Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka
10 Pambuyo pa zimenezi, Ambuye anasankha anthu ena 70 n’kuwatumiza awiliawili kuti atsogole kupita ku mizinda ndi ku malo osiyanasiyana kumene iye anali kufunika kupitako. 2 Kenako anawauza kuti: “Zoonadi, zokolola n’zoculuka koma anchito ndi ocepa. Conco pemphani Mwini zokolola kuti atumize anchito okakolola. 3 Pitani! Taonani, ndikukutumizani monga nkhosa pakati pa mimbulu. 4 Musanyamule zikwama za ndalama, kapena cola ca zakudya, kapenanso nsapato. Ndipo musapatse moni* munthu aliyense m’njila. 5 Mukalowa m’nyumba iliyonse, muzinena kuti: ‘Mtendele ukhale panyumba ino.’ 6 Ndipo ngati panyumbapo pali munthu wokonda mtendele, mtendele wanu udzakhala pa iye. Koma ngati palibe, mtendele wanu udzabwelela kwa inu. 7 Muzikhala m’nyumba imeneyo, ndipo muzidya ndi kumwa zimene angakupatseni. Pakuti wanchito ayenela kulandila malipilo ake. Musamacoke kumene mwafikilako n’kupita kunyumba zina.
8 “Ndiponso mukalowa mumzinda, anthuwo n’kukulandilani, muzidya zimene akukonzelani. 9 Komanso muzicilitsa odwala mumzindawo ndi kuwauza kuti: ‘Ufumu wa Mulungu wakuyandikilani.’ 10 Koma mukalowa mumzinda ndipo sanakulandileni, muzipita m’misewu yake n’kunena kuti: 11 ‘Tikukutumula fumbi la mumzinda wanu limene lakhala ku mapazi athu, monga umboni wokutsutsani. Koma dziwani kuti Ufumu wa Mulungu wayandikila.’ 12 Ndikukuuzani kuti cilango ca Sodomu cidzakhala cocepelako poyelekezela ndi ca mzinda umenewo.
13 “Tsoka kwa iwe Korazini! Tsoka kwa iwenso Betsaida! Cifukwa nchito zamphamvu zimene zacitika mwa inu, zikanacitika ku Turo ndi ku Sidoni, anthu kumeneko akanalapa kalekale, ndipo akanavala masaka aciguduli n’kukhala pa phulusa. 14 Conco, cilango ca Turo ndi Sidoni pa Tsiku la Ciweluzo cidzakhala cocepelako poyelekezela ndi canu. 15 Ndipo iwe Kaperenao, kodi mwina udzakwezedwa kumwamba? Ayi udzatsikila ku Manda!*
16 “Amene amakumvelani amamvelanso ine. Ndipo amene amakunyalanyazani amanyalanyazanso ine. Komanso amene amanyalanyaza ine amanyalanyazanso Iye amene anandituma.”
17 Ndiyeno ophunzila 70 aja anabwelela ali ndi cimwemwe, ndipo anati: “Ambuye, ngakhale ziwanda zinali kutigonjela tikagwilitsa nchito dzina lanu.” 18 Iye atamva zimenezi anati: “Ndikuona Satana atagwa kale ngati mphenzi kucokela kumwamba. 19 Taonani! ndakupatsani ulamulilo wopondaponda njoka ndi zinkhanila, komanso ulamulilo wogonjetsa mphamvu zonse za mdani. Ndipo palibe ciliconse cimene cidzakuvulazani. 20 Komabe, musakondwele kuti mizimu yakugonjelani. Koma kondwelani cifukwa cakuti maina anu alembedwa kumwamba.” 21 Pa nthawi imeneyo, iye anakondwela kwambili mwa mzimu woyela, ndipo anati: “Ndikukutamandani inu Atate, Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi, cifukwa zinthu zimenezi mwazibisa mosamala kwa anthu anzelu komanso ophunzila kwambili, koma mwaziulula kwa ana aang’ono. Inde Atate, cifukwa munaona kuti zimenezi ndiye zili bwino. 22 Atate wanga wapeleka zinthu zonse kwa ine, ndipo palibe amene akumudziwa bwino Mwana kupatulapo Atate. Palibenso amene akuwadziwa bwino Atate kupatulapo Mwana, komanso aliyense amene Mwanayo wafuna kumuululila za Atatewo.”
23 Kenako mseli Yesu anauza ophunzila akewo kuti: “Odala ndi anthu amene akuona zinthu zimene inu mukuona. 24 Pakuti ndikukuuzani kuti aneneli ambili komanso mafumu anali kulakalaka kuona zimene inu mukuona, ndi kumva zimene inu mukumva.”
25 Ndiyeno munthu wina wodziwa Cilamulo anaimilila kuti amuyese. Anati: “Mphunzitsi, ndiyenela kucita ciyani kuti ndikalandile moyo wosatha?” 26 Yesu anamufunsa kuti: “Kodi m’Cilamulo munalembedwa ciyani? Umawelengamo zotani?” 27 Munthuyo anayankha kuti: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, mphamvu zako zonse, ndi maganizo ako onse.’ Komanso ‘uzikonda munthu mnzako mmene umadzikondela wekha.’” 28 Yesu anati: “Wayankha molondola, pitiliza kucita zimenezo, ndipo udzapeza moyo.”
29 Koma munthuyo pofuna kudzionetsela kuti ndi wolungama, anafunsanso Yesu kuti: “Kodi munthu mnzanga amene ndiyenela kumukonda ndani makamaka?” 30 Yesu poyankha anati: “Munthu wina anali kucokela ku Yerusalemu kupita ku Yeriko, ndipo anakumana ndi acifwamba amene anamuvula zovala, kumumenya, ndi kumusiya atatsala pang’ono kufa. 31 Tsopano zinangocitika kuti wansembe wina anali kudutsa mu msewuwo. Koma ataona munthuyo, anamulambalala. 32 Ndiyeno Mlevi anafika pa malopo, ndipo nayenso atamuona anamulambalala. 33 Koma Msamariya wina amene anali kuyenda mu msewuwo anafika pamalopo, ndipo atamuona anamva cisoni. 34 Conco iye anafika pamene panali munthuyo n’kuthila mafuta ndi vinyo pa zilonda zake n’kuzimanga. Ndiyeno anamukwezeka pa bulu wake n’kupita naye kunyumba ya alendo kuti akamusamalile. 35 Tsiku lotsatila anatenga madinari awili n’kupatsa wosamalila alendoyo, ndipo anamuuza kuti: ‘Umusamalile, ndipo zilizonse zimene utaye kuwonjezela pa zimenezi, ndidzakubwezela pobwelela.’ 36 Kodi pa atatuwa, ukuona kuti ndani anaonetsa cikondi kwa munthu uja amene anakumana ndi acifwamba?” 37 Munthuyo anati: “Ndi uja amene anamucitila cifundo.” Kenako Yesu anamuuza kuti: “Pita iwenso uzikacita zimenezo.”
38 Tsopano iwo anapitiliza ulendo wawo, ndipo analowa m’mudzi winawake. Kumeneko mayi wina dzina lake Marita anamulandila m’nyumba yake monga mlendo. 39 Mayiyo anali ndi m’bale wake dzina lake Mariya. Mariyayo anakhala pansi ku mapazi a Ambuye n’kumamvetsela zimene anali kukamba.* 40 Koma Marita anatangwanika ndi nchito zambili. Conco iye anafika kwa Yesu n’kunena kuti: “Ambuye, kodi sizikukukhudzani kuti m’bale wangayu wandilekelela kuti ndigwile ndekha nchito? Muuzeni kuti abwele andithandize.” 41 Koma Ambuye anamuyankha kuti: “Marita, Marita, ukuda nkhawa komanso kutangwanika ndi zinthu zambili. 42 Koma zofunikila n’zocepa cabe, mwinanso n’cimodzi cokha. Pakuti Mariya wasankha gawo labwino,* ndipo gawoli silidzalandidwa kwa iye.”