Kwa Aroma
13 Munthu aliyense azimvela aulamulilo waukulu, pakuti palibe ulamulilo umene ungakhalepo pokhapo ngati Mulungu waulola. Olamulila amene alipo ali pa maudindo awo osiyanasiyana m’mphamvuwo mololedwa ndi Mulungu. 2 Conco aliyense amene amatsutsana ndi ulamulilo, amatsutsana ndi zimene Mulungu anakonza. Amene amatsutsana ndi zimene Mulungu anakonza adzadzibweletsela ciweluzo. 3 Cifukwa olamulila amenewa amaopsa ngati umacita zoipa, osati ngati umacita zabwino. Kodi ukufuna kuti usamaope olamulila? Pitiliza kucita zabwino, ndipo olamulilawo adzakutamanda. 4 Iwo ndi mtumiki wa Mulungu kuti zinthu zizikuyendela bwino. Koma ngati ucita zoipa, uzicita mantha cifukwa iwo sanyamula lupanga pacabe. Olamulilawo ndi mtumiki wa Mulungu amene amaonetsa mkwiyo* wa Mulungu kwa munthu wocita zoipa.
5 Conco pali cifukwa comveka coti muziwagonjela, osati cabe cifukwa coopa mkwiyowo, koma cifukwanso ca cikumbumtima canu. 6 N’cifukwa cake mumakhomanso misonkho, cifukwa iwo ndi anchito a Mulungu otumikila anthu, ndipo amakwanilitsa colingaci nthawi zonse. 7 Pelekani kwa onse zimene amafuna.* Wofuna msonkho m’patseni msonkho. Wofuna ndalama ya ciphaso m’patseni ndalama ya ciphaso. Wofuna kuopedwa muopeni. Wofuna kupatsidwa ulemu m’patseni ulemu.
8 Musakhale ndi nkhongole iliyonse kwa munthu aliyense, kupatulapo nkhongole ya kukondana wina ndi mnzake, pakuti amene amakonda munthu mnzake amakwanilitsa lamulo. 9 Cifukwa malamulo onena kuti, “Usacite cigololo, usaphe munthu, usabe, usasilile mwansanje,” ndi lamulo lina lililonse limene lilipo, cidule cake n’cakuti: “Uzikonda munthu mnzako mmene umadzikondela wekha.” 10 Cikondi sicilimbikitsa munthu kucita mnzake zoipa. Conco cikondi cimalimbikitsa munthu kukwanilitsa lamulo.
11 Ndipo muzicita zimenezi cifukwa nyengo ino mukuidziwa, kuti tili kale m’nthawi yofunika kuti muuke ku tulo, cifukwa palipano cipulumutso cathu cayandikila kwambili kuposa pa nthawi imene tinakhala okhulupilila. 12 Usiku watsala pang’ono kutha, ndipo masana ayandikila. Conco tiyeni tivule n’kutaya nchito za mdima, ndipo tivale zida za kuwala. 13 Tiyeni tikhale ndi makhalidwe oyenela monga anthu ocita zinthu masana. Tizipewa maphwando oipa,* kumwa mwaucidakwa, ciwelewele, khalidwe lopanda manyazi,* mikangano, komanso nsanje. 14 Koma valani Ambuye Yesu Khristu, ndipo musamakonzekele kucita zimene thupi limalakalaka.