Yesu anawauza kuti: “Bweletsani zina mwa nsomba zimene mwangopha kumenezo.” 11 Conco Simoni Petulo anakwela m’bwatomo n’kukokela ku mtunda ukonde wodzala ndi nsomba zikuluzikulu zokwana 153. Koma ngakhale kuti zinali zoculuka zedi, ukondewo sunang’ambike. 12 Yesu anawauza kuti: “Bwelani mudye cakudya cam’mawa.” Panalibe ngakhale wophunzila mmodzi amene analimba mtima kumufunsa kuti: “Kodi ndinu ndani?” cifukwa iwo anadziwa kuti ndi Ambuye. 13 Yesu anatenga mkate n’kuwapatsa, ndipo anacitanso cimodzimodzi ndi nsomba. 14 Aka kanali kacitatu Yesu kuonekela kwa ophunzilawo pambuyo pakuti waukitsidwa kwa akufa.
15 Atatsiliza kudya cakudya ca m’mawaco, Yesu anafunsa Simoni Petulo kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi umandikonda ine kuposa izi?” Iye anamuyankha kuti: “Inde Ambuye, inunso mukudziwa kuti ndimakukondani kwambili.” Iye anamuuza kuti: “Dyetsa ana a nkhosa anga.” 16 Yesu anamufunsanso kaciwili kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi umandikonda ine?” Iye anamuyankha kuti: “Inde Ambuye, inunso mudziwa kuti ndimakukondani kwambili.” Yesu anamuuza kuti: “Weta ana a nkhosa anga.” 17 Iye anamufunsanso kacitatu kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi umandikonda ine?” Petulo anamva cisoni kuti anafunsidwa kacitatu kuti: “Kodi ine umandikonda kwambili?” Conco iye anamuuza kuti: “Ambuye, inu mudziwa zonse. Mudziwa kuti ndimakukondani kwambili.” Yesu anamuuza kuti: “Dyetsa ana a nkhosa anga. 18 Ndithudi ndikukuuza, pamene unali mnyamata unali kudzivalika wekha n’kupita kumene unali kufuna. Koma ukadzakalamba, udzatambasula manja ako, ndipo munthu wina adzakuvalika, ndipo adzakunyamula ndi kukupeleka kumene iwe sufuna.” 19 Iye anakamba zimenezi poonetsa mtundu wa imfa imene Petulo adzalemekeza nayo Mulungu. Atanena zimenezi, anamuuza kuti: “Pitiliza kunditsatila.”
20 Petulo anaceuka, ndipo anaona wophunzila amene Yesu anali kumukonda akuwatsatila. Wophunzilayu ndi uja amene anatsamila pacifuwa ca Yesu pa cakudya camadzulo n’kumufunsa kuti: “Ambuye, ndani amene akufuna kukupelekani?” 21 Ndiyeno Petulo atamuona, anafunsa Yesu kuti: “Ambuye, nanga n’ciyani cidzacitika kwa uyu?” 22 Yesu anamuuza kuti: “Ngati ine ndifuna kuti akhalebe ndi moyo mpaka n’tabwela, kodi iwe zikukhudza bwanji? Iwe ungopitiliza kunditsatila.” 23 Conco mbili imene inamveka pakati pa abale inali yakuti wophunzilayu sadzafa. Koma Yesu sanakambe kuti wophunzilayu sadzafa ayi. Iye anati: “Ngati ine ndifuna kuti akhalebe ndi moyo mpaka n’tabwela, kodi zikukhudza bwanji?”
24 Wophunzilayu ndi amene akucitila umboni zinthu zimenezi. Iye ndiye analemba zinthu zimenezi, ndipo tidziwa kuti umboni wake ndi woona.
25 Palinso zinthu zina zambili zimene Yesu anacita. Zinthu zimenezi zikanalembedwa mwatsatanetsatane, ndiona kuti mipukutu yolembedwayo sikanakwana padziko.