Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka
4 Yesu atadzazidwa ndi mzimu woyela, anacoka ku Yorodani, ndipo mzimuwo unali kumutsogolela m’cipululu 2 kwa masiku 40. Kumeneko Mdyelekezi anamuyesa. Yesu sanadye ciliconse pa masiku amenewo. Conco masikuwo atatha, anamva njala. 3 Mdyelekezi ataona izi anamuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu usanduke mtanda wamkate.” 4 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amati, ‘Munthu sangakhale ndi moyo ndi cakudya cokha ayi.’”
5 Kenako anapita naye pa malo okwela ndi kumuonetsa maufumu onse a padziko lapansi m’kanthawi kocepa. 6 Ndiyeno Mdyelekezi anamuuza kuti: “Ulamulilo wonsewu ndi ulemelelo ndikupatsani cifukwa zinapelekedwa kwa ine, ndipo ndingazipeleke kwa aliyense amene ndafuna. 7 Conco ngati mungagwade pansi ndi kundilambilako kamodzi kokha, zonsezi zikhala zanu.” 8 Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amati, ‘Yehova Mulungu wako ndi amene uyenela kum’lambila, ndipo uyenela kutumikila iye yekha basi.’”
9 Ndiyeno anapita naye ku Yerusalemu n’kumukwezeka pamwamba penipeni pa* kacisi. Kenako anamuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, dziponyeni pansi kucokela pano, 10 cifukwa Malemba amati, ‘Iye adzalamula angelo ake za inu kuti akutetezeni,’ 11 ndipo, ‘Iwo adzakuwakhani ndi manja awo kuti phazi lanu lisagunde mwala.’” 12 Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amati, ‘Usamuyese Yehova Mulungu wako.’” 13 Conco Mdyelekezi atatsiliza mayeselo onsewo anacoka n’kumusiya, ndipo anayembekezela nthawi ina yabwino.
14 Tsopano Yesu atadzazidwa ndi mphamvu ya mzimu anabwelela ku Galileya. Ndipo mbili yake yabwino inafalikila m’madela onse ozungulila. 15 Komanso iye anayamba kuphunzitsa m’masunagoge awo, ndipo anthu onse anali kumulemekeza.
16 Ndiyeno anapita ku Nazareti kumene anakulila. Mwacizolowezi cake, pa tsiku la Sabata analowa m’sunagoge ndi kuimilila kuti awelenge. 17 Conco anamupatsa mpukutu wa mneneli Yesaya. Iye anautambasula ndipo anapeza pamene panalembedwa mawu akuti: 18 “Mzimu wa Yehova uli pa ine cifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa osauka. Anandituma kuti ndilengeze za ufulu kwa anthu ogwidwa ukapolo, komanso kuti akhungu ayambe kuona. Anandituma kudzamasula anthu opondelezedwa, 19 ndi kudzalalikila za caka covomelezeka ca Yehova.” 20 Atatelo, anapinda mpukutuwo n’kuubweza kwa mtumiki wa m’sunagogemo. Kenako anakhala pansi. Maso a anthu onse m’sunagogemo anangoti dwii pa iye. 21 Ndiyeno anayamba kuwauza kuti: “Lelo, lemba limene mwangolimva kumeneli lakwanilitsidwa.”
22 Anthu onsewo anayamba kum’tamanda ndipo anadabwa ndi mawu acisomo otuluka pakamwa pake. Iwo anali kufunsana kuti: “Kodi ameneyu si mwana wa Yosefe?” 23 Iye atamva zimenezi anawauza kuti: “Mosakayikila, mudzakamba mwambi uwu pa ine wakuti ‘Iwe wocilitsa anthu, dzicilitse wekha. Zinthu zimene tinamva kuti unazicita ku Kaperenao, uzicitenso kuno kwanu.’” 24 Conco iye anati: “Ndithu ndikukuuzani, palibe mneneli amene amalandilidwa kwawo. 25 Mwacitsanzo, ndithu ndikukuuzani kuti: Mu Isiraeli munali akazi ambili amasiye m’masiku a Eliya pamene kumwamba kunatsekedwa kwa zaka zitatu ndi miyezi 6, ndipo m’dziko lonselo munagwa njala yaikulu. 26 Koma Eliya sanatumizidwe kwa aliyense wa akaziwo. M’malomwake, anatumizidwa kwa mkazi wamasiye wa ku Zarefati m’dziko la Sidoni. 27 Komanso m’nthawi ya mneneli Elisa, mu Isiraeli munali anthu ambili akhate. Koma palibe ngakhale mmodzi wa iwo amene anacilitsidwa,* kupatulapo Namani wa ku Siriya.” 28 Tsopano onse amene anali kumvetsela zimenezi m’sunagogemo anakwiya kwambili. 29 Iwo ananyamuka ndipo mofulumila anamutulutsila kunja kwa mzinda. Kenako anapita naye pamwamba pa phili pamene panamangidwa mzinda wawo, kuti akamuponye kuphompho. 30 Koma iye anangodutsa pakati pawo n’kumapita.
31 Ndiyeno anapita ku Kaperenao, mzinda wa ku Galileya. Ndipo anali kuphunzitsa anthu pa Sabata. 32 Anthuwo anadabwa kwambili ndi kaphunzitsidwe kake cifukwa anali kukamba mwaulamulilo. 33 Tsopano m’sunagogemo munali munthu wina wogwidwa ndi mzimu, inde ciwanda conyansa. Munthuyo anali kukuwa mwamphamvu kuti: 34 “Aa! Mufuna ciyani kwa ife inu Yesu Mnazareti? Kodi mwabwela kudzatiwononga? Ine ndikudziwa bwino kuti ndinu Woyela wa Mulungu.” 35 Koma Yesu anaudzudzula mzimuwo kuti: “Khala cete, ndipo tuluka mwa iye.” Pamenepo ciwandaco cinamugwetsela pansi munthuyo pakati pawo, basi n’kutuluka mwa iye popanda kumuvulaza. 36 Anthu onsewo ataona izi, anadabwa kwambili, ndipo anayamba kukambilana kuti: “Onani, mawu ake ndi amphamvu kwambili cifukwa mwa ulamulilo ndi mphamvu akulamula mizimu yonyansa kutuluka, ndipo ikutulukadi!” 37 Conco mbili yake inafalikila paliponse m’madela onse ozungulila.
38 Atatuluka m’sunagoge muja, anakalowa m’nyumba ya Simoni. Pa nthawiyo, apongozi aakazi a Simoni anali kudwala malungo aakulu. Conco iwo anamupempha kuti awathandize. 39 Ndiyeno iye anaimilila pafupi ndi mayiwo n’kudzudzula malungowo, ndipo malungowo anathelatu. Nthawi yomweyo mayiwo anaimilila n’kuyamba kuwakonzela cakudya.
40 Koma pamene dzuwa linali kulowa, onse amene anali ndi anthu odwala matenda osiyanasiyana anawabweletsa kwa iye. Ndipo anawacilitsa mwa kuika manja ake pa aliyense wa iwo. 41 Nazonso ziwanda zinatuluka mwa anthu ambili zikufuula kuti: “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.” Koma anali kuzidzudzula ndipo sanali kuzilola kuti zilankhule, cifukwa zinali kumudziwa kuti ndi Khristu.
42 Kutaca m’mawa, iye anacoka n’kupita ku malo opanda anthu. Koma khamu la anthu linayamba kumufunafuna,* mpaka anafika kumene iye anali. Ndipo iwo anamucondelela kuti asawasiye. 43 Koma iye anawauza kuti: “Ndiyenela kukalengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ku mizinda inanso, cifukwa n’zimene ndinatumidwa kudzacita.” 44 Atatelo, anapita kukalalikila m’masunagoge a ku Yudeya.