Kwa Aroma
14 Landilani munthu amene ali ndi cikhulupililo cofooka, koma musamaweluze amene ali ndi maganizo osiyana ndi anu.* 2 Wina amakhala ndi cikhulupililo cakuti angadye ciliconse, koma munthu wofooka amadya zamasamba zokha. 3 Munthu amene amadya ciliconse, asamaone munthu amene amasala zakudya zina kukhala wotsika. Ndipo amene amasala zakudya zina, asaweluze munthu amene amadya ciliconse, cifukwa nayenso analandilidwa ndi Mulungu. 4 Kodi iwe ndiwe ndani kuti uweluze wanchito wa mwiniwake? Mbuye wake ndiye woyenela kumuweluza kuti ndi wolakwa kapena ndi wosalakwa, cifukwa Yehova ndiye angamuthandize kuti zimuyendele bwino.
5 Wina amaona tsiku lina kuti liposa linzake, koma wina amaona kuti masiku onse n’cimodzimodzi. Munthu aliyense atsimikize kuti zimene akukhulupilila n’zovomelezeka. 6 Amene amasunga tsiku amalisunga kuti alemekeze Yehova. Komanso amene amadya ciliconse, amadya kuti alemekeze Yehova cifukwa amayamika Mulungu. Amene amasala zakudya zina, amatelo kuti alemekeze Yehova, ndipo amayamika Mulungu. 7 Kukamba zoona, palibe aliyense wa ife amene amakhala ndi moyo kuti adzilemekeze yekha, ndipo palibe amene amafa kuti adzilemekeze yekha. 8 Pakuti tikakhala ndi moyo, timakhalila moyo Yehova, ndipo tikafa, timafela Yehova. Conco kaya tikhale ndi moyo kapena tife, ndife ake a Yehova. 9 Ndiye cifukwa cake Khristu anafa n’kukhalanso ndi moyo, kuti akhale Ambuye wa akufa komanso amoyo.
10 Koma n’cifukwa ciyani umaweluza m’bale wako? Kapenanso n’cifukwa ciyani umapeputsa m’bale wako? Pakuti tonsefe tidzaimilila patsogolo pa mpando woweluzila wa Mulungu. 11 Cifukwa Malemba amati: “‘Na pali ine Mulungu wamoyo,’ watelo Yehova, ‘bondo lililonse lidzandigwadila, pakuti lilime lililonse lidzavomeleza poyela kuti ndine Mulungu.’” 12 Cotelo, aliyense wa ife adzayankha yekha kwa Mulungu.
13 Pa cifukwa cimeneci, tisamaweluzane, m’malomwake tsimikizani mtima kuti simuikila m’bale wanu cokhumudwitsa kapena copunthwitsa. 14 Ndikudziwa komanso ndikukhulupilila mwa Ambuye Yesu kuti palibe cakudya cimene ndi codetsedwa pa ico cokha. Koma ngati munthu winawake akuona kuti cinacake ndi codetsedwa, ndiye kuti ndi codetsedwa kwa iye. 15 Ngati m’bale wako akukhumudwa cifukwa ca cakudya, ndiye kuti sukumuonetsanso cikondi. Musawononge munthu amene Khristu anamufela cifukwa ca zakudya zanu. 16 Conco musalole kuti anthu azikamba zoipa pa zabwino zimene mumacita. 17 Cifukwa pa nkhani ya Ufumu wa Mulungu, cofunika kwambili si kudya kapena kumwa ayi, koma cilungamo, mtendele, ndi cimwemwe, zimene zimabwela mwa mzimu woyela. 18 Aliyense wotumikila Khristu mwa njila imeneyi ndi wovomelezeka kwa Mulungu, ndipo anthu amakondwela naye.
19 Conco, tiyeni tiziyesetsa kucita zinthu zobweletsa mtendele, komanso zolimbikitsana wina ndi mnzake. 20 Lekani kuwononga nchito ya Mulungu cabe cifukwa ca zakudya. N’zoona kuti zakudya zonse n’zoyela, koma n’kulakwa* kudya zakudyazo ngati wina akukhumudwa nazo. 21 Si bwino kudya nyama kapena kumwa vinyo, kapena kucita ciliconse cimene cimakhumudwitsa m’bale wako. 22 Cikhulupililo cimene uli naco, ukhale naco pakati pa iwe ndi Mulungu. Munthu amakhala wacimwemwe ngati sakudziimba mlandu pa zimene wasankha kucita. 23 Ngati munthu amadya koma amakayikila, ndiye kuti watsutsidwa kale, cifukwa sakudya mogwilizana ndi cikhulupililo. Ndithudi, ciliconse cosagwilizana ndi cikhulupililo ndi chimo.