Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka
3 M’caka ca 15 ca ulamulilo wa Kaisara Tiberiyo, Pontiyo Pilato anali bwanamkubwa wa Yudeya. Herode* anali kulamulila cigawo* ca Galileya, Filipo m’bale wake anali kulamulila madela a Itureya ndi Tirakoniti. Ndipo Lusaniyo anali kulamulila cigawo ca Abilene. 2 M’masiku amenewo, Anasi anali wansembe wamkulu, ndipo Kayafa anali mkulu wa ansembe. Pa nthawiyo, Yohane mwana wa Zekariya ali m’cipululu, uthenga wa Mulungu unafika kwa iye.
3 Conco iye anapita m’madela onse ozungulila Yorodani, ndipo anali kulalikila kuti anthu ayenela kubatizika monga cizindikilo ca kulapa kuti macimo awo akhululukidwe. 4 Izi zinacitika malinga ndi zimene zinalembedwa m’buku la mneneli Yesaya kuti: “Winawake akufuula m’cipululu kuti: ‘Konzani njila ya Yehova. Wongolani misewu yake. 5 Cigwa ciliconse cifoceledwe, ndipo phili lililonse komanso citunda ciliconse zisalazidwe. Njila zokhotakhota ziwongoledwe, ndipo njila zokumbikakumbika zisalazidwe. 6 Anthu onse adzaona cipulumutso ca Mulungu.’”*
7 Ndiyeno Yohane anayamba kulankhula ndi gulu la anthu omwe anali kubwela kuti iye awabatize. Anati: “Ana a njoka inu, ndani wakucenjezani kuti muthawe mkwiyo umene ukubwela? 8 Ndiye balani zipatso zoonetsa kulapa. Musadzinamize n’kumati, ‘Tili ndi Abulahamu atate wathu.’ Pakuti ndikukuuzani kuti Mulungu angathe kusandutsa miyala iyi kukhala ana a Abulahamu. 9 Ndithudi, nkhwangwa yaikidwa kale pa mizu ya mitengo. Cotelo mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino udzadulidwa ndi kuponyedwa pa moto.”
10 Ndiyeno khamu la anthulo linamufunsa kuti: “Kodi tiyenela kucita ciyani?” 11 Iye anawayankha kuti: “Amene ali ndi zovala ziwili* apatseko munthu amene alibe, ndipo amene ali ndi cakudya acitenso cimodzimodzi.” 12 Nawonso okhometsa misonkho anabwela kwa iye kuti abatizidwe, ndipo anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, kodi tiyenela kucita ciyani?” 13 Iye anawayankha kuti: “Musamalipilitse anthu* zopitilila pa mtengo wa msonkho.” 14 Nawonso asilikali anali kumufunsa kuti: “Kodi tiyenela kucita ciyani?” Iye anawauza kuti: “Musamavutitse aliyense* kapena kunamizila munthu aliyense mlandu. Koma muzikhutila ndi malipilo anu.”
15 Tsopano anthu anali kuyembekezela Khristu, ndipo onse anali kudzifunsa m’mitima yawo zokhudza Yohane kuti: “Kodi ameneyu angakhale Khristu kapena?” 16 Yohane anawayankha onsewo kuti: “Ine ndikukubatizani ndi madzi. Koma wamphamvu kuposa ine akubwela, ndipo sindine woyenelela kumasula nthambo za nsapato zake. Ameneyo adzakubatizani ndi mzimu woyela komanso moto. 17 Fosholo yake youluzila ili m’manja mwake kuti ayeletse kothelatu malo ake opunthila mbewu. Komanso kuti tiligu amututile m’nkhokwe yake, koma mankhusu* awatenthe pa moto wosazimitsika.”
18 Iye anapelekanso malangizo ena ambili, ndipo anapitiliza kulalikila uthenga wabwino kwa anthu. 19 Yohane anadzudzula Herode wolamulila cigawo, cifukwa ca Herodiya mkazi wa m’bale wake, komanso cifukwa ca zoipa zonse zimene Herode anacita. 20 Koma cifukwa codzudzulidwa, Herodeyo anacitanso coipa cina kuwonjezela pa zonsezi: Anatsekela Yohane m’ndende.
21 Pamene anthu onse anali kubatizidwa, Yesu nayenso anabatizidwa. Ndipo pamene iye anali kupemphela, kumwamba kunatseguka, 22 ndiponso mzimu woyela wooneka ngati nkhunda unatsika n’kudzatela pa iye. Kenako kumwamba kunamveka mawu akuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondeka, ndimakondwela nawe.”
23 Yesu anayamba utumiki wake ali ndi zaka pafupifupi 30. Anthu anali kumudziwa kuti anali mwana,
wa Yosefe,
mwana wa Heli,
24 mwana wa Matati,
mwana wa Levi,
mwana wa Meliki,
mwana wa Yanai,
mwana wa Yosefe,
25 mwana wa Matatiyo,
mwana wa Amosi,
mwana wa Nahumu,
mwana wa Esili,
mwana wa Nagai,
26 mwana wa Maati,
mwana wa Matatiyo,
mwana wa Semeini,
mwana wa Yoseki,
mwana wa Yoda,
27 mwana wa Yoanani,
mwana wa Resa,
mwana wa Zerubabele,
mwana wa Salatiyeli,
mwana wa Neri,
28 mwana wa Meliki,
mwana wa Adi,
mwana wa Kosamu,
mwana wa Elimadama,
mwana wa Ere,
29 mwana wa Yesu,
mwana wa Eliezere,
mwana wa Yorimu,
mwana wa Matati,
mwana wa Levi,
30 mwana wa Sumeyoni,
mwana wa Yudasi,
mwana wa Yosefe,
mwana wa Yonamu,
mwana wa Eliyakimu,
31 mwana wa Meleya,
mwana wa Mena,
mwana wa Matata,
mwana wa Natani,
mwana wa Davide,
32 mwana wa Jese,
mwana wa Obedi,
mwana wa Boazi,
mwana wa Salimoni,
mwana wa Nasoni,
33 mwana wa Aminadabu,
mwana wa Arini,
mwana wa Hezironi,
mwana wa Perezi,
mwana wa Yuda,
34 mwana wa Yakobo,
mwana wa Isaki,
mwana wa Abulahamu,
mwana wa Tera,
mwana wa Nahori,
35 mwana wa Serugi,
mwana wa Reu,
mwana wa Pelegi,
mwana wa Ebere,
mwana wa Shela,
36 mwana wa Kainani,
mwana wa Aripakisadi,
mwana wa Semu,
mwana wa Nowa,
mwana wa Lameki,
37 mwana wa Metusela,
mwana wa Inoki,
mwana wa Yaredi,
mwana wa Mahalaliyeli,
mwana wa Kainani,
38 mwana wa Enosi,
mwana wa Seti,
mwana wa Adamu,
mwana wa Mulungu.