Wolembedwa na Maliko
1 Ciyambi ca uthenga wabwino wonena za Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, 2 monga zinalembedwela m’buku la mneneli Yesaya kuti: “(Taona! Nikutumiza mthenga wanga patsogolo pako,* amene adzakukonzela njila.) 3 Winawake akufuula m’cipululu kuti: ‘Konzani njila ya Yehova! Wongolani misewu yake.’” 4 Yohane M’batizi anali ku cipululu, ndipo anali kulalikila kuti anthu ayenela kubatizika monga cizindikilo ca kulapa kuti macimo awo akhululukidwe. 5 Anthu a mu Yudeya yense na onse a mu Yerusalemu anali kupita kwa iye. Iye anali kuwabatiza* mu Mtsinje wa Yorodani, ndipo iwo anali kuulula macimo awo poyela. 6 Yohane anali kuvala covala ca ubweya wa ngamila na lamba wacikumba m’ciuno mwake. Ndipo anali kudya dzombe na uci. 7 Iye anali kulalikila kuti: “Winawake wamphamvu kuposa ine akubwela m’mbuyo mwanga, ndipo ine sindine woyenela kuŵelama na kumasula nthambo za nsapato zake. 8 Ine nakubatizani na madzi, koma iye adzakubatizani na mzimu woyela.”
9 M’masiku amenewo, Yesu anabwela kucokela ku Nazareti wa ku Galileya, ndipo anabatizidwa na Yohane mu Yorodani. 10 Yesu atangovuuka m’madzimo, anaona kumwamba kukutseguka komanso mzimu ukutsika ngati nkhunda kudzatela pa iye. 11 Ndipo kumwamba kunamveka mawu akuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondeka, nimakondwela nawe.”
12 Nthawi yomweyo mzimuwo unamulimbikitsa kupita ku cipululu. 13 Conco anakhalabe ku cipululuko masiku 40, ndipo anali kuyesedwa na Satana. Kumeneko kunalinso nyama za kuchile, koma angelo anali kumutumikila.
14 Tsopano Yohane atamangidwa, Yesu anapita ku Galileya kukalalikila uthenga wabwino wa Mulungu. 15 Anali kulalikila kuti: “Nthawi yoikidwilatu ija yakwana, ndipo Ufumu wa Mulungu wayandikila. Lapani ndipo khulupililani uthenga wabwino.”
16 Iye akuyenda m’mbali mwa Nyanja ya Galileya, anaona Simoni na m’bale wake Andireya akuponya maukonde awo panyanja popeza anali asodzi. 17 Conco Yesu anawauza kuti: “Nitsatileni, ndipo ine nidzakusandutsani asodzi a anthu.” 18 Nthawi yomweyo iwo anasiya maukonde awo n’kumutsatila. 19 Atapita patsogolo pang’ono, anaona Yakobo mwana wa Zebedayo na m’bale wake Yohane, akusoka maukonde awo m’bwato, 20 ndipo nthawi yomweyo anawaitana. Pamenepo iwo anasiya tate wawo Zebedayo m’bwatomo pamodzi na aganyu n’kumutsatila. 21 Iwo anapita ku Kaperenao.
Tsiku la Sabata litangoyamba, Yesu anapita kukaloŵa m’sunagoge n’kuyamba kuphunzitsa. 22 Ndipo iwo anadabwa kwambili na kaphunzitsidwe kake, cifukwa anali kuwaphunzitsa monga munthu wa ulamulilo, osati monga alembi. 23 Pa nthawiyo, m’sunagogemo munali mwamuna wina wogwidwa na mzimu wonyansa. Mwamunayo anafuula kuti: 24 “Mufuna ciyani kwa ife, inu Yesu Mnazareti? Kodi mwabwela kudzatiwononga? Ine nikudziŵa bwino kuti ndinu Woyela wa Mulungu!” 25 Koma Yesu anadzudzula mzimuwo kuti: “Khala cete, tuluka mwa iye!” 26 Kenako mzimu wonyansawo unacititsa munthuyo kupalapata, ndipo unakuwa mwamphamvu n’kutuluka mwa iye. 27 Anthu onsewo anadabwa kwambili moti anayamba kukambilana, amvekele: “N’ciyani cimeneci? N’ciphunzitso catsopano! Ngakhale mizimu yonyansa akuilamula mwamphamvu, ndipo ikumumvela.” 28 Conco mbili yokamba za iye inawanda mofulumila m’madela onse a cigawo ca Galileya.
29 Kenako, anatuluka m’sunagogemo n’kupita kunyumba kwa Simoni na Andireya, ali pamodzi na Yakobo na Yohane. 30 Pa nthawiyo, apongozi aakazi a Simoni anali gone cifukwa codwala malungo, ndipo mwamsanga iwo anamufotokozela za mayiyo. 31 Yesu anapita pomwe panali mayiyo, ndipo anamugwila dzanja n’kumuutsa. Pamenepo malungowo anathelatu, moti mayiyo anayamba kuwakonzela cakudya.
32 Madzulo dzuŵa litaloŵa, anthu anayamba kumubweletsela odwala onse komanso ogwidwa na ziŵanda. 33 Ndipo anthu onse a mu mzindawo anasonkhana pakhomo la nyumbayo. 34 Zitatelo, iye anacilitsa anthu ambili odwala matenda osiyana-siyana, ndiponso anatulutsa ziŵanda zambili. Koma sanalole kuti ziŵandazo zilankhule, cifukwa zinali kumudziŵa kuti ni Khristu.*
35 M’mamaŵa kukali mdima, iye anauka n’kupita panja kwayekha. Kumeneko anayamba kupemphela. 36 Koma Simoni na amene anali naye anayamba kumufunafuna. 37 Atamupeza anamuuza kuti: “Aliyense akukufunafunani.” 38 Koma iye anawauza kuti: “Tiyeni tipite kwina, ku midzi yapafupi kuti nikalalikilenso kumeneko, cifukwa n’cimene n’nabwelela.” 39 Ndipo anapita kukalalikila m’masunagoge awo m’cigawo conse ca Galileya,·komanso anali kutulutsa ziŵanda.
40 Kumeneko kunabwelanso munthu wina wakhate. Iye anagwada n’kuyamba kumucondelela kuti: “Ngati mufuna munganiyeletse.” 41 Pamenepo Yesu anamva cifundo kwambili, ndipo anatambasula dzanja lake n’kumukhudza. Kenako anati: “Nifuna! Khala woyela.” 42 Nthawi yomweyo khate lake linathelatu moti anakhala woyela. 43 Kenako anamuuza kuti azipita na kumupatsa malangizo amphamvu 44 akuti: “Samala kuti usauzeko aliyense zimenezi. Koma pita ukadzionetse kwa wansembe, ndipo kaamba ka kuyeletsedwa kwako ukapeleke zinthu zimene Mose analamula kuti ukhale umboni kwa iwo.” 45 Koma munthuyo atacoka, anayamba kuilengeza kwambili nkhaniyo na kuifalitsa m’madela ambili. Kaamba ka ici, Yesu sanathenso kuloŵa mu mzinda uliwonse moonekela, koma anali kukhala kunja kumalo opanda anthu. Ngakhale n’telo, anthu anali kubwelabe kwa iye kucokela ku mbali zonse.