Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Yohane
15 “Ine ndine mtengo wampesa weniweni ndipo Atate ndi mlimi. 2 Iye adzadula nthambi iliyonse mwa ine imene sibala zipatso, ndipo adzayeletsa nthambi iliyonse yobala zipatso mwa kuitengulila* kuti ibale zipatso zoculuka. 3 Inu ndinu oyela kale cifukwa ca mawu amene ndakuuzani. 4 Khalanibe ogwilizana ndi ine, ndipo inenso ndidzakhalabe wogwilizana ndi inu. Nthambi singabale zipatso payokha, ngati siyolumikizika kumtengo wampesa. Mofananamo, inunso simungabale zipatso ngati simukhalabe ogwilizana ndi ine. 5 Ine ndine mtengo wampesa, ndipo inu ndinu nthambi zake. Aliyense wogwilizana ndi ine, inenso ndidzagwilizana naye, ndipo adzabala zipatso zambili cifukwa popanda ine palibe ciliconse cimene mungacite. 6 Ngati munthu sakhalabe wogwilizana ndi ine, ali ngati nthambi yodulidwa imene imauma. Anthu amasonkhanitsa nthambizo n’kuziponya pamoto, ndipo zimapsa. 7 Ngati mukhalabe ogwilizana ndi ine, komanso ngati mawu anga akhalabe mwa inu, mungapemphe ciliconse cimene mufuna ndipo cidzacitika. 8 Atate amalemekezeka ngati mupitiliza kubala zipatso zambili ndi kuonetsa kuti ndinu ophunzila anga. 9 Monga mmene Atate amandikondela, inenso ndimakukondani. Khalanibe m’cikondi canga. 10 Mukamasunga malamulo anga, mudzakhalabe m’cikondi canga, monga mmene inenso ndasungila malamulo a Atate wanga ndi kukhalabe m’cikondi cake.
11 “Ndakuuzani zinthu zimenezi kuti cimwemwe canga cikhale mwa inu, komanso kuti cimwemwe canu cisefukile. 12 Lamulo langa n’lakuti muzikondana wina ndi mnzake mmenenso ine ndimakukondelani. 13 Palibe munthu amene ali ndi cikondi cacikulu kuposa ca munthu amene wapeleka moyo wake cifukwa ca mabwenzi ake. 14 Mukhala mabwenzi anga mukamacita zimene ndimakulamulani. 15 Sindikukuchulaninso kuti akapolo, cifukwa kapolo sadziwa zimene mbuye wake akucita. Koma ndakuchulani kuti mabwenzi, cifukwa ndakuuzani zonse zimene ndinamva kwa Atate wanga. 16 Si ndinu amene munandisankha, koma ine ndinakusankhani. Ndinakusankhani kuti mupitilize kubala zipatso, komanso kuti zipatso zanu zisathe, kuti ciliconse cimene mungapemphe Atate m’dzina langa akupatseni.
17 “Ndikukulamulani zimenezi n’colinga cakuti muzikondana wina ndi mnzake. 18 Ngati dziko limadana nanu, dziwani kuti linadana ndi ine lisanadane ndi inu. 19 Mukanakhala a dzikoli, dzikoli likanakukondani monga akeake. Tsopano simuli a dziko, koma ine ndakusankhani kucokela m’dzikoli, n’cifukwa cake dzikoli limadana nanu. 20 Muzikumbukila mawu amene ndinakuuzani akuti: Kapolo saposa mbuye wake. Ngati iwo azunza ine, inunso adzakuzunzani. Ngati asunga mawu anga, adzasunganso mawu anu. 21 Koma iwo adzakucitilani zinthu zonsezi cifukwa ca dzina langa, popeza samudziwa amene anandituma. 22 Ndikanapanda kubwela n’kulankhula nawo, akanakhala opanda chimo. Koma tsopano alibe cifukwa cokanila chimo lawo. 23 Amene amadana ndi ine, amadananso ndi Atate wanga. 24 Ndikanapanda kucita nchito pakati pawo zimene palibe munthu aliyense akanazicita, iwo akanakhala opanda chimo. Koma tsopano andiona ndipo adana nane, komanso adana ndi Atate wanga. 25 Koma zimenezi zacitika kuti mawu olembedwa m’Cilamulo cawo akwanilitsidwe, akuti: ‘Anadana nane popanda cifukwa.’ 26 Mthandizi amene ndidzakutumizilani kucokela kwa Atate akadzabwela, amene ndi mzimu wa coonadi wocokela kwa Atate, ameneyo adzacitila umboni, 27 ndipo inunso mudzandicitila umboni, cifukwa mwakhala nane kucokela paciyambi.