Kwa Afilipi
4 Cotelo inu abale anga amene ndimakukondani ndipo ndikulakalaka kukuonani, inu amenenso ndinu cimwemwe canga ndi cisoti canga caulemelelo. Okondedwa anga, ndikukulimbikitsani kuti mupitilize kuima zolimba mwa Ambuye.
2 Ndikudandaulila Eodiya komanso Suntuke kuti akhale ndi maganizo amodzi mwa Ambuye. 3 Ndikupempha iwenso wanchito mnzanga weniweni,* kuti upitilize kuwathandiza azimai amenewa. Iwo ayesetsa mwakhama kugwila nane nchito yolengeza uthenga wabwino. Acita zimenezi limodzinso ndi Kilementi, komanso anchito anzanga ena onse amene maina ao ali m’buku la moyo.
4 Nthawi zonse muzikondwela mwa Ambuye. Ndibwelezanso kunena kuti, Muzikondwela! 5 Anthu onse azidziwa kuti ndinu ololela. Ambuye ali pafupi. 6 Musamade nkhawa ndi cinthu ciliconse. Koma pa ciliconse, mwa pemphelo ndi pembedzelo, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. 7 Mukatelo, mtendele wa Mulungu umene umapambana kumvetsa zinthu kwa mtundu uliwonse, udzateteza mitima yanu komanso maganizo anu mwa Khristu Yesu.
8 Potsiliza abale, pitilizani kuganizila mozama zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambili, zilizonse zolungama, zilizonse zoyela, zilizonse zolimbikitsa cikondi, zilizonse zimene anthu amaziyamikila, khalidwe lililonse labwino, komanso ciliconse cotamandika. 9 Muzicita zimene munaphunzila, zimene munazibvomeleza, zimene munamva kwa ine, komanso zimene munandiona ndikucita. Mukatelo, Mulungu wamtendele adzakhala nanu.
10 Ndikukondwela kwambili mwa Ambuye kuti tsopano mwayambanso kuonetsa kuti mumandiganizila. Ndikudziwa kuti mwakhala mukundiganizila kwa nthawi yonseyi. Koma kungoti mpata ndiwo munalibe kuti muonetse zimenezi. 11 Sikuti ndikulankhula zimenezi cifukwa ndikusowekela zina zake ai, pakuti ndaphunzila kukhala wokhutila mosasamala kanthu mmene zinthu zilili pa umoyo wanga. 12 Ndikudziwa mmene zimakhalila ukakhala wosauka, ndikudziwanso mmene zimakhalila ukakhala wolemela. Pa ciliconse komanso m’mikhalidwe yosiyana-siyana ndaphunzila cinsinsi cokhala wokhuta ndi cokhala wanjala. Ndaphunzilanso cinsinsi cokhala ndi zoculuka komanso cokhala wopanda kalikonse. 13 Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kwa iye amene amandipatsa mphamvu.
14 Komabe munacita bwino kundithandiza m’masautso anga. 15 Ndipo inu Afilipi, mukudziwanso bwino kuti pamene ndinali kucoka ku Makedoniya, mutangomvetsela uthenga wabwino, panalibe mpingo wina umene unandithandiza pa nkhani ya kupatsa ndi kulandila, kupatulapo inu nokha. 16 Cifukwa pamene ndinali ku Tesalonika, inu munanditumizila kenakake kuti kandithandize pa zimene ndinali kusowekela, ndipo simunacite zimenezi kamodzi kokha, koma munatelo kawili konse. 17 Sikuti ndikufuna kuti mundipatse mphatso, koma ndikufuna kuti muzicita zinthu zabwino zimene zingakupindulileni kwambili. 18 Ine ndili ndi zonse zofunikila, ndipo zikuposa pa zimene ndikufunikila. Sindikusowa kanthu cifukwa Epafurodito wandipatsa zinthu zimene mwanditumizila. Zinthu zimenezi zili ngati pfungo lonunkhila bwino, ndiponso ngati nsembe yobvomelezeka ndi yosangalatsa kwa Mulungu. 19 Ndipo Mulungu wanga adzakupatsani zonse zimene mukufunikila malinga ndi kuculuka kwa cuma cake caulemelelo kudzela mwa Khristu Yesu. 20 Tsopano Mulungu amene ndi Atate wathu alandile ulemelelo mpaka muyaya. Ameni.
21 Mundipelekele moni kwa oyela onse amene ali mu mgwilizano ndi Khristu Yesu. Abale amene ali ndi ine akukupatsani moni. 22 Oyela onse akupeleka moni, koma maka-maka a m’nyumba ya Kaisara.
23 Cisomo ca Ambuye Yesu Khristu cikhale nanu, cifukwa ca makhalidwe anu abwino.*