Kwa Aroma
1 Ine Paulo kapolo wa Khristu Yesu, ndinaitanidwa kuti ndikhale mtumwi komanso ndinasankhidwa kuti ndilengeze uthenga wabwino wa Mulungu. 2 Iye analonjeza uthengawu kalekale kupitila mwa aneneli ake m’Malemba oyela. 3 Uthengawo umakamba za Mwana wake, amene ndi mbadwa* ya Davide, 4 ndipo Mulungu anaukitsa Mwana wake ameneyu mwa kugwilitsa nchito mphamvu ya mzimu wake woyela. Inde, ameneyu ndi Yesu Khristu Ambuye wathu. 5 Kudzela mwa ameneyu, tinalandila cisomo ca Mulungu, ndipo ndinasankhidwa kukhala mtumwi kuti ndikathandize anthu a mitundu yonse kuti aonetse cikhulupililo, akhale omvela, ndiponso kuti alemekeze dzina lake. 6 Inunso munaitanidwa pakati pa anthu a mitundu imeneyo kuti mukhale otsatila a Yesu Khristu. 7 Kalatayi ndalembela inu nonse okhala ku Roma amene mumakondedwa ndi Mulungu komanso munaitanidwa kuti mukhale oyela:
Cisomo ndi mtendele wocokela kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale nanu.
8 Coyamba, ndikuyamika Mulungu wanga kudzela mwa Yesu Khristu cifukwa ca nonsenu, cifukwa anthu padziko lonse akukamba za cikhulupililo canu. 9 Nthawi zonse ndikamapemphela ndimakuchulani m’mapemphelo anga, ndipo Mulungu, amene ndikumucitila utumiki wopatulika ndi mtima wanga wonse polalikila uthenga wabwino wonena za Mwana wake, akundicitila umboni. 10 Ndimapempha Mulungu kuti ngati n’kotheka komanso ngati n’zimene iye akufuna, ndibwele kwanuko tsopano. 11 Cifukwa ndikulakalaka kudzakuonani kuti ndidzakupatseni mphatso inayake yauzimu, kuti mukhale olimba, 12 kapena kuti ndidzalimbikitsidwe ndi cikhulupililo canu, inunso mudzalimbikitsidwe ndi cikhulupililo canga.
13 Koma ndikufuna kuti mudziwe abale, kuti kwa nthawi yaitali ndakhala ndikufuna kubwela kwanuko koma zakhala zikulepheleka mpaka pano. Ndikufuna ndidzaone zotulukapo zabwino za nchito yathu yolalikila ngati mmene zilili pakati pa anthu a mitundu ina yonse. 14 Ine ndili ndi nkhongole kwa Agiriki ndi kwa anthu amene si Agiriki, komanso kwa anthu anzelu ndi kwa anthu opusa. 15 Conco ndikufunitsitsa kudzalengeza uthenga wabwino kwa inunso kumeneko ku Roma. 16 Ine sindikucita nawo manyazi uthenga wabwino. Kukamba zoona, uthengawo ndi njila yamphamvu imene Mulungu akuigwilitsa nchito populumutsa aliyense amene ali ndi cikhulupililo, coyamba Ayuda kenako Agiriki. 17 Mu uthenga umenewu, Mulungu amaulula cilungamo cake kwa anthu amene ali ndi cikhulupililo. Zikatelo, cikhulupililo ca anthuwo cimalimba mogwilizana ndi zimene Malemba amakamba kuti: “Koma wolungama adzakhala ndi moyo cifukwa ca cikhulupililo cake.”
18 Kucokela kumwamba, Mulungu akuonetsa mkwiyo wake kwa anthu onse osamuopa, ndi osalungama amene akucititsa kuti coonadi cisadziwike. 19 Cifukwa Mulungu wawapatsa umboni wokwanila wowathandiza kuti amudziwe. 20 Kucokela pomwe dziko linalengedwa, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekela bwino. Makhalidwe akewo, ngakhalenso mphamvu zake zosatha komanso Umulungu wake, zikuonekela m’zinthu zimene anapanga, moti anthuwo alibenso cifukwa comveka cosakhulupilila kuti Mulungu aliko. 21 Ngakhale kuti iwo anali kumudziwa Mulungu, sanamulemekeze monga Mulungu kapena kumuyamikila. M’malomwake, iwo anayamba kuganiza mopanda nzelu, ndipo mitima yawo yopusa inacita mdima. 22 Ngakhale kuti amakamba kuti ndi anzelu, iwo ndi opusa. 23 M’malo molemekeza Mulungu amene sangafe, iwo amalemekeza zifanizilo za anthu amene amafa, komanso zifanizilo za mbalame, nyama za miyendo inayi ndiponso nyama zokwawa.
24 Conco malinga ndi zilakolako za mitima yawo, Mulungu anawaleka kuti acite zonyansa, kuti acititse manyazi matupi awo. 25 Iwo anasinthanitsa coonadi ca Mulungu ndi bodza, ndipo amalambila ndiponso kucita utumiki wopatulika ku zinthu zolengedwa m’malo mwa Mlengi amene ayenela kutamandidwa mpaka muyaya. Ameni. 26 N’cifukwa cake Mulungu anawaleka kuti atsatile zilakolako zosalamulilika za kugonana, popeza akazi pakati pawo analeka njila yacibadwa yogwilitsila nchito matupi awo n’kumacita zosemphana ndi cibadwa. 27 Amunanso cimodzimodzi, analeka njila yacibadwa yofuna akazi* n’kumatenthetsana okhaokha mwaciwawa ndi cilakolako coipa. Amuna okhaokha kucitilana zonyansa n’kulandililatu mphoto yoyenelela kulakwa kwawo.
28 Popeza iwo sanaone kuti afunika kudziwa Mulungu molondola, iye anawasiya kuti apitilize kuganiza zoipa, n’kumacita zinthu zosayenela. 29 Ndipo anali kucita zosalungama za mtundu ulionse, kuipa konse, dyela,* komanso zinthu zonse zoipa. Mitima yawo inadzaza ndi kaduka, kupha anthu, ndewo, cinyengo ndi njilu. Anali kukonda misece, 30 ndiponso kujeda anzawo, anali kudana ndi Mulungu, anali acipongwe, odzikuza, odzitama, aciwembu, osamvela makolo, 31 osazindikila, osasunga mapangano, opanda cikondi cacibadwa, komanso opanda cifundo. 32 Ngakhale kuti anthu amenewa amalidziwa bwino lamulo lolungama la Mulungu, lakuti amene amacita zinthu zimenezi ndi oyenela imfa, amapitiliza kuzicita. Komanso amagwilizana ndi anthu amene amacita zimenezi.