Kodi Mulungu Wosaonekayo Mungamuone?
“MULUNGU ndiye mzimu,” ndipo anthu sangathe kumuona. (Yohane 4:24) Komabe, Baibulo limakamba kuti anthu ena, mwa njila ina yake, anaona Mulungu. (Aheberi 11:27) Nanga zimenezi zinatheka bwanji? Kodi n’zoonadi kuti Mulungu wosaonekayo mungamuone”?—Akolose 1:15.
Tiyeni tiyelekeze nkhaniyi ndi munthu amene anabadwa wakhungu. Kodi khungu lake limamucititsa kulephela kudziŵa zonse zimene zikucitika pamalo pamene ali? Iyai. Munthu wakhungu amatha kudziŵa zinthu m’njila zosiyanasiyana. Zimenezi zimamucititsa kuzindikila anthu, zinthu ndiponso zinthu zina zimene zikucitika. Munthu wina wosaona anati: “Mphamvu yoona si ili m’maso koma ili m’maganizo.”
Mofananamo, ngakhale kuti Mulungu simungamuone ndi maso anu, mukhoza kumuona pogwilitsila nchito “maso a mtima wanu.” (Aefeso 1:18) Tiyeni tione njila zitatu zimene zingatithandize kucita zimenezi.
‘AKUONEKELA M’ZINTHU ZIMENE ANAPANGA’
Nthawi zambili, munthu wakhungu ali ndi luso lokhoza kumva ndi kukhudza zinthu, limene limamuthandiza kudziŵa zinthu zimene sangaone. Mofananamo, mungathe kuona zinthu za m’dziko ndi kudziŵa Mulungu wosaonekayo amene analenga zinthuzo. “Cilengedwele dziko kupita mtsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekela bwino . . . m’zinthu zimene anapanga.”—Aroma 1:20.
Mwacitsanzo, tiyeni tiganizile kumene tikhala. Dziko linapangidwa mwapadela kwambili cakuti silinapangidwe cabe kuti tizingokhalamo koma kuti tizikondwela ndi umoyo. Timakondwela tikamamva kamphepo kayeziyezi, tikamaothela dzuŵa, tikamadya cipatso cokoma kapena tikamamvetsela kuimba kotsitsimula kwa mbalame. Kunena zoona, mphatso zimenezi zimaonetselatu kuti Mlengi wathu amatiganizila, ndi wacifundo ndiponso woolowa manja.
Kodi cilengedwe cimatiphunzitsa ciani ponena za Mulungu? Cinthu coyamba n’cakuti, zakumwamba zimaonetsa mphamvu za Mulungu. Umboni wa sayansi waposacedwapa waonetsa kuti cilengedwe cikukulilakulilabe ndipo zimenezi zikucitika mofulumila kwambili. Mukamayangana kuthambo usiku, dzifunseni funso ili: Kodi mphamvu imene imacititsa cilengedwe kupitilizabe kukula imacokela kuti makamaka? Baibulo limatiuza kuti Mlengi ali ndi ‘mphamvu zoculuka ndi zoopsa.’ (Yesaya 40:26) Cilengedwe ca Mulungu cimationetsa kuti iye ndi “Wamphamvuyonse”—ndi “wamphamvu zambili.”—Yobu 37:23.
“AMENE ANAFOTOKOZA ZA MULUNGU”
Mai wina amene ali ndi ana aŵili aamuna ndipo ndi akhungu, anati: “Kukamba n’kofunika kwambili kuti aphunzile zinthu. Auzeni ciliconse cimene mukuona ndi kumva, [ndipo] muzikhala wokonzeka kupitiliza kufotokoza ciliconse cimene mukuona. Ndinu maso ao.” Mofananamo, ngakhale kuti “palibe munthu anaonapo Mulungu ndi kale lonse,” Yesu Mwana wa Mulungu, “amene ali pa cifuwa ca Atate ndiye amene anafotokoza za Mulungu.” (Yohane 1:18) Popeza Yesu ndi colengedwa coyamba ca Mulungu ndipo iye ndi Mwana wobadwa yekha, anakhala maso athu oonela kumwamba. Iye angatifotokozele bwinobwino za Mulungu wosaonekayo.
Onani zinthu zocepa zimene Yesu, amene anakhala zaka zambilimbili kumwamba ndi Atate ake anafotokoza ponena za Mulungu:
Mulungu wakhala akugwila nchito mosalema. “Atate wanga akugwilabe nchito mpaka pano.”—Yohane 5:17.
Mulungu amadziŵa zosoŵa zathu. “Atate wanu amadziŵa zimene mukufuna musanapemphe n’komwe.”—Mateyu 6:8.
Mulungu amatisamalila mokoma mtima. “Atate wanu wa kumwamba . . . amawalitsila dzuŵa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsila mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.”—Mateyu 5:45.
Mulungu amationa kuti ndife ofunika aliyense payekha. “Kodi mpheta ziŵili si paja amazigulitsa kakhobidi kamodzi kocepa mphamvu? Komatu palibe ngakhale imodzi imene idzagwa pansi Atate wanu osadziŵa. Ndipotu tsitsi lenilenilo la m’mutu mwanu amaliŵelenga. Conco musacite mantha: Ndinu ofunika kwambili kuposa mpheta zoculuka.”—Mateyu 10:29-31.
MUNTHU AMENE ANAONETSA MAKHALIDWE A MULUNGU
Nthawi zambili, anthu akhungu amamvetsa zinthu m’njila zosiyana ndi anthu amene amaona. Munthu wosaona akhoza kudziŵa mthunzi osati monga malo amene palibe dzuŵa koma monga malo amene pamveka kuzizila akacoka pa dzuŵa. Monga mmene munthu wakhungu sangaonele mthunzi kapena dzuŵa, ndi cimodzimodzinso ndi ife, Yehova sitingamumvetse patokha. Conco, anatumiza munthu amene anaonetsa bwino makhalidwe ndi umunthu wa Yehova.
Munthuyo anali Yesu. (Afilipi 2:7) Yesu sanangokamba za Atate wake koma anationetsanso mmene Atatewo alili. Filipo wophunzila wa Yesu anati: “Ambuye, tionetseni Atatewo.” Poyankha Yesu anati: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yohane 14:8, 9) Kodi kupitila mwa Yesu mungaone ciani za Atate?
Yesu anali wokoma mtima, wodzicepetsa ndi wocezeka. (Mateyu 11:28-30) Anthu ambili anabwela kwa iye cifukwa anali munthu wotsitsimula. Yesu anali kumva cisoni cimene anthu ena anali naco ndipo anali kukondwela ndi anthu amene anali kukondwela. (Luka 10:17, 21; Yohane 11:32-35) Mukamaŵelenga ndi kumvetsela nkhani za m’Baibulo zokhudzaYesu, muziikako nzelu kwambili ndi kuona m’maganizo mwanu monga ngati zinthuzo zikucitika inu mukuona. Ngati musinkhasinkha mmene Yesu anali kucitila zinthu ndi anthu mudzatha kuona bwinobwino makhalidwe osangalatsa a Mulungu ndipo mudzamuyandikila.
KUMVETSETSA MULUNGU
Ponena za mmene munthu wakhungu amadziŵila dziko, mai wina analemba kuti: “Munthu wakhungu amaphunzila zinthu m’njila zosiyanasiyana monga (kugwila, kununkhiza, kumva ndi zina zotelo), ndiyeno amafunika kuika pamodzi zinthu zimene adziŵa kuti apange cimodzi.” Mofananamo, mukamaona zinthu zimene Mulungu analenga, mukamaŵelenga zinthu zimene Yesu ananena zokhudza atate wake, ndi kuganizila mmene Yesu anaonetsela makhalidwe a Atate wake, mudzakhala ndi cithunzi cabwino ca mmene Yehova alili. Iye adzakhala weniweni kwa inu.
Yobu wa m’nthawi yakale anali ndi cocitika cofanana. Poyamba iye anakamba ‘mosazindikila.’ (Yobu 42:3) Koma pambuyo poganizila cilengedwe codabwitsa ca Mulungu, Yobu ananena kuti: “Ndinali kungomva za inu, koma tsopano diso langa lakuonani.”—Yobu 42:5.
‘Ngati mudzam’funafuna Yehova iye adzalola kuti mum’peze’
Zimenezi zingakhalenso zoona ndi inu. “Ukam’funafuna [Yehova] adzalola kuti um’peze.” (1 Mbiri 28:9) Mboni za Yehova zidzakhala zokondwela kukuthandizani kufunafuna Mulungu wosaonekayo ndi kum’peza.