Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Yohane
14 “Mitima yanu isavutike. Khulupililani Mulungu, ndipo khulupililaninso ine. 2 M’nyumba ya Atate wanga muli malo ambili okhalamo. Mukanakhala kuti mulibe, n’kanakuuzani. Conco ndikupita kukakukonzelani malo. 3 Komanso ndikapita kukakukonzelani malo, ndidzabwelanso kudzakutengani n’kupita nanu, kuti kumene ine ndikakhale inunso mukakhale komweko. 4 Ndipo njila ya kumene ine ndikupita, inu muidziwa.”
5 Thomasi anamufunsa kuti: “Ambuye, kumene inu mukupita sitidziwako. Ndiye njilayo tingaidziwe bwanji?”
6 Yesu anamuyankha kuti: “Ine ndine njila, coonadi, ndi moyo. Palibe amene angafike kwa Atate akapanda kudzela mwa ine. 7 Anthu inu mukanandidziwa ine, mukanawadziwanso Atate wanga. Kuyambila tsopano kupita m’tsogolo mwawadziwa, ndipo mwawaona kale.”
8 Filipo anamuuza kuti: “Ambuye, tionetseni Atatewo, ndipo mukatelo tikhutila.”
9 Yesu anamuuza kuti: “Ngakhale kuti anthu inu ndakhala nanu kwa nthawi yaitali yonseyi, Filipo, kodi sunandidziwebe? Amene waona ine waonanso Atate. Nanga n’cifukwa ciyani ukuti ‘Tionetseni Atate’? 10 Kodi sukhulupilila kuti ine ndi Atate ndife ogwilizana? Zimene ndimakuuzani si za m’maganizo mwanga ayi, koma Atate amene akhalabe ogwilizana nane, akucita nchito zawo. 11 Khulupilila kuti ine ndi Atate ndife ogwilizana. Apo ayi, khulupilila cifukwa ca nchitozo. 12 Ndithudi ndikukuuzani, aliyense wondikhulupilila adzacitanso nchito zimene ine ndimacita. Ndipo adzacita nchito zazikulu kuposa zimenezi cifukwa ine ndikupita kwa Atate. 13 Komanso ciliconse cimene mudzapempha m’dzina langa ine ndidzacicita, kuti Atate alemekezedwe kupitila mwa Mwana wake. 14 Mukapempha ciliconse m’dzina langa, ine ndidzacicita.
15 “Ngati mumandikonda, mudzasunga malamulo anga. 16 Ndidzapempha Atate, ndipo iwo adzakupatsani mthandizi* wina amene adzakhala nanu kwamuyaya. 17 Mthandiziyo ndi mzimu wa coonadi, umene dzikoli silingaulandile, cifukwa siliuona kapena kuudziwa. Inu mumaudziwa cifukwa uli mwa inu ndipo umakhala mwa inu. 18 Sindidzakusiyani mukulila,* ndidzabwela kwa inu. 19 Posacedwapa dziko silidzandionanso. Koma inu mudzandiona cifukwa ndili ndi moyo, ndiponso inu mudzakhala ndi moyo. 20 Pa tsiku limenelo mudzadziwa kuti ine ndi Atate ndife ogwilizana, komanso kuti inu ndi ine ndife ogwilizana. 21 Aliyense amene ali ndi malamulo anga ndipo amawatsatila, ndi amene amandikonda. Komanso aliyense amene amandikonda, Atate wanganso adzamukonda. Inenso ndidzamukonda, ndipo ndidzadzionetsa bwinobwino kwa iye.”
22 Yudasi, koma osati Isikariyoti, anamufunsa kuti: “Ambuye, n’cifukwa ciyani mukufuna kudzionetsa bwinobwino kwa ife osati kudzikoli?”
23 Yesu anamuyankha kuti: “Ngati munthu amandikonda adzasunga mawu anga, ndipo Atate wanga adzamukonda, komanso tidzapita kwa iwo n’kuyamba kukhala nawo. 24 Amene sandikonda sasunga mawu anga. Mawu amene mukuwamvawa si anga ayi, koma ndi a Atate amene anandituma.
25 “Ndakuuzani zinthu zimenezi pamene ndikali nanu. 26 Koma mthandiziyo, amene ndi mzimu woyela umene Atate adzatumiza m’dzina langa, ameneyo adzakuphunzitsani zinthu zonse, ndi kukukumbutsani zonse zimene ndinakuuzani. 27 Ndikusiyilani mtendele, ndipo ndikupatsani mtendele wanga. Sindikupatsani mtendelewo mmene dziko limakupatsilani ayi. Mitima yanu isavutike kapena kucita mantha. 28 Mwamva kuti ndakuuzani kuti, ‘Ndikupita ndipo ndidzabwelanso kwa inu.’ Ngati mumandikonda, mukanakondwela kuti ndikupita kwa Atate, cifukwa Atate ndi wamkulu kuposa ine. 29 Conco ndakuuzani tsopano zimenezi zisanacitike, kuti zikadzacitika mukakhulupilile. 30 Sindikamba nanu zambili cifukwa wolamulila wa dzikoli akubwela, ndipo iye alibe mphamvu pa ine. 31 Koma kuti dziko lidziwe kuti ndimawakonda Atate, ndikucita ndendende zimene Atatewo anandilamula. Nyamukani, tiyeni ticokeko kuno.