Kwa Afilipi
2 Conco ngati muzilimbikitsana mwa Khristu, kutonthozana mwacikondi, kucezelana ndi Akhristu anzanu, kukondana kwambili, komanso kucitilana cifundo, 2 ndiye kuti cimwemwe canga cidzasefukila. Muzionetsa kuti mumaganiza mofanana, muli ndi cikondi cofanana, ndinu ogwilizana kwambili, komanso kuti muli ndi maganizo amodzi. 3 Musamacite ciliconse ndi mtima wokonda mikangano kapena cifukwa codzikuza, koma modzicepetsa, muziona ena kuti amakuposani. 4 Musamangofuna zokomela inu mwini, koma zokomelanso ena.
5 Khalani ndi maganizo amenenso Khristu Yesu anali nao. 6 Ngakhale kuti iye anali m’cifanizo ca Mulungu, sanaganizilepo zoti ayese kulanda udindo wa Mulungu kuti akhale wofanana naye. 7 Sanacite zimenezo ai, koma anasiya zonse zimene anali nazo n’kukhala ngati kapolo, ndipo anakhala wofanana ndi anthu ena onse. 8 Kuonjezela pamenepo, atakhala munthu* anadzicepetsa, ndipo anakhala womvela mpaka imfa. Inde, imfa ya pamtengo wozunzikilapo.* 9 Pa cifukwa cimeneci, Mulungu anamukweza n’kumupatsa udindo wapamwamba kwambili, ndipo anamukomela mtima n’kumupatsa dzina loposa dzina lina lililonse. 10 Anacita zimenezi kuti onse agwade,* kaya ali kumwamba, padziko lapansi, kapena pansi pa nthaka.* 11 Komanso kuti aliyense abvomeleze poyela kuti Yesu Khristu ndi Ambuye, zimene zidzapeleka ulemelelo kwa Mulungu Atate.
12 Okondedwa anga, pamene ndinali nanu limodzi, nthawi zonse munali omvela. Simunacite zimenezi panthawi yokhayo pamene ndinali nanu limodzi, koma mukupitilizabe kukhala omvela kwambili ngakhale panopa pomwe sindili nanu limodzi. Conco pitilizani kugwilila nchito cipulumutso canu mwamantha ndi kunjenjemela. 13 Cifukwa Mulungu ndi amene amakulimbitsani. Amakupatsani mtima wofuna kucita zinthu zimene iye amakonda, komanso mphamvu zocitila zinthuzo. Iye amacita zimenezi cifukwa ndi zimene zimamukondweletsa. 14 Mukamacita zinthu muzipewa kung’ung’udza komanso mikangano, 15 kuti mukhale opanda cifukwa cokunenezelani komanso osalakwa. Mukhale ana a Mulungu opanda ulemali pakati pa m’badwo wopotoka maganizo ndi wokhota-khota. Pakati pa m’badwo umenewu, inu mukuwala ngati zounikila m’dzikoli. 16 Pamene mukucita zimenezi, mugwile mwamphamvu mau a moyo. Mukatelo ndidzakhala ndi cifukwa cosangalalila m’tsiku la Khristu, cifukwa ndidzadziwa kuti kuthamanga kwanga komanso khama langa sizinapite pacabe. 17 Komabe, ngakhale kuti ndikuthilidwa ngati nsembe ya cakumwa pa nsembe zimene inu mukupeleka ndi pa utumiki wopatulika umene* mukucita cifukwa ca cikhulupililo canu, ndikusangalala ndipo ndikukondwela nanu limodzi nonsenu. 18 Cotelo, ndikukulimbikitsani kuti inunso musangalale limodzi ndi ine.
19 Koma ine ndikuyembekezela kuti Ambuye Yesu andilola kutumiza Timoteyo kwa inu posacedwapa, kuti ndidzalimbikitsidwe ndikadzamva mmene zinthu zilili kwa inu. 20 Cifukwa ndilibe wina amene ali ndi mtima ngati wake, amene angasamaliledi moona mtima zosowa zanu. 21 Anthu ena onse akungoganizila zofuna zao zokha, osati za Yesu Khristu. 22 Koma inu mukudziwa bwino citsanzo cabwino cimene Timoteyo anaonetsa, kuti monga mwana ndi tate wake, watumikila ngati kapolo limodzi ndi ine polengeza uthenga wabwino. 23 Conco, ndikuyembekezela kumutumiza kwa inu ndikangodziwa mmene zinthu zikhalile kwa ine. 24 Ndithudi, ndikhulupilila kuti Ambuye akalola inenso ndidzabwela kwa inu posacedwa.
25 Koma palipano ndikuona kuti ndi bwino ndikutumizileni Epafurodito. Ameneyu ndi m’bale wanga, wanchito mnzanga ndi msilikali mnzanga. Iye ndi nthumwi yanu komanso amanditumikila pa zosowa zanga. 26 Ndikufuna kumutumiza cifukwa akulakalaka kukuonani inu nonse, ndipo akubvutika maganizo cifukwa munamva kuti anali kudwala. 27 N’zoona kuti iye anadwaladi kwa kaya-kaya. Koma Mulungu anamucitila cifundo. Ndipo cifundo cimeneco sanacitile iye yekha ai, koma anacitilanso ine kuti cisoni cimene ndili naco cisawonjezeke. 28 Conco, ndikumutumiza mwamsanga kwa inu kuti mukamuona mukhalenso acimwemwe komanso kuti nkhawa yanga icepe. 29 Cotelo monga mwa nthawi zonse, mulandileni mwa Ambuye ndi manja awili komanso mwacimwemwe. Ndipo abale ngati amenewa muziwalemekeza kwambili. 30 Iye anatsala pang’ono kufa pamene anali kugwila nchito ya Khristu,* ndipo anaika moyo wake paciswe. Anatelo kuti adzanditumikile m’malo mwa inu, popeza simukanatha kubwela kuno kuti mudzandithandize.